bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 22
1 Samuel 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 23 →
1
Pamenepo Davide adathaŵa ku Gati, nakabisala ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi onse a m'banja la bambo wake atamva, adapita kumene kunali Davide.
2
Tsono aliyense amene anali pa mavuto, kapena anali ndi ngongole, kapena anali wosakondwa, onsewo adasonkhana kwa Davide. Iyeyo ankaŵatsogolera. Onse anali ngati anthu 400 pamodzi.
3
Pambuyo pake Davide adachoka kumeneko, napita ku Mizipa ku Mowabu. Adapempha mfumu ya ku Mowabu kuti, “Chonde, bwanji bambo wanga ndi mai wanga akhale nao kuno, mpaka nditadziŵa zimene Mulungu adzandichitire.”
4
Choncho adaŵasiya kumeneko makolo akewo kwa mfumu ya ku Mowabuko, ndipo iwo adakhala komweko nthaŵi yonse imene Davide ankabisala kuphanga kuja.
5
Tsono mneneri Gadi adauza Davide kuti, “Musakhale pano. Muchoke, mupite ku dziko la Yuda.” Pomwepo Davide adachoka, nakaloŵa m'nkhalango ya Hereti.
6
Tsono Saulo adamva kuti Davide ndi anthu ake adapezeka. Tsiku limenelo Sauloyo adaakhala pansi patsinde pa mtengo wa mbwemba womera pa chitunda china ku Gibea, mkondo uli m'manja, ankhondo ake atamzungulira.
7
Ndiye Sauloyo adafunsa ankhondo ake aja kuti, “Imvani tsono inu Abenjamini. Kodi mwana wa Yese adzakupatsani minda aliyense mwa inu? Kodi adzakusandutsani atsogoleri a magulu ankhondo nonsenu?
8
Mwina nchifukwa chaketu mukundichita chiwembu chotere. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adandiwululira pamene mwana wanga ankagwirizana ndi mwana wa Yese. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akulabadako za ine kapena kundinong'onezako kuti mwana wanga wautsa mtima wa munthu wanga Davide kuti andiwukire, monga akuchitira leromu.”
9
Apo Doegi Mwedomu, amene adaaimirira pafupi ndi nduna za Saulo, adanena kuti, “Ine ndidamuwona mwana wa Yese akupita ku Nobu kwa Ahimeleki, mwana wa Ahitubi.
10
Ndipo Ahimelekiyo adafunsa Chauta zimene Davide ankayenera kuchita. Kenaka adampatsa chakudya, nampatsanso lupanga la Goliyati, Mfilisti uja.”
11
Tsono mfumu Saulo adaitanitsa wansembe Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, pamodzi ndi onse a m'banja la bambo wake, amene anali ansembe ku Nobu. Onsewo adabwera kwa mfumu.
12
Ndipo Saulo adati, “Imva tsono, iwe mwana wa Ahitubi.” Iye adayankha kuti, “Inde, mbuyanga.”
13
Saulo adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wandichita chiwembu iwe ndi mwana wa Yese? Wampatsa buledi ndi lupanga, ndipo wamfunsira kwa Mulungu zoti achite. Taonani, tsopano wandiwukira, ndipo akundilalira lero lino!”
14
Koma Ahimeleki adayankha mofunsa kuti, “Amfumu, kodi ndani pakati pa ankhondo anu amene ali wokhulupirika ngati Davide? Iye uja ndi mkamwini wanu, mtsogoleri wa gulu lanu lokutchinjirizani, ndiponso munthu wolemekezeka m'banja mwanu?
15
Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu zoti achite? Iyai, amfumu! Musandinenere kanthu kena kalikonse koipa, ine mtumiki wanu, kapenanso wina aliyense wa m'banja la bambo wanga, pakuti sindikudziŵa kanthu pa nkhaniyi mpang'ono pomwe.”
16
Komabe mfumu idati, “Iwe Ahimeleki, ndi onse a m'banja la bambo wako, mufa ndithu nonse!”
17
Tsono idauza alonda omwe anali naye kuti, “Apheni ansembe a Chautaŵa, chifukwa akugwirizana ndi Davide. Adaadziŵa kuti Davideyo adathaŵa, koma sadandiwululire zimenezo.” Koma anyamata a mfumuwo sadasamule manja kuti aphe ansembe a Chauta.
18
Pomwepo mfumu idauza Doegi kuti, “Kaŵaphe ndiwe.” Doegi, Mwedomu uja, adapitadi kukapha ansembewo. Adapha anthu 85 ololedwa kuvala efodi ya thonje lokoma.
19
Kunena za Nobu, mzinda wa ansembe uja, Saulo adalamula kuti anthu onse okhalamo aphedwe. Choncho amuna ndi akazi, ana ndi makanda, kudzanso ng'ombe, abulu ndi nkhosa, zonsezo adazipha ankhondo ake.
20
Koma mmodzi mwa ana aamuna a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake Abiyatara, adapulumuka, nathaŵa kutsatira Davide.
21
Ndipo adauza Davide kuti Saulo adapha ansembe a Chauta.
22
Davide adauza Abiyatara kuti “Ha! Tsiku limene lija nditaona kuti Doegi Mwedomu ali konkuja, ndidaadziŵa kuti kosapeneka konse akauza Saulo. Nchifukwa chake tsono uli pa ine mlandu wa imfa ya onse a m'banja la bambo wako.
23
Koma iwe khala ndi ine, usaope ai, pakuti amene akufuna moyo wako, akufunanso moyo wanga. Ukakhala ndi ine, ukhala pabwino.”
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31