bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 13
Leviticus 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 14 →
1
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2
“Munthu akakhala ndi chithupsa pathupi pake, kapena m'buko, kapena chikanga, ndipo mwina nkusanduka ngati nthenda ya khate pakhungu pakepo, munthuyo abwere naye kwa wansembe Aroni kapena kwa aliyense mwa ana ake amene ali ansembe.
3
Wansembe aonetsetse pakhungu pali nthendapo. Akapeza kuti ubweya wa pamalo pali nthendapo wasanduka woyera, ndipo kuti nthendayo yazama ndithu kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe atamuwonetsetsa ndithu, amutchule kuti ndi woipitsidwa.
4
Koma pakhungupo pakamaoneka kuti mpoyera, ndipo nthendayo sidapitirire khungu, ndipo ubweya wapamalopo sudasanduke woyera, wansembeyo amuike padera munthu wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.
5
Wansembe amuwonetsetse wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Akaiwona nthendayo kuti sidafalikire pa khungu, pamenepo wansembeyo amtsekere munthu uja masiku asanu ndi aŵiri ena.
6
Tsono wansembe uja amuwonetsetsenso wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Pakhungu pakakhala pothimbirira, nthendayo yosafalikira pakhungupo, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi wosaipitsidwa. Umenewo ndi m'buko chabe, tsono wodwalayo achape zovala zake, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
7
Koma m'bukowo ukafalikira pa khungu, munthuyo atadziwonetsa kale kwa wansembe kuti amuyeretse, munthuyo akaonekerenso pamaso pa wansembe.
8
Wansembe amuwonetsetsenso munthuyo. Akaona kuti m'bukowo wafalikiradi pa khungu, atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa, limenelo ndi khate.
9
“Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, abwere naye kwa wansembe.
10
Wansembe amuwonetsetse. Akakhala ndi chithupsa cha maonekedwe oyera pa khungu, chimene chasandutsa ubweya wapamalopo kukhala woyera, ndipo pachithupsapo pakakhala zilonda,
11
limenelo ndi khate lachikhalire limene lili pakhungu pakelo, ndipo wansembe amutchule kuti ndi woipitsidwa. Sikufunika kumtsekera chifukwa ndi woipitsidwadi.
12
Khatelo likafalikira pa khungu, kotero kuti likhala litagwira khungu lonse la munthu wodwalayo kuyambira kumutu mpaka kumapazi, monga m'mene wansembe angaonere,
13
pamenepo wansembeyo aonetsetse. Khatelo likakhala litagwira thupi lonse, wodwalayo amutchule kuti ndi wosaipitsidwa. Thupi lonse lasanduka loyera ndipo munthuyo ndi wosaipitsidwa.
14
Koma pathupi pake pakaoneka zilonda, ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa.
15
Tsono wansembe aonetsetse zilondazo, ndipo munthu wodwalayo amtchule kuti ndi woipitsidwa. Zilondazo nzoipitsa poti limenelo ndi khate.
16
Koma zilondazo zikasinthikanso ndi kusanduka zoyera, pamenepo munthu wodwalayo abwere kwa wansembe.
17
Tsono wansembeyo amuwonetsetse. Zilondazo zikakhala kuti zasanduka zoyera, wansembeyo amutchule munthu wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Ndi woyera ameneyo.
18
“Pa khungu la munthu wodwalayo pakakhala chithupsa choti chidapola,
19
ndipo pamene panali chithupsacho pakatuluka zotupatupa zoyera kapena banga loyera mofiirira, aziwonetse kwa wansembe.
20
Wansembe aonetsetse bwino, ndipo chithupsacho chikazama, ubweya wake nusanduka woyera, wansembeyo amutchule munthu wodwala uja kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yaphulika pachithupsapo.
21
Koma wansembe akaonetsetsa, napeza kuti ubweya wake sudasanduke woyera, ndipo chithupsacho sichidazame, koma chikuzimirira, wansembeyo amuike padera wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.
22
Nthendayo ikafalikira pa khungu, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa, limenelo ndi khate.
23
Koma bangalo likakhala pa malo amodzi, osafalikira, chimenecho nchipsera cha chithupsa. Wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa.
24
“Munthu akakhala ndi bala lamoto, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera kumene,
25
wansembe aliwonetsetse. Ubweya wapabangapo ukasanduka woyera, ndipo balalo likaoneka kuti lazama, limenelo ndi khate lomwe laphulika pa balalo. Wansembe atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate.
26
Koma wansembe akaonetsetsa, napeza kuti ubweya wake sudasanduke woyera, ndipo balalo silidazame, koma likuzimirira, wansembe amuike padera wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri.
27
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate.
28
Koma bangalo likakhala pa malo amodzi losafalikira pa khungu, ndipo likuzimirira, limenelo ndi thuza la balalo. Wansembeyo amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa, popeza kuti nchipsera cha bala lamoto chabe.
29
“Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena kundevu,
30
wansembe aiwonetsetse nthendayo. Ikaoneka kuti ikuzama, ndipo ubweya ukakhala wachikasu ndi wotetemera, wansembeyo amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi mfundu yonyerenyesa, khate lakumutu kapenanso lakundevu.
