bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 7
Leviticus 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 8 →
1
“Nsembe yopepesera kupalamula njoyera kopambana. Lamulo lake ndi ili:
2
pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, azipheraponso nsembe yopepesera kupalamula, ndipo awaze magazi ake pa guwa mozungulira.
3
Tsono apereke mafuta ake onse, mchira wamafuta ndi mafuta okuta matumbo.
4
Aperekenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi ochotsa ndi imso zija.
5
Wansembe azitenthere pa guwa zonsezo, kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula.
6
Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Aidyere pa malo oyera. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana.
7
Nsembe yopepesera kupalamula njofanafana ndi nsembe yopepesera machimo, ndipo nsembe ziŵiri zonsezo zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe wochita mwambo wopepesera machimo ndiye amene nyamayo ikhale yake.
8
Ndipo wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake.
9
Tsono chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni, kapena cha zonse zimene amakazinga mu mphika kapena m'chiwaya, zikhale za wansembe amene apereke zimenezo.
10
Ndipo chopereka chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chouma, chikhale cha ana onse a Aroni. Anawo aigaŵane molingana.
11
“Lamulo la nsembe yachiyanjano imene aliyense angathe kupereka kwa Chauta ndi ili:
12
akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta.
13
Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo, abwere ndi mitanda ya buledi wotupitsa.
14
Kenaka atengeko mtanda umodzi pa mtundu uliwonse wa buledi, kuti ukhale nsembe yopereka kwa Chauta. Mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe zachiyanjano.
15
Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozerayo aidye pa tsiku lopereka nsembe yakeyo. Asaisungeko mpang'ono pomwe kufikira m'maŵa mwake.
16
Koma nsembe yake ikakhala yoti waipereka moilumbirira kapena mwaufulu, aidye pa tsiku lomwe akuiperekalo, ndipo nyama yotsala aidye m'maŵa mwake.
17
Koma nyama yotsalako kufikira tsiku lachitatu, aitenthe pa moto.
18
Ngati munthu adya nyama ya nsembe yachiyanjano pa tsiku lachitatu, amene waiperekayo Mulungu sadzamulandira, ndipo nsembeyo sidzampindulira kanthu. Idzakhala chinthu chonyansa ndipo amene adzadye imeneyo adzakhala wopalamula.
19
“Nyama imene ikhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, munthu asaidye, koma itenthedwe pa moto. Onse amene ali osaipitsidwa pa zachipembedzo angathe kudya nyama ya nsembe.
20
Koma munthu woipitsidwa akadya nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.
21
Ndipo wina aliyense akakhudza chinthu chonyansa pa zachipembedzo, kaya nchonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, tsono nadyako nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, munthuyo achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.”
22
Chauta adauza Mose kuti,
23
“Uza Aisraele kuti asadye mafuta ang'ombe, kapena ankhosa kapenanso ambuzi.
24
Mafuta a nyama yofa yokha, ndi mafuta a nyama yojiwa ndi zilombo, angathe kuŵagwiritsa ntchito zina zilizonse, koma iwowo asadye.
25
Pakuti munthu amene adya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Chauta kuti ikhale nsembe yotentha pamoto, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.
26
Ndiponso kulikonse kumene akakhale, asadye magazi aliwonse, ambalame kapena anyama.
27
Munthu aliyense wophwanya lamulo limeneli, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.”
28
Chauta adauza Mose kuti,
29
“Uza Aisraele kuti, ‘Munthu amene apereka nsembe yake yachiyanjano kwa Chauta, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Chauta. Pa nsembe yake yachiyanjanoyo
30
atengeko ndi manja ake zigawo zoyenera kuzitentha, zopereka kwa Chauta, ndiye kuti mafuta ndi nganga yomwe. Tsono ngangayo aiweyule kuti ikhale chopereka choweyula kwa ine.
31
Apo wansembe atenthe mafuta pa guwa, koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake.
32
Wansembe mumpatsenso ntchafu ya ku dzanja lamanja, kuti ikhale chopereka cha pa nsembe yanu yachiyanjano.
33
Pakati pa ana a Aroni, wansembe amene apereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, ndiye adzalandire ntchafu ya ku dzanja lamanja ngati chigawo chake.
34
Choncho nganga yopereka moweyula manjayo, pamodzi ndi ntchafu yoperekayo, ndikuzichotsa zonsezo kwa Aisraele. Ndikuzichotsa pa nsembe zao zachiyanjano, ndipo ndikuzipereka kwa wansembeyo Aroni ndi kwa ana ake, kuti zikhale chigawo chao nthaŵi zonse.
35
Chimenecho ndicho chigawo cha Aroni ndi cha ana ake, chotapa pa zopereka kwa Chauta zoyenera kutentha pa moto, chimene chidapatulidwa kuti chikhale chigawo chao, pa tsiku limene iwo adaperekedwa kuti akhale ansembe otumikira Chauta.
36
Chauta ndiye amene adalamula Aisraele kuti azipereka zimenezi kwa ansembe, pa tsiku limene adadzozedwa. Zimenezo ndizo chigawo chao nthaŵi zonse pa mibadwo yao yonse.’ ”
37
Ameneŵa ndiwo malamulo a nsembe zonsezi: yopsereza, ya chakudya, yopepesera machimo, yopepesera kupalamula, yakudzoza, ndiponso yachiyanjano.
38
Malamulo ameneŵa ndi amene Chauta adapereka kwa Mose pa phiri lija la Sinai, pa tsiku limene adalamula Aisraele kuti abwere ndi nsembe zao kwa Chauta, ku chipululu cha Sinai chija.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27