bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 17
1 Samuel 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 18 →
1
Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Soko, m'dziko la Yuda. Adamanga zithando zao pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.
2
Saulo adasonkhanitsa Aisraele, namanga zithando zao zankhondo m'chigwa cha Ela, nandanditsa gulu lankhondo kuti amenyane ndi Afilistiwo.
3
Afilisti ndi Aisraele adaika ankhondo ao moyang'anana, ena mbali ina paphiri, ena mbali ina paphirinso, pakatipa chigwa.
4
Tsono ku zithando za Afilisti kudatuluka munthu wina wamphamvu wa ku Gati, dzina lake Goliyati. Msinkhu wake unali pafupi mamita atatu.
5
Ankavala chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo, amene kulemera kwake kunali ngati makilogramu 57.
6
Ankavalanso zokuta miyendo yake zamkuŵa, ndipo ankanyamula nthungo yamkuŵa pa phewa.
7
Thunthu la mkondo wake linali ngati mtanda wa choombera nsalu. Mutu wa nkhondowo unkalemera ngati makilogramu asanu ndi aŵiri. Patsogolo pake pankapita munthu womunyamulira chishango.
8
Goliyatiyo adaimirira ndi kufuula kwa ankhondo a Aisraele kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita kukonzekera nkhondo chotere? Ineyo ndine Mfilisti, inuyo ndinu akapolo a Saulo. Bwanji osati mungosankhula munthu pakati panupo, adze kwa ine.
9
Ngati angathe kulimbana nane ndi kundipha, ndiye kuti Afilisti tonse tidzakhala akapolo anu. Koma ndikampambana ndi kumupha, inuyo mudzakhala akapolo athu ndi kumatigwirira ntchito.
10
Tiwonane lero lino basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.”
11
Atamva mau a Mfilistiyo, Saulo ndi Aisraele onse adachita mantha nathyoka m'nkhongono.
12
Davide anali mwana wa Mwefurati wa ku Betelehemu dzina lake Yese, amene anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Pa nthaŵi ya ufumu wa Saulo, Yese anali atakalamba kale kwambiri.
13
Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama.
14
Davide anali mzime. Ana akuluakulu atatuwo ndiwo anali ku nkhondo ndi Saulo.
15
Koma Davide ankapita ku zithando za Saulo, namabwerako nthaŵi zina kukaŵeta nkhosa za bambo wake ku Betelehemu.
16
Pa masiku makumi anai Goliyati uja adakhala akutuluka, namadziwonetsa m'maŵa ndi madzulo.
17
Tsiku lina Yese adauza mwana wake Davide kuti, “Abale ako uŵatengere makilogramu khumi a tirigu wokazinga, ndi mitanda khumi yabulediyi, ndipo upite nazo mofulumira ku zithando zao.
18
Utengenso mphumphu khumizi za tchizi, upite nazo kwa mkulu wolamulira ankhondo. Ukaone m'mene abale ako akukhalira, ndipo ubwereko ndi chizindikiro china chosonyeza kuti ali bwino.
19
Saulo, abale akowo ndi Aisraele ena, akumenyana nkhondo ndi Afilisti ku chigwa cha Ela.”
20
Tsono Davide adanyamuka m'mamaŵa, nasiyira nkhosa munthu wina wozisunga. Adatenga zakudyazo napita, monga momwe bambo wake adaamlamulira. Adafika ku zithando pamene ankhondo ankandanda pa mzere wankhondo, nkufuula mfuu wankhondo.
21
Aisraele ndi Afilisti adaandanda pa mzere wankhondo moyang'anana.
22
Tsono zakudya zija Davide atasiyira munthu wosunga katundu, adathamangira kumene kunali ankhondo, nakalonjera abale ake.
23
Pamene ankalankhula ndi abale akewo, adangoona Goliyati uja akutuluka ku magulu ankhondo a Afilisti, akulankhula zonyoza zomwe zija. Davide nkumva zimenezo.
24
Aisraele onse atamuwona munthuyo, adathaŵa chifukwa ankamuwopa kwambiri.
25
Ankati, “Muwonenitu munthu uja! Amangobwera, amangodzatinyoza Aisraelefe. Tsono amene amuphe, mfumu idati idzampatsa chuma chambiri, adzampatsanso mwana wake wamkazi kuti amkwatire. Banja la bambo wake silidzalipiranso msonkho.”
26
Tsono Davide adafunsa anthu amene anali pafupi naye kuti, “Adzamtani munthu amene adzaphe Mfilistiyu ndi kuŵachotsa manyazi Aisraele? Mfilisti wosaumbalidwayu ndaninso kuti angamanyoze ankhondo a Mulungu wamoyo?”
27
Anthu adamuuzanso zomwe zija zimene mfumu idaati idzachitire munthu wodzapha Goliyatiyo.
28
Eliyabu, mkulu wake, atamva Davideyo akulankhula ndi anthu, adamupsera mtima, namufunsa kuti, “Wadzachita chiyani kuno? Nanga nkhosa zija wasiyira yani ku chipululu? Ndikudziŵa kuti ndiwe wodzikuza ndi woipa mtima. Wadza kuno kudzangoona nkhondo chabe!”
29
Davide adati, “Kodi ndachimwa chiyani? Ndiye kuti ndileke nkulankhula komwe?”
30
Tsono adachoka apo napita kwa wina namufunsa zokhazokhazo. Aliyense adamuyankhanso monga poyamba paja.
31
Mau amene ankalankhula Davide aja atamveka, anthu adakafotokozera Saulo, ndipo Sauloyo adamuitanitsa.
