bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 26
Leviticus 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 27 →
1
“Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
2
Muzisunga masiku anga a Sabata ndi kulemekeza malo anga oyera. Ine ndine Chauta.
3
“Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi,
4
ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso.
5
Mudzakhala mukupuntha dzinthu mpaka nthaŵi yothyola zipatso, ndipo mudzakhala mukuthyola zipatso mpaka nthaŵi yobzala. Mudzadya chakudya mpaka kukhuta, ndi kumakhala m'dziko mwanu popanda chokuvutani.
6
Ndidzabweretsa mtendere m'dziko mwanu, ndipo muzidzagona pansi popanda wokuwopsani. Ndidzapirikitsa zilombo zoopsa m'dziko mwanu, ndipo m'dziko mwanu simudzakhala nkhondo.
7
Mudzapirikitsanso adani anu, ndipo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga.
8
Anthu asanu okha mwa inu adzapirikitsa anthu zana ndipo anthu zana mwa inu adzapirikitsa anthu zikwi khumi, ndipo adani anuwo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga
9
Ndidzakukumbukirani, ndipo ndidzakubalitsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzalimbitsa chipangano changa ndi inu.
10
Muzidzadyabe sundwe wakalekale, koma mudzachotsa sundweyo m'khokwe, kuti zatsopano zipeze malo.
11
Ndidzakhala pakati panu ndipo sindidzaipidwa nanu.
12
Ndidzayenda pakati panu. Ine ndidzakhala Mulungu wanu, inu mudzakhala anthu anga.
13
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo a Aejipito. Ndadula goli lanu kuti muziyenda moongoka.
14
“Koma mukapanda kundimvera ndi kutsata malamulo anga onseŵa,
15
mukamanyoza malamulo anga, ndipo mtima wanu ukamadana ndi zimene ndikulamulani, mpaka kusamvera malamulo anga onse ndi kuswa chipangano changa,
16
ndidzakuchitani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi, chifuwa chachikulu choondetsa ndiponso malungo oononga maso ndi ofooketsa moyo. Mudzabzala mbeu zanu, koma osakololapo kanthu, chifukwa choti adani anu adzazidya.
17
Ndidzakufulatirani, ndipo adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulani, ndipo muzidzangothaŵa popanda wokupirikitsani.
18
Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu.
19
Ndidzaononga nyonga zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale youma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuŵa.
20
Nyonga zanu zidzapita pachabe, poti nthaka yanu sidzabala kanthu, ndipo mitengo yake sidzabala zipatso.
21
“Tsono mukamayenda motsutsana ndi Ine osandimvera, ndidzabweretsa miliri inanso pa inu, yopambana machimo anu kasanunkaŵiri.
22
Ndidzabweretsanso zilombo zolusa pakati panu, zimene zidzakudyerani ana anu, ndi kukuwonongerani ng'ombe zanu. Zilombozo zidzachepetsa chiŵerengero chanu, kotero kuti m'njira zanu simuzidzapita anthu.
23
“Mukapanda kubwerera kwa Ine nditakulangani chotere, ndipo mukachitabe zotsutsana ndi Ine,
24
Inenso ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anuwo.
25
Ndidzabweretsa lupanga pa inu limene lidzakulangani chifukwa chophwanya chipangano changa. Ndipo mukasonkhana m'mizinda mwanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani m'manja mwa adani anu.
26
Ndidzachepetsa buledi wanu wa tsiku ndi tsiku mpaka akazi khumi adzapanga buledi mu uvuni umodzi. Ndipo adzakugaŵirani bulediyo pang'onopang'ono. Choncho mudzadya, koma osakhuta.
27
“Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndipo mukachitabe zotsutsana ndi Ine,
28
Inenso ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwiniwake ndidzakulangani mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu.
29
Mudzadya ana anu aamuna, ndipo mudzadyanso ana anu aakazi.
30
Ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano ku mapiri ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo lubani, ndipo ndidzaponya mitembo yanu pa mafano opanda moyo, ndipo ndidzadana nanu.
31
Ndidzasandutsa mizinda yanu kuti ikhale mabwinja, ndidzasandutsanso malo anu achipembedzo kuti akhale opanda anthu, ndipo sindidzalolanso kumva fungo lokoma la zopereka zanu.
32
Ndidzaononga dziko lanu kotero kuti adani anu amene adzakhale m'menemo adzadabwa.
33
Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzakupirikitsani, lupanga lili pambuyo. Dziko lanu lidzasanduka chipululu, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja.
34
“Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo.
35
Nthaŵi zonse pamene dzikolo lilibe anthu, nthaka idzapuma, kupuma kwake kumene sidapumepo pa zaka zonse pamene inu munkakhalamo.
36
Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani.
37
Mudzaphunthwitsana monga ngati mukuthaŵa nkhondo, ngakhale palibe amene akukupirikitsani. Ndipo simudzakhala ndi mphamvu zoti mulimbane ndi adani anu.
38
Mudzatha, kuchita kuti psiti, pakati pa mitundu ya anthu, ndipo dziko la adani anu lidzakudyani.
39
Ngakhale ena amene mudzatsalenu, nanunso mudzazunzika m'dziko la adani anu chifukwa cha machimo anu, ndipo mudzazunzikanso chifukwa cha machimo a makolo anu.
40
“Tsono adzaulula machimo ao ndi machimo a makolo ao chifukwa cha kunyenga kwao kumene adandinyenga nako, ndiponso chifukwa cha kuyenda motsutsana ndi Ine.
41
Paja chifukwa cha zimenezo Ine ndidatsutsana nawo ndi kuŵafikitsa ku dziko la adani ao. Tsono mitima yao youma idzadzichepetsa ndi kulola kulangidwa chifukwa cha machimo ao.
42
Pamenepo ndidzakumbukira chipangano changa ndi Yakobe, Isaki, ndi Abrahamu, ndipo dzikolo ndidzalikumbukira.
43
Koma ayambe aisiya nthaka yaoyo, kuti ikondwerere zaka zoipumuza, pamene dziko lili lopanda anthu, iwo atachoka. Tsono iwo adzalangika chifukwa cha machimo ao, popeza kuti adanyoza zimene ndidaŵalamula, ndipo mitima yao idadana ndi malangizo anga.
44
Ngakhale zitachitika zonsezo, pamene ali m'dziko la adani ao, sindidzaŵanyoza ndipo sindidzadana nawo mpaka kuŵaononga kwathunthu ndi kuphwanya chipangano changa ndi iwo, chifukwa Ine ndine Chauta, Mulungu wao.
45
Koma poŵachitira chifundo ndidzakumbukira chipangano changa ndi makolo ao amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, mitundu ina ya anthu ikupenya, kuti ndikhale Mulungu wao. Ine ndine Chauta.”
46
Ameneŵa ndiwo malamulo ndi malangizo amene Chauta adaika pakati pa Iye mwini ndi Aisraele pa phiri la Sinai, kudzera mwa Mose.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27