bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 3
1 Samuel 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 4 →
1
Mnyamata uja Samuele ankatumikira Chauta, ndipo Eli ankamuyang'anira. Masiku amenewo mau a Chauta sankamveka kaŵirikaŵiri, ndipo kuwona zinthu m'masomphenya sikunkachitikanso kaŵirikaŵiri.
2
Tsiku lina Eli anali gone kumalo kwake. Maso ake adaali atayamba kupenya mwachimbuuzi, kotero kuti sankatha kupenya bwino.
3
Samuelenso anali gone m'Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthaŵiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime.
4
Tsono Chauta adaitana kuti, “Samuele, Samuele!” Iye adayankha kuti, “Ŵaŵa!”
5
Adathamangira kwa Eli nati, “Ndabwera, ndamva kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane, kagone.” Motero Samuele adapita kukagona.
6
Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane mwana wanga, kagone.”
7
Pamenepo nkuti Samuele asanadziŵe Chauta, ndipo mau a Chauta nkuti asanaululidwe kwa iyeyo.
8
Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nakanena kuti, “Ndabwera, mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo.
9
Tsono adauza Samuele kuti, “Pita, kagone. Akakuitananso, ukanene kuti, ‘Lankhulani, Inu Chauta, poti mtumiki wanune ndilikumva.’ ” Choncho Samuele adapita kukagona kumalo kwake.
10
Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthaŵi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “Lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.”
11
Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Tamvera, patsala pang'ono kuti ndichite chinthu mu Israele chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzachimva.
12
Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndidalankhula za Eli ndi banja lake, kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza.
13
Ndikumdziŵitsa Eliyo kuti ndili pafupi kulanga banja lake mpaka muyaya, chifukwa cha zoipa zimene ana ake ankandichita. Eli ankazidziŵa zimenezo, koma osaŵaletsa.
14
Nchifukwa chake ndikulumbira kuti mlandu wa banja la Eli sudzatha konse mpaka muyaya, ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.”
15
Samuele adagona mpaka m'maŵa. Atadzuka adatsekula zitseko za nyumba ya Chauta. Ankachita mantha kumuuza Eli zimene Chauta adaamuululirazo.
16
Koma Eli adamuitana nati, “Samuele mwana wanga.” Samuele adati, “Ŵaŵa!”
17
Apo Eli adafunsa kuti, “Kodi nchiyani chimene Mulungu wakuuza? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu, ukandibisira kanthu kalikonse pa zonse zimene wakuuza.”
18
Choncho Samuele adamuuza zonse osambisira kanthu kalikonse. Ndipo Eli adati, “Ameneyo ndi Chauta. Nachite zimene zikumkomera.”
19
Monse Samuele ankakula, Chauta anali naye, motero zonse zimene Samueleyo ankanena zinkachitikadi.
20
Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adadziŵa kuti Chauta adamsankha Samuele kuti akhale mneneri.
21
Chauta ankadziwululabe ku Silo. Kumeneko ankamveketsa mau ake kwa Samuele polankhula naye. Ndipo mau ake a Samuele ankafika kwa Aisraele onse.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31