bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 28
1 Samuel 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 29 →
1
Nthaŵi ina Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo, kuti amenyane ndi Aisraele. Tsono Akisi adauza Davide kuti, “Udziŵe kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita nane ku nkhondo.”
2
Davide adayankha kuti, “Chabwino, mudzaona zimene ndichite ine mtumiki wanu.” Akisi adati, “Chabwino, ndidzakuika kuti ukhale mlonda wonditchinjiriza pa moyo wako wonse.”
3
Nthaŵi imeneyi nkuti Samuele atafa, ndipo Aisraele atalira maliro ake, namuika ku mzinda wake ku Rama. Saulo anali atachotsa anthu onse olankhula ndi mizimu ndi anthu onse oombeza maula am'dzikomo.
4
Tsono Afilisti adasonkhana nadzamanga zithando zao zankhondo ku Sunemu. Saulo nayenso adasonkhanitsa Aisraele, ndipo adamanga zithando ku Gilibowa.
5
Saulo ataona gulu laankhondo la Afilisti, adayamba kuwopa ndi kunjenjemera kwambiri.
6
Adapempha nzeru kwa Chauta, koma sadamuyankhe ngakhale podzera m'maloto, kapena mwa Urimu kapena mwa aneneri.
7
Pamenepo Saulo adauza nduna zake kuti, “Mundifunire mkazi wolankhula ndi mizimu kuti ndipite kwa iyeyo, ndikapemphe nzeru.” Ndunazo zidamuuza kuti, “Ku Endori aliko mkazi wolankhula ndi mizimu.”
8
Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.”
9
Mkaziyo adati, “Inutu mukudziŵa zimene adachita mfumu Saulo. Suja adachotsa m'dziko muno anthu olankhula ndi mizimu ndiponso oombeza? Chifukwa chiyani tsono mukunditchera msampha kuti mundiphe?”
10
Koma Saulo adalonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Chauta wamoyo, sudzalangidwa kaamba ka zimenezi.”
11
Apo mkaziyo adafunsa kuti, “Kodi ndikuitanireni yani?” Saulo adati, “Itanire Samuele.”
12
Pamene mkaziyo adaona Samuele, adakuwa kwambiri nati, “Chifukwa chiyani mwandinyenga? Ndinu mfumu Saulo!”
13
Tsono mfumuyo idamuuza kuti, “Usaope. Kodi ukuwona chiyani?” Mkaziyo adati, “Ndikuwona mzimu ukutuluka pansi.”
14
Saulo adafunsa mkaziyo kuti, “Kodi maonekedwe a mzimuwo ngotani?” Mkaziyo adati, “Imene ikutuluka ndi nkhalamba, yavala mkanjo.” Apo Saulo adadziŵa kuti ndi Samuele ameneyo, ndipo adapereka ulemu pakuŵerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi.
15
Pamenepo Samuele adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani wandivuta ponditulutsa kuti ndibwere kuno?” Saulo adayankha kuti, “Ndavutika kwambiri, pakuti Afilisti abwera kudzandithira nkhondo, ndipo Mulungu wandifulatira osandiyankhanso, ngakhale podzera mwa aneneri, kapena m'maloto. Nchifukwa chake ndakuitanani kuti mundiwuze zomwe ndiyenera kuchita.”
16
Samuele adati, “Chifukwa chiyani ukufuna ine tsopano, chikhalirecho Chauta wakufulatira kale ndipo wasanduka mdani wako?
17
Chauta wakuchita zomwe adakuuza kudzera mwa ine. Wakulanda ufumu, waupereka kwa wina, kwa Davide.
18
Chauta akuchita zimenezi lero, chifukwa chakuti sudamvere mau ake, ndipo sudaonongeretu Aamaleke ndi zinthu zao.
19
Tsono adzakupereka iweyo pamodzi ndi Aisraele kwa Afilisti. Ndipo maŵa, iwe ndi ana ako, mudzabwera kuli ine kuno. Ndithudi, Chauta adzapereka gulu lankhondo la Aisraele kwa Afilisti.”
20
Pompo Saulo adagwa pansi, kuchita kuti nyutu, ali wodzazidwa ndi mantha chifukwa cha mau a Samuele. Ndipo analibenso nyonga, poti sadadye kanthu tsiku lonse.
21
Apo mkazi uja adasendera pafupi ndi Saulo, ndipo ataona kuti akuchita mantha, adamuuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ine ndataya moyo wanga pomvera zimene munandiwuza.
22
Nchifukwa chake tsono, inunso mumvere mau anga. Mundilole ndikuikireni kabuledi pang'ono, mudye kuti muwone nyonga zoyendera.”
23
Saulo adakana nati, “Ine sindidya ai.” Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo adamkakamiza, ndipo adaŵamvera. Choncho adadzuka pansi paja nakhala pa bedi.
24
Mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa, ndipo adamupha mwachangu. Adatenga ufa naukanyanga, naphika buledi wosatupitsidwa.
25
Tsono adadzapereka bulediyo kwa Saulo ndi nduna zake, ndipo onse adadya. Pambuyo pake adanyamuka, nachokapo usiku womwewo.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31