32
Tsono Davide adauza Saulo kuti, “Munthu aliyense asataye mtima chifukwa cha Mfilistiyu. Ineyo mnyamata wanune ndipita kukamenyana naye.”
33
Saulo adamuuza kuti, “Sungathe kukamenyana naye Mfilistiyu, pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iyeyu ndi munthu wozoloŵera kumenya nkhondo kuyambira ubwana wake.”
34
Apo Davide adauza Saulo kuti, “Mnyamata wanune ndinkaŵeta nkhosa za bambo wanga. Ndipo mkango ukafika, kapena chimbalangondo, ndi kugwira mwanawankhosa pakati pa nkhosazo,
35
ndinkalondola mpaka kuchipha chilombocho ndi kupulumutsa mwanawankhosayo kukamwa kwake. Ndipo chikati chindiwukire, ndinkachigwira tchoŵa lake ndi kuchikantha mpaka kuchipha.
36
Ineineyo ndidaphapo mikango ndi zimbalangondo zomwe. Tsono Mfilisti wosaumbalidwayu, ndidzamupha monga momwe ndidaphera zilombo zija, popeza kuti akunyoza magulu ankhondo a Mulungu wamoyo.
37
Chauta amene adandipulumutsa ku mkango ndi ku chimbalangondo, adzandipulumutsa kwa Mfilistiyu.” Apo Saulo adauza Davide kuti, “Pita, Chauta akhale nawe.”
38
Tsono Saulo adaveka Davide zovala zake zankhondo. Adamveka chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo.
39
Kenaka Davide adamanga lupanga m'chiwuno mwake. Atayesera kuyenda, adaona kuti akulephera poti sadazoloŵere. Ndiye adauza Saulo kuti, “Sindingathe kuyenda nazo, poti sindidazoloŵere.” Choncho adavula zovalazo.
40
Tsono adatenga ndodo yake m'manja. Adatola miyala isanu yosalala yakumtsinje, naiika m'thumba lake lakubusa. Ali ndi khwenengwe m'manja, adapita kukakumana ndi Mfilisti uja.
41
Tsono Mfilistiyo adayambapo kupita kumene kunali Davide, munthu wonyamula chishango ali patsogolo pake.
42
Ndipo atayang'ana Davideyo, adayamba kumnyoza, poona kuti anali mnyamata chabe, wofiirira ndiponso wa maonekedwe okongola.
43
Tsono adafunsa Davide kuti, “Kodi ndine galu, kuti uzibwera kwa ine ndi ndodo?” Pompo adayamba kutemberera Davide potchula milungu yake.
44
Kenaka adauza Davide kuti, “Idza kuno, mnofu wako ndidyetsera mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo.”
45
Koma Davide adauza Mfilistiyo kuti, “Wadza kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo. Koma ine ndikudza kwa iwe m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa magulu ankhondo a Aisraele, amene iwe wamunyoza.
46
Lero lomwe lino Chauta akupereka m'manja mwanga. Ndikulasa ndi kukugwetsa pansi, ndipo ndikudula mutu. Mitembo ya magulu ankhondo a Afilisti ndiipereka lero lino kwa mbalame zamumlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo, kuti dziko lonse lapansi lidziŵe kuti kuli Mulungu ku dziko la Israele.
47
Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.”
48
Tsono Mfilistiyo adasendera pafupi kuti akumane ndi Davide. Pomwepo Davideyo adathamanga mofulumira ku mzere wankhondo uja, kuti nayenso akakumane naye.
49
Adapisa dzanja m'thumba natulutsamo mwala, ndipo adauponya namlasa pa mphumi Mfilistiyo. Mwalawo udamuloŵa m'mutu, ndipo Mfilistiyo adagwa pansi chafufumimba.
50
Choncho Davide adampambana Goliyati uja pomlasa ndi mwala wam'khwenengwe, namupha Mfilistiyo. M'manja mwa Davide munalibe konse lupanga.
51
Pompo adathamanga, nakaimirira pamwamba pa Mfilisti uja. Adasolola lupanga lake lomwe m'chimake, namtsiriza pomdula mutu. Tsono Afilisti ataona kuti ngwazi yao yamphamvu pa nkhondo yafa, adathaŵa.
52
Aisraele ndi anthu a ku dziko la Yuda adanyamuka akufuula, napirikitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekeroni. Tsono Afilisti ovulala ankagwa pa njira yonse kuyambira ku Saraimu mpaka ku Gati ndi Ekeroni.
53
Ndipo Aisraele adabwererako kumene ankapirikitsa Afilisti kuja, nadzafunkha m'zithando zankhondo za Afilistiwo.
54
Kenaka Davide adatenga mutu wa Mfilisti uja napita nawo ku Yerusalemu. Koma zida zokha za Mfilistiyo adaziika m'hema mwake.
55
Pamene Saulo adaaona Davide akupita kukamenyana ndi Mfilisti uja, adafunsa Abinere mkulu wa ankhondo kuti, “Kodi iwe Abinere, mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abinere adayankha kuti, “Pepani inu amfumu muli apa, ine sindingadziŵe.”
56
Apo mfumu idati, “Kafunse kuti kodi mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani?”
57
Tsono pamene Davide ankabwererako kumene adaakapha Mfilisti kuja, Abinere adamtenga napita naye kwa Saulo, mutu wa Mfilisti uja uli m'manja mwake.
58
Saulo adafunsa Davide kuti, “Kodi mnyamata iwe, paja ndiwe mwana wa yani?” Davide adayankha kuti, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese, wa ku Betelehemu.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31