bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 19
Leviticus 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 20 →
1
Chauta adauzanso Mose kuti,
2
“Uza mpingo wonse wa Aisraele kuti, ‘Mukhale oyera pakuti Ine Chauta, Mulungu wanu, ndine woyera.
3
Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
4
Musabwerere ku mafano, kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’
5
“Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, Mulungu wanu, muchite mwa njira yoti mulandiridwe.
6
Muidye tsiku lomwe mwaiperekalo, kapena m'maŵa mwake, koma zotsalako mpaka pa tsiku lachitatu muzitenthe.
7
Mukaidya pa tsiku lachitatu, kuteroko nkuchita chinthu chonyansa, ndipo nsembeyo sidzalandiridwa.
8
Munthu aliyense amene aidye, adzasenza tchimo lake chifukwa chakuti waipitsa chinthu choyera cha Chauta. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.
9
“Pamene mukolola m'minda mwanu, musakolole munda wanu mpaka m'malire mwenimweni, ndipo musatolenso khunkha lake.
10
Musakolole mphesa zonse m'munda wanu wamphesa, ndipo musatolenso mphesa zakugwa m'munda mwanumo. Zimenezo musiyire anthu osauka ndiponso alendo, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
11
“Musabe, musachite zinthu zonyenga, ndipo musaname.
12
Musalumbire m'dzina langa monyenga ndi kumaipitsa dzina la Ine Mulungu wanu pakutero. Ine ndine Chauta.
13
“Musachenjeretse mnzanu kapena kumubera zinthu zake. Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka m'maŵa.
14
Musatemberere gonthi, kapena kumuikira chokhumudwitsa munthu wakhungu. Koma muziwopa Mulungu wanu, Ine ndine Chauta.
15
“Musamaweruza mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa anthu osoŵa ndi anthu otchuka, koma muziweruza mnzanu mwachilungamo.
16
Musamangoyendayenda uku ndi uku kumachita ukazitape pakati pa anthu a mtundu wanu. Musachite kanthu kalikonse kamene kangathe kudzetsa imfa ya munthu wina. Ine ndine Chauta.
17
“Musadane ndi mbale wanu mumtima mwanu, koma mumdzudzule mosabisa kuti mungavomerezane naye pa tchimo lake.
18
Musabwezere choipa, ndipo musakwiyire anthu a mtundu wanu, koma mukonde mnzanu monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Ine ndine Chauta.
19
“Muzitsata malamulo anga. Musalole kuti ng'ombe zanu zikwerane ndi zoŵeta za mtundu wina. Musafese mbeu za mitundu iŵiri m'munda mwanu, ndipo musavale chovala chopangidwa ndi nsalu za mitundu iŵiri.
20
“Munthu akagona ndi mkazi amene ali mdzakazi wofunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma wosaomboledwa kapenanso asanalandire ufulu wake, aimbidwe mlandu. Onsewo asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake.
21
Koma mwamunayo abwere ndi nsembe yopepesera kupalamula kwake pamaso pa Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Nsembe yopepesera kupalamulayo ikhale nkhosa yamphongo.
22
Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a munthuyo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopepesera kupalamulayo pamaso pa Chauta, chifukwa cha tchimo limene munthuyo adachita, ndipo tchimo adachitalo lidzakhululukidwa.
23
“Pamene muloŵa m'dzikomo ndi kubzala mitengo yamitundumitundu ya zipatso, zipatsozo zikhale zoletsedwa. Zikhale zoletsedwa kwa inu zaka zitatu, musadye pa nthaŵi imeneyo.
24
Pa chaka chachinai, zipatso zonse zidzakhala zopatulikira Chauta ngati nsembe yomtamandira.
25
Koma pa chaka chachisanu mudzatha kudya zipatso zake, kuti choncho mitengoyo idzakubalireni kwambiri. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
26
“Musadye nyama yamagazi. Musamaombeza kapena kuchita zaufiti.
27
Musamamete mduliro kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu.
28
Musadzichekecheke pa thupi lanu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini za mtundu uliwonse. Ine ndine Chauta.
29
“Musaipitse mwana wanu wamkazi pakumsandutsa mkazi wachiwerewere kuti dziko lingasanduke la anthu adama ndi loipa kwambiri.
30
Muzisunga masiku anga a Sabata ndi kulemekeza malo anga oyera, Ine ndine Chauta.
31
“Musamapita kwa anthu olankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa anyanga. Musaŵafunefune kuti angakuipitseni. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
32
“Muzikhala mwaulemu pamaso pa munthu waimvi. Wokalamba muzimchitira ulemu, ndipo pakutero mudzaopa Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.
33
“Pamene mlendo akhala nanu m'dziko mwanu, musamchite choipa.
34
Mlendo amene akhala nanu, akhale ngati mbadwa pakati panu, ndipo mumkonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Pajatu inunso mudaali alendo m'dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
35
“Musamaweruza milandu molakwa, ndipo muyeso wanu woyesera utali wa zinthu, kulemera kwa zinthu kapena kuchuluka kwa zinthu, usamakhala wonyenga.
36
Miyeso yanu ya sikelo, miyeso yoyesera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi hini izikhala yolungama. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito.
37
Muzimvera malamulo anga onse, muzichita monga momwe ndidakulamulirani, malamulowo muziŵatsata. Ine ndine Chauta.”
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27