bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 24
Leviticus 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 25 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Lamula Aisraele kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri, kuti nyale izikhala yoyaka nthaŵi zonse m'Nyumba mwanga.
3
Aroni aiyatse nyaleyo pamaso pa Chauta kunja kwa nsalu yochinga bokosi lachipangano, limene lili m'chihema chamsonkhano, kuti ikhale chiyakire kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse.
4
Aroni ayatse nyale zimene zili pa choikapo chake cha golide wabwino kwambiri, kuti zikhale zoyaka nthaŵi zonse pamaso pa Chauta.
5
“Mutenge ufa wosalala, ndipo muphike makeke khumi ndi aŵiri. Keke iliyonse ikhale ya ufa wokwanira makilogaramu aŵiri.
6
Muŵaike m'mizere iŵiri pa tebulo la golide wabwino kwambiri, mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi.
7
Pa mzere uliwonse muikepo lubani wokoma, kuti pamodzi ndi bulediyo akhale chikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta.
8
Pa tsiku la Sabata lililonse Aroni aziika makeke a nsembeyo mosalephera pamaso pa Chauta m'malo mwa Aisraele, kuti chikhale chipangano chamuyaya.
9
Chakudyacho chikhale cha Aroni ndi ana ake, ndipo achidyere m'malo oyera, pakuti kwa iyeyo chimenecho nchopatulika kopambana, chochokera pa nsembe yopsereza kwa Chauta. Lamuloli ndi lamuyaya.”
10
Tsiku lina munthu wina amene mai wake anali Wachiisraele, koma bambo wake anali wa ku Ejipito, adapita kwa Aisraele ndipo adakangana ndi Mwisraele mmodzi ku mahema.
11
Munthu uja adanyoza dzina la Chauta ndi kulitemberera. Tsono adabwera naye kwa Mose. Dzina la mai wake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.
12
Adamuika m'ndende mpaka atadziŵa kufuna kwa Chauta.
13
Chauta adauza Mose kuti,
14
“Umtulutse kuzithandoko munthu wotembererayo. Onse amene adamumva akutemberera asanjike manja ao pamutu pake, kutsimikiza kuti ndi wochimwadi, ndipo mpingo wonse umponye miyala.
15
Tsono uza Aisraele kuti, ‘Aliyense wotemberera Mulungu wake alangidwe,
16
wonyoza dzina la Chauta ayenera kuphedwa. Mpingo wonse umponye miyala. Mlendo kapena mbadwa akangonyoza dzina la Chauta, ayenera kuphedwa.
17
Munthu wopha mnzake ayenera kuphedwa.
18
Munthu wopha choŵeta cha mnzake amlipire china, moyo ulipe moyo.
19
Munthu akapundula mnzake, nayenso amchite zomwezo.
20
Kuphwanya fupa kulipe kuphwanya fupa, diso lilipe diso, dzino lilipe dzino. Monga momwe munthu adapundulira mnzake, nayenso amchite zomwezo.
21
Munthu wopha choŵeta cha mnzake, alipire china, koma munthu wopha mnzake ayenera kuphedwa.
22
Lamulo la mlendo ndi mbadwa likhale limodzi lomwelo. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ”
23
Mose adauza Aisraele zimenezi, ndipo iwo adatulutsa munthu wotemberera uja m'zithandomo, namponya miyala. Motero Aisraele adachita zimene Chauta adalamula Mose.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27