bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 29
1 Samuel 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 30 →
1
Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Afeki. Nawonso Aisraele adamanga zithando zankhondo pa chitsime cha ku Yezireele.
2
Pamene atsogoleri ankhondo a Afilisti ankatsogoza magulu ao a ankhondo mazana angapo ndiponso zikwi zingapo, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo ndi Akisi.
3
Pamenepo atsogoleri aja a Afilisti adafunsa kuti, “Kodi Ahebriŵa akuchita chiyani kuno?” Akisi adayankha kuti, “Uyutu ndi Davide, mtumiki wa Saulo mfumu ya Aisraele. Iye wakhala nane tsopano masiku ambiri kapena nditi zaka, chibwerere chake kuno sindidampeze cholakwa chilichonse mpaka lero lino.”
4
Koma iwo adamkalipira Akisiyo namuuza kuti, “Mumbweze munthuyo kuti abwerere ku malo amene mudampatsa. Sadzapita nafe ku nkhondo, kuwopa kuti kunkhondoko angakasanduke mdani wathu. Nanga munthu ameneyu angathe kudziyanjanitsa bwanji ndi mbuyake? Iyeyu angathe kuchita zimenezi pakupha anthu athu ali panoŵa.
5
Ameneyutu ndi Davide, yemwe uja ankamuvinira ndi kumuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi?’ ”
6
Apo Akisi adaitana Davide namuuza kuti, “Pali Chauta wamoyo, iwe wakhala wokhulupirika kwa ine, ndipo kutumikira kwako m'magulu anga ankhondo kwandikomera kwambiri. Sindidakupeze cholakwa kuyambira tsiku limene udabwera kuno mpaka lero lino. Komabe atsogoleri enaŵa sakukufuna.
7
Choncho ubwerere tsopano. Upite mwamtendere, kuwopa kuti atsogoleri a Afilisti angaipidwe nawe.”
8
Davide adamufunsa kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza chiyani pa ine mtumiki wanu, kuyambira nthaŵi imene ndidayamba kukugwirirani ntchito mpaka tsopano lino? Nanga ndilekerenji kukamenyana nkhondo ndi adani anu, mbuyanga mfumu?”
9
Akisi adayankha kuti, “Ndikudziŵa kuti ndiwe wosalakwa ndithu, monga mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri ankhondo a Afilisti akunena kuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’
10
Tsono udzuke m'mamaŵa, pamodzi ndi anthu ako amene udabwera nawo, munyamuke kukangocha.”
11
Choncho Davide ndi anthu omwe anali naye adanyamuka m'mamaŵa nabwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilisti adakafika mpaka ku Yezireele.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31