bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 5
1 Samuel 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 6 →
1
Afilisti atalanda Bokosi lachipangano lija, adalinyamula kuchoka nalo ku Ebenezeri nakafika nalo ku Asidodi.
2
Tsono adatenga Bokosilo nakaliika m'nyumba ya Dagoni, mulungu wao, pambali pa Dagoniyo.
3
M'maŵa mwake anthu a ku Asidodi atadzuka m'mamaŵa, adangoona Dagoni atagwa chafufumimba patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Apo anthuwo adatenga fanolo, naliikanso pamalo pake.
4
Koma m'maŵa mwakenso atadzuka, adangoonanso Dagoni uja atagwa, ali chafufumimba, patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Mutu wa Dagoni ndi manja ake omwe zinali zitaduka ndi kugwera pa chiwundo. Thunthu lake lokha la Dagoniyo ndilo limene lidamutsalira.
5
Chimenechi ndicho chifukwa chake chimene ansembe a Dagoni ndi anthu onse amene amaloŵa m'nyumba ya Dagoni, sapondera pa chiwundo cha nyumbayo ku Asidodi, mpaka pano.
6
Kenaka Chauta adalanga koopsa anthu a ku Asidodi. Iwowo pamodzi ndi anthu a m'dziko lozungulira adaŵalanga ndi mafundo.
7
Anthuwo ataona m'mene zinthu zinaliri, adati, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele lisakhale ndi ife, pakuti Mulungu wao watilanga kwambiri ifeyo ndi mulungu wathu yemwe Dagoni.”
8
Choncho adaitana akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, nafunsana kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipangano la Chauta wa Aisraele?” Anthuwo adayankha kuti, “Bokosi limeneli litumizidwe ku Gati.” Motero adatumiza Bokosi lachipanganolo kumeneko.
9
Koma atafika nalo ku Gati, Chauta adauvuta mzindawo, ndipo anthu adachita mantha kwambiri. Choncho anthu amumzindamo adazunzika kwabasi, ana ndi akulu omwe, kotero kuti mafundo ankaŵatuluka anthu onsewo.
10
Tsono adatumiza Bokosi lachipanganolo ku Ekeroni. Koma litangofika ku Ekeroniko, anthu akumeneko adalira kuti, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele, abwera nalo kwathu kuno, kuti atiphetse ife pamodzi ndi anthu athu.”
11
Nchifukwa chake adaitananso akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, ndipo adati, “Chotsani Bokosili, ndipo mulibwezere kumene lidachokera, kuti lingatiphe ife pamodzi ndi anthu athu.” Pakuti munali mantha aakulu zedi mumzinda monsemo. Mulungu ankaŵalanga koopsa anthu akumeneko.
12
Anthu amene sadafe, adavutika ndi mafundo, ndipo kulira kwa anthu amumzindamo kudamveka mpaka kumwamba.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31