bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 1
Leviticus 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 2 →
1
Pamene Chauta anali m'chihema chamsonkhano adaitana Mose, namuuza kuti,
2
“Uza Aisraele kuti, ‘Munthu aliyense akamabwera ndi chopereka kwa Chauta, azitenga ng'ombe kapena nkhosa kapena mbuzi.’
3
“Ngati munthu apereka nsembe yopsereza kwathunthu, azipereka ng'ombe yamphongo yopanda chilema. Aziiperekera pa khomo la chihema chamsonkhano, kuti Chauta ailandire.
4
Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake.
5
Pambuyo pake aiphe pamaso pa Chauta, ndipo ansembe, ana a Aroni, abwere ndi magazi ake. Awaze magaziwo mozungulira guwa limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
6
Ndipo asende nyamayo ndi kuidula nthulinthuli.
7
Tsono ansembe, ana a Aroni aja, asonkhe moto pa guwa, ndipo ayalike nkhuni pamotopo.
8
Pamenepo ansembe aike nthuli za nyamayo, mutu wake pamodzi ndi mafuta omwe, pa nkhuni zimene zili pa guwalo.
9
Koma atsuke matumbo ake pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Tsono wansembe aipsereze nyama yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
10
“Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya nkhosa kapena mbuzi, ikhale yaimuna yopanda chilema.
11
Ndipo aiphere cha kumpoto kwa guwa, pamaso pa Chauta. Tsono ansembe, ana a Aroni, awaze magazi ake pa guwalo molizungulira.
12
Pambuyo pake ataidula nthulinthuli nyamayo, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo aike zonsezo pa nkhuni zimene zili pa guwa.
13
Koma matumbo ake aŵatsukire padera, pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Ndipo wansembe apereke zonsezo ndi kuzitentha pa guwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
14
Ngati munthu apereka kwa Chauta nsembe yopsereza ya mbalame, ikhale njiŵa kapena nkhunda.
15
Wansembe abwere nayo ku guwa, aidule mutu moipotola, ndi kutentha mutuwo paguwapo. Magazi ake aŵathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa.
16
Tsono achotse chitsokomero pamodzi ndi nthenga zake zomwe, ndi kuzitaya potayira phulusa, pafupi ndi guwa, cha kuvuma kwake.
17
Pambuyo pake aing'ambe pakati, phiko lina uku, lina uku, koma osachotsa mapikowo. Kenaka aitenthe pa moto wankhuni wapaguwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27