31
Wansembe ataiwonetsetsa mfundu yonyerenyesayo, niwoneka kuti sidazame, ndipo palibe ubweya wakuda pamalopo, wansembeyo amuike padera munthu wodwala mfundu yonyerenyesayo masiku asanu ndi aŵiri.
32
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonenso nthendayo. Mfunduyo ikakhala yakuti sidafalikire, ndipo palibe ubweya wachikasu, ndipo mfunduyo ikaoneka kuti sidazame,
33
wodwalayo amete, koma mfunduyo asaimete. Wansembe amtsekere masiku asanu ndi aŵiri ena munthu wodwala mfundu yonyerenyesayo.
34
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonetsetsenso mfunduyo, ndipo ikakhala yakuti sidafalikire pa khungu, ndiponso ikaoneka kuti sidazame, wansembe atchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Tsono wadwalayo achape zovala zake, ndipo akhale wosaipitsidwa.
35
Koma mfunduyo ikafalikira pa khungu, wodwalayo atayeretsedwa kale,
36
pamenepo wansembe amuwonetsetse wodwalayo. Mfunduyo ikakhala itafalikira pa khungu, wansembe asafunefune ubweya wachikasu ai, munthuyo ndi woipitsidwa.
37
Koma wansembe akaipenyetsetsa mfunduyo napeza kuti pamera ubweya wakuda, ndiye kuti mfunduyo ndi yopola. Tsono wansembe amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa.
38
“Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi maŵanga oyera pa khungu,
39
wansembe aonetsetse bwino. Maŵanga apakhunguwo akakhala oyerera, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pakhungupo. Tsono munthuyo ndi wosaipitsidwa.
40
“Tsitsi la munthu likatha kumutu chapankhongo, ndiye kuti ndi dazi limenelo, koma munthuyo ndi wosaipitsidwa.
41
Munthu akakhala wopanda tsitsi pa mphumi ndiponso m'litsipa, ndiye kuti ali ndi dazi lapamphumi, koma ndi wosaipitsidwa.
42
Koma pa dazi lapankhongo kapena lapamphumi pakakhala banga la nthenda loyera mofiirira, limenelo ndi khate limene likutuluka pa nkhongo kapena pa mphumi.
43
Tsono wansembe amuwonetsetse wodwalayo, ndipo banga lotupalo likakhala loyera mofiirira pa dazi lapankhongolo kapena lapamphumilo, monga m'mene limaonekera khate pa khungu,
44
ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Wansembe ayenera kumtchula kuti ndi woipitsidwa, ali ndi khate lakumutu.
45
“Munthu wakhate avale nsanza, ndipo tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wam'mwamba, ndipo azifuula kuti, ‘Ndine woipitsidwa, ndine woipitsidwa.’
46
Wodwalayo adzakhalabe woipitsidwa nthaŵi zonse pamene ali ndi nthendayo, ndipo akhale payekha kunja kwa mahema.
47
“Chovala chaubweya kapena chathonje chikakhala ndi nguwi
48
kapena nsalu yathonje kapena yaubweya, kapenanso chikopa kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa,
49
ndipo nguwiyo ikakhala ndi maonekedwe achisipu kapena ofiira pa chovalapo, kapena pa thonje loluka, kapena pa chikopa, kaya pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nguwi ndithu, ndipo chovalacho achiwonetse kwa wansembe.
50
Wansembeyo aiwonetsetse nguwiyo. Chovalacho achiike padera masiku asanu ndi aŵiri.
51
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri aiwonetsetsenso nguwiyo. Ikakhala itafalikira pa chovalacho, kapena pa chikopa cha ntchito ya mtundu uliwonse, imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chovalacho ndi choipitsidwa.
52
Tsono wansembe achitenthe chovalacho, chifukwa nguwiyo yaipitsa chovala chaubweya kapena chathonjecho, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, poti imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chinthucho achitenthe.
53
“Wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo sidafalikire pa chovalacho, kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa,
54
wansembeyo alamule kuti achape chovalacho, ndipo achiike padera masiku asanu ndi aŵiri ena.
55
Ndipo wansembe achiwonetsetse chovala chimenecho chitachapidwa. Ngati banga la nguwiyo silidasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti siidafalikire, chovalacho nchoipitsidwa ndithu. Muchitenthe, osasamala zakuti banga la nguwiyo lili kumbuyo kapena kumaso.
56
“Koma wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo njothimbirira atachapa chovalacho, ang'ambe banga la nguwilo pa chovala chathonjecho kapena chachikopacho.
57
Bangalo likaonekanso pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Zonse zanguwizo muzitenthe.
58
Koma chovala, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachapa, tsono nguwiyo nkuchoka, muchapenso kachiŵiri, ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”
59
Limeneli ndi lamulo la nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena m'chovala chathonje, kapenanso m'chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
Recommended Reading
Commentary
Leviticus Commentaries
→
Devotional
Leviticus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→