bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 6
Leviticus 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 7 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwira Chauta chifukwa cha kunyenga mnzake pomakana kumubwezera mnzakeyo zimene adamsungiza, kapena kumubera, kapena kumnyenga,
3
kapena kunama kuti sadatole zimene zidatayika, kapena kumalumbira zonama pa kanthu kalikonse,
4
munthu akachimwa pa zimenezi ndi wopalamula ndithu, abweze zimene adalandazo, zimene adatenga monyengazo, zomsungizazo, ndi zotayika zimene adatolazo.
5
Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, abweze zonsezo ndi kuwonjezapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, tsono amubwezere mwini wakeyo.
6
Ndipo nsembe yopepesera kupalamula, yopereka kwa Chauta, abwere nayo kwa wansembe. Ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, mtengo wake wa nkhosayo ukhale wokwanira mtengo woikidwa wa nyama ya nsembe yopepesera kupalamula.
7
Tsono wansembe achite mwambo wopepesera machimo a munthuyo pamaso pa Chauta, ndipo zonse zimene wochimwayo adachita napalamula pakutero, zidzakhululukidwa.”
8
Chauta adauza Mose kuti,
9
“Ulamule Aroni pamodzi ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza kwathunthu ndi ili: nsembeyo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka m'maŵa, ndipo moto wapaguwapowo uzikhala uli chiyakire.
10
Tsono wansembe avale mkanjo wake wabafuta, avalenso kabudula wabafuta, ndipo atengeko phulusa la nyama yopsereza pa guwa ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo.
11
Tsono avule zovala zake, avale zina, ndipo aole phulusalo nkukaliika pa malo oyeretsedwa kunja kwa mahema.
12
Moto wapaguwa uzikhala uli chiyakire, usazime. Wansembe azisonkhezera motowo ndi nkhuni m'maŵa mulimonse, ndipo aziyala nsembe yopsereza paguwapo, ndi kupserezapo mafuta a nsembe zachiyanjano.
13
Moto ukhale uli chiyakire paguwapo, usazime.’ ”
14
“Lamulo la chopereka cha chakudya ndi ili: ana a Aroni aipereke nsembeyo pamaso pa Chauta patsogolo pa guwa.
15
Tsono mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala woperekedwa ku nsembeyo, pamodzi ndi mafuta ndi lubani yense amene ali pa chopereka cha chakudyacho. Azitenthe pa guwa, kuti zikhale chikumbutso, ndipo zitulutse fungo lokomera Chauta.
16
Tsono Aroni ndi ana ake adye zimene zatsalapo. Zikhale zosafufumitsa, ndipo azidyere pa malo oyera, ndiye kuti pa bwalo la chihema chamsonkhano.
17
Poziphika asathiremo chofufumitsira. Ndaŵapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lao la nsembe zanga zopsereza. Zonsezo nzoyera kwambiri monga nsembe yopepesera machimo, ndiponso nsembe yopepesera kupalamula.
18
Ana onse aamuna a Aroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, monga kudalembedwa kuti zidzatero nthaŵi zonse pa mibadwo yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.”
19
Chauta adauza Mose kuti,
20
“Nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Chauta pa tsiku limene wansembe adzozedwa, izikhala yotere: apereke ufa wosalala wokwanira kilogaramu limodzi ngati chopereka cha chakudya cha nthaŵi zonse. Apereke theka limodzi m'maŵa, ndipo linalo apereke madzulo.
21
Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya. Ubwere nacho ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi chopereka cha chakudya. Ndipo aipereke kuti itulutse fungo lokomera Chauta.
22
Tsono wansembe wa fuko la Aroni amene wadzozedwa kuti aloŵe m'malo mwake, aipereke kwa Chauta nthaŵi zonse monga kudalembedwera. Aipsereze nsembe yonse poti lamulo ndi lamuyaya.
23
Chopereka cha chakudya chilichonse cha wansembe chikhale chopsereza kwathunthu, asachidye ai.”
24
Chauta adauza Mose kuti,
25
“Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopepesera machimo ndi ili: pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, aphereponso nsembe yopepesera machimo kwa Chauta. Imeneyo ndi nsembe yoyera kopambana.
26
Wansembe amene aiperekere machimoyo, adye nyamayo. Aidyere pa malo oyera, pa bwalo la chihema chamsonkhano.
27
Aliyense wokhudza nsembeyo adzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake. Tsono magazi ake akagwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo oyera.
28
Ndipo auphwanye mphika wadothi umene adaphikamo nyamayo. Koma akaphika wamkuŵa, autsuke mphikawo ndi kuutsukuluza ndi madzi.
29
Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana.
30
Koma asadye nyama ya nsembe yopepesera machimo imene magazi ake amabwera nawo ku chihema chamsonkhano, kudzapepesera machimo ku malo oyera. Aitenthe pa moto imeneyo.’
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27