bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Samuel 24
1 Samuel 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 25 →
1
Saulo atabwerako kumene ankamenyana ndi Afilisti kuja, adamva kuti Davide ali ku chipululu cha Engedi.
2
Tsono adatenga ankhondo okhoza zedi 3,000 amene adaŵasankha pakati pa ankhondo onse. Adapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale.
3
Adafika ku makola a nkhosa a pamphepete pa njira, pamene panali phanga. Saulo adaloŵa m'phangamo kuti akadzithandize. Pamenepo nkuti Davide ndi anthu ake akubisala m'kati mwenimweni mwa phangalo.
4
Apo anthu a Davide aja adamuuza kuti, “Tsiku lija ndi lero limene Chauta ankanena, muja adaakuuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wako m'manja mwako, udzamchita zomwe zidzakukomere.’ ” Tsono Davide adanyamuka, nakadulako chidutswa ku mkanjo wa Saulo, iyeyo osadziŵako ai.
5
Koma pambuyo pake Davideyo adavutika mumtima mwake, chifukwa chakuti anali atadula chidutswa chija ku mkanjo wa Saulo.
6
Tsono adauza anthu ake kuti, “Chauta andiletse kumchita choipa mbuyanga, wodzodzedwa wa Chauta. Ndisampweteke, popeza kuti ngwodzozedwa wa Chauta.”
7
Choncho Davide atalankhula mau ameneŵa, anthu ake adamvera, pakuti sadaŵalole kuti amthire nkhondo Saulo. Pamenepo Saulo adatuluka m'phanga muja namapita.
8
Pambuyo pake Davide nayenso adatuluka m'phangamo, ndipo adaitana Saulo kuti, “Mbuyanga mfumu.” Saulo atacheuka, Davide adamgwadira pogunditsa nkhope yake pansi.
9
Adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani mumamvera mau a anthu amene amanena kuti, ‘Davide akufuna kukuphani?’
10
Lero mwaonatu ndi maso anu kuti Chauta anakuperekani m'manja mwanga m'phanga muja. Ena ankandikakamiza kuti ndikupheni, koma ndakulekani dala. Ndinati, ‘Sindipweteka mbuyanga, poti ngwodzozedwa wa Chauta.’
11
Atate anga, onanitu chidutswa cha mkanjo wanu chili m'manja mwangachi. Pamenepo mudziŵe kuti mumtima mwanga mulibe cholakwa kapena zokuukirani, poti ndadula chidutswa ku mkanjo wanu, koma osakuphani. Sindidakulakwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.
12
Chauta aonetse kuti wolakwa ndani pakati pa ine ndi inu. Akulangeni chifukwa cha zimene mukundichitazi. Koma ine sindikupwetekani, ai.
13
Paja anthu akale adati, ‘Munthu woipa, ntchito zake nzoipa.’ Motero ine sindikupwetekani, ai.
14
Kodi mfumu ya Israele yadzalondola yani? Kodi ikufuna kugwira yani? Zedi, mukulondola ine galu wakufa! Mufuna kupha ine nthata!
15
Nchifukwa chake Chauta aweruze, ndipo agamule pakati pa ine ndi inu kupeza wolakwa. Anditeteze. Aonetse kulungama kwanga pondipulumutsa kwa inu.”
16
Davide atamaliza kulankhula mau ameneŵa, Saulo adafunsa kuti, “Kani liwu limeneli ndi lakodi, mwana wanga Davide?” Apo Saulo adayamba kulira mokweza.
17
Adauza Davide kuti, “Iwe wachita chilungamo kupambana ine, pakuti wandichitira ine zabwino pamene ine ndakuchita zoipa.
18
Lero waonetsa ubwino wako pakuti sudandiphe, Chauta atandipereka kwa iwe.
19
Kodi munthu atapeza mdani wake, angalole kuti mdaniyo apulumuke? Motero Chauta akuchitire zabwino, chifukwa cha zimene wandichitira lerozi.
20
Ona tsono, ndikudziŵa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndipo kuti ufumu wa Israele udzakhazikika pa iwe.
21
Undilonjeze molumbira tsono m'dzina la Chauta kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira, kuti dzina langa ndi la abambo anga lisaiŵalike.”
22
Davide adalumbira zonsezi Saulo alikumva. Tsono Saulo adabwerera kwao, koma Davide ndi anthu ake adapitanso kuphanga kobisalira kuja.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31