bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 8
Leviticus 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 9 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Utenge Aroni ndi ana ake. Utengenso zovala, mafuta odzozera, ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziŵiri zamphongo, ndipo utengenso dengu la buledi wosafufumitsa.
3
Tsono usonkhanitse mpingo wonse pa khomo la chihema chamsonkhano.”
4
Mose adachitadi zomwe Chauta adamlamula. Choncho mpingo wonse udasonkhana pa khomo la chihema chamsonkhano.
5
Ndipo adauza mpingo wonsewo kuti, “Nazi zimene Chauta walamula kuti zichitike.”
6
Apo Mose adabwera ndi Aroni ndi ana ake, naŵasambitsa.
7
Kenaka adamuveka mwinjiro Aroniyo, ndi kummanga lamba m'chiwuno. Adamuveka mkanjo ndi chovala cha efodi, ndipo adammanganso lamba wa efodiyo m'chiwuno.
8
Tsono adamuveka chovala chapachifuwa, ndipo m'chovalacho adaikamo zinthu zotchedwa Urimu ndi Tumimu.
9
Ndipo adamuveka nduŵira kumutu. Kumaso kwa nduŵirayo adaikako mphande yagolide, chizindikiro chopatulira, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
10
Pambuyo pake Mose adatenga mafuta odzozera, nadzoza chihema chamsonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, ndipo adazipatula.
11
Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika.
12
Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika.
13
Kenaka adabwera ndi ana a Aroni aja naŵaveka miinjiro, naŵamanga malamba m'chiwuno, ndi kuŵaveka zikofiya kumutu.
14
Pambuyo pake Mose adabwera ndi ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.
15
Kenaka Mose adaipha natenga magazi ake ndi kuŵapaka ndi chala chake pa nyanga za guwa molizungulira, ndipo adaliyeretsa. Adathiranso magazi patsinde pa guwalo nalipatula. Motero adachita mwambo wopepesera machimo.
16
Tsono Mose adatenga mafuta onse akumatumbo ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndi imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndipo adazitenthera paguwapo.
17
Koma ng'ombe yamphongo ija, chikopa chake, nyama yake, ndi ndoŵe yake, zonsezi adazitenthera kunja kwa mahema, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
18
Pambuyo pake adapereka nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosayo.
19
Kenaka Mose adaipha nathira magazi ake pa guwa mozungulira.
20
Atadula nkhosayo nthulinthuli, Mose adatentha mutu wake ndi nthuli zija ndi mafuta ake omwe.
21
Tsono atatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, adazitenthanso. Motero adatentha nkhosa yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma, yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, monga momwe Iye adaalamulira Mose.
22
Tsono Mose adapereka nkhosa ina yamphongo, yoyenerera pa mwambo wodzoza ansembe. Ndipo Aroni pamodzi ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.
23
Apo Mose adaipha, natengako magazi ake naŵapaka pa nsonga ya khutu la Aroni ku dzanja lamanja. Adapakanso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha ku phazi la dzanja lamanja.
24
Pambuyo pake adabwera ndi ana a Aroni, ndipo Mose adapaka magazi pa nsonga za makutu ao a ku dzanja lamanja ndi pa zala zao zazikulu za ku dzanja lamanja, ndiponso pa zala zao zazikulu za ku phazi la ku dzanja lamanja. Kenaka Mose adathira magazi pa guwa molizungulira.
25
Adatenga mafuta, mchira wamafuta, mafuta onse akumatumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ake omwe, ndi ntchafu ya ku dzanja lamanja.
26
Ndipo m'dengu la buledi wosafufumitsa, lopatulikira Chauta, adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi wopaka mafuta ndi mtanda umodzi wa buledi wopyapyala. Zonsezo ataziika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija,
27
adazikhazika m'manja mwa Aroni ndi m'manja mwa ana ake, ndipo adaziweyula kuti zikhale zopereka zoweyula kwa Chauta.
28
Pambuyo pake Mose adazichotsa m'manja mwaomo nazitentha pa guwa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ija, kuti zikhale nsembe yopereka pa mwambo wodzoza ansembe, ya fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto yopereka kwa Chauta.
29
Ndipo adatenga nganga naiweyula kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Chimenecho ndicho chigawo cha Mose cha nkhosa yamphongo yopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata malamulo a Chauta kwa Mose.
30
Tsono Mose adatengako mafuta odzozera aja ndi magazi amene anali pa guwa, nawaza Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zao. Umu ndimo m'mene Mose adapatulira Aroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zao.
31
Mose adauza Aroni ndi ana ake kuti, “Muphike nyamayo pa khomo la chihema chamsonkhano, ndipo muidyere pomwepo, pamodzi ndi buledi amene ali m'dengu la zopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata zimene Chauta adaalamula kuti, ‘Aroni pamodzi ndi ake ndiwo adzadye zimenezo.’
32
Zotsala zake za nyamayo ndi za buledi zomwe, muzitenthe.
33
Ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano, mpaka masiku a mwambo wodzoza ansembe atatha, poti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi aŵiri.
34
Chauta adatilamula kuti tikuchiteni zimene takuchitanizi, kuti ukhale mwambo wopepesera machimo anu.
35
Muzikhala pa khomo la chihema chamsonkhano usiku ndi usana, masiku asanu ndi aŵiri, ndipo muzichita zimene Chauta wakulamulani, kuti mungafe. Zimenezi nzimene Chauta wandilamula.”
36
Tsono Aroni ndi ana ake adachitadi zonsezo, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27