bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 2
Leviticus 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 3 →
1
“Munthu wina aliyense akabwera kudzapereka chopereka cha chakudya kwa Chauta, nsembeyo ikhale ya ufa wosalala. Ufawo authire mafuta ndi lubani,
2
ndipo abwere nawo kwa ansembe, ana a Aroni. Atapeko ufa wosakaniza ndi mafuta uja dzanja limodzi, ndi lubani wake yense. Tsono wansembe atenthe zimenezo pa guwa, kusonyeza kuti nsembeyo yaperekedwa kwa Chauta, ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
3
Zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni pamodzi ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
4
“Ukamapereka chopereka cha chakudya chophika mu uvuni, chikhale buledi wa ufa wa tirigu wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta, kapena ikhale timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta.
5
Nsembe yako ikakhala chakudya chophika pa chitsulo chamoto, chikhale buledi wa ufa wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta.
6
Umuduledule ndi kumupaka mafuta. Chimenecho ndicho chopereka cha chakudya.
7
Ndipo nsembe yako ikakhala ya chopereka cha chakudya chophika pa chiwaya, chikhale ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta.
8
Tsono ubwere nacho chopereka chimenechi kwa Chauta, ndipo utachipereka kwa wansembe, iyeyo abwere nacho ku guwa.
9
Apo wansembeyo atengeko gawo lina la choperekacho kusonyeza kuti chaperekedwa kwa Chauta, tsono achitenthe paguwapo. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
10
Ndipo zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
11
“Chopereka cha chakudya chimene upereka kwa Chauta chikhale chopanda chofufumitsira, pakuti suyenera kupereka kwa Chauta nsembe yotentha pa moto, imene ili ndi chofufumitsira kapena uchi.
12
Ziŵirizo ungathe kubwera nazo ngati nsembe ya zokolola zoyambirira zopereka kwa Chauta. Koma usazitenthere pa guwa kuti zipereke fungo lonunkhira.
13
Zopereka zako zonse za zakudya uzithire mchere, osaiŵala ai: mcherewo ndi wosonyeza chipangano cha pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Uzithira mchere nsembe zako zonse.
14
“Ukamapereka kwa Chauta chopereka cha chakudya choyamba kucha, nsembeyo ikhale ya mbeu zatsopano zokazinga ndi zopunthapuntha.
15
Ndipo uchithithire mafuta ndi lubani. Chimenecho ndicho chopereka cha chakudya.
16
Tsono wansembe atenthe chigawo cha mbeu zopunthapuntha zija ndi cha mafuta, ndiponso lubani wake yense, kuti ikhale nsembe yachikumbutso. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27