bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 4
Leviticus 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 5 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Uza Aisraele kuti pa zonse zimene Chauta adaletsa, munthu aliyense akachimwapo mosadziŵa, pochita kanthu kena kalikonse koletsedwa, azichita izi:
3
wochimwayo akakhala wansembe wodzozedwa, pakutero wausandutsa wopalamula mpingo wonse, tsono azipereka kwa Chauta ng'ombe yaing'ono yamphongo yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo ake.
4
Wansembe abwere ndi ng'ombeyo pa khomo la chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphe pamaso pa Chauta.
5
Kenaka wansembe wodzozedwayo atengeko magazi a ng'ombeyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano.
6
Apo aviike chala chake m'magazi, ndi kuwaza magaziwo kasanu ndi kaŵiri patsogolo pa nsalu yochinga malo oyera pamaso pa Chauta.
7
Pambuyo pake wansembe apakeko magaziwo pa nyanga za guwa la m'chihema chamsonkhano lofukizirapo lubani wonunkhira fungo lokoma pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala a ng'ombeyo aŵathire pa tsinde la guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
8
Tsono mafuta onse a ng'ombe yamphongo yoperekera nsembe yopepesera machimoyo, aŵachotse pamodzi ndi mafuta okuta matumbo, ndiponso mafuta ena onse okhala pamatumbopo.
9
Achotsenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu za mafuta akuchiŵindi ochotsa pamodzi ndi imso zija,
10
monga momwe amazichotsera ku ng'ombe yopereka pa nsembe yachiyanjano. Tsono wansembeyo atenthe zonsezo pa guwa la nsembe zopsereza.
11
Koma chikopa cha ng'ombe yamphongoyo, pamodzi ndi mnofu wake, mutu wake, miyendo yake, matumbo ake ndi ndoŵe yake,
12
kungoti ng'ombe yonseyo, atuluke nayo kunja kwa mahema, ku malo oyeretsedwa kumene amatayako phulusa, ndipo pamalo pomwepo aitenthere pa moto wankhuni.
13
“Ngati mpingo wonse wa Aisraele uchimwa mosachitira dala, nuchita zimene Chauta amaletsa, ngakhale uli wosadziŵako, ngwopalamula ndithu.
14
Tsono tchimo lakelo nkudziŵika, mpingo wonsewo upereke ng'ombe yaing'ono yamphongo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo abwere nayo pa khomo la chihema chamsonkhano.
15
Apo atsogoleri a mpingo asanjike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Chauta, ndipo aiphe pamaso pa Chauta.
16
Wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ng'ombe yamphongoyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano.
17
Pamenepo wansembeyo aviike chala chake m'magazi, ndipo pamaso pa Chauta awaze magaziwo kasanu ndi kaŵiri patsogolo pa nsalu yochinga.
18
Pambuyo pake magaziwo aŵapake pa nyanga za guwa limene lili m'chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala aŵathire patsinde pa guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
19
Kenaka mafuta ake onse aŵachotse ndi kuŵatenthera pa guwa.
20
Umu ndimo m'mene ng'ombe yamphongo aichitire. Monga adachitira ndi ng'ombe yamphongo yopereka pa nsembe yopepesera machimo, ndimo aichitirenso imeneyi. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimowu, mpingowo udzakhululukidwa.
21
Tsono ng'ombeyo aitulutsire kunja kwa mahema ndi kuitentha monga momwe adachitira ndi yoyamba ija. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo, yoperekera mpingo wonse.
22
“Wolamula akachimwa mosadziŵa, kuchimwira Chauta, Mulungu wake, pa chinthu choletsedwa, napalamula pakutero,
23
pambuyo pake ena nkumudziŵitsa za tchimo lakelo, iyeyo apereke nsembe ya tonde wopanda chilema.
24
Tsono wolamulayo asanjike dzanja lake pamutu pa tondeyo ndi kumupha pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza pamaso pa Chauta. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo.
25
Wansembe atengeko magazi a tondeyo ndi chala chake, aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalowo patsinde pa guwa lomwelo.
26
Kenaka mafuta ake onse aŵatenthere pa guwa, monga momwe amachitira ndi mafuta a nsembe yachiyanjano. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a wopalamula uja, munthuyo adzakhululukidwa.
27
“Ngati munthu wamba aliyense achimwa mosadziŵa, pochita china chilichonse chimene Chauta amaletsa, napalamula pakutero,
28
tchimo lakelo akalizindikira, apereke nsembe ya mbuzi yaikazi yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo.
29
Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa mbuzi ya nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aiphere pa malo amene amaperekera nsembe yopsereza.
30
Atatero, wansembe atengeko magazi ndi chala chake, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndipo magazi otsalawo aŵathire patsinde pa guwa lomwelo.
31
Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano, ndipo wansembe aŵatenthe pa guwalo, kuti atulutse fungo lokomera Chauta. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a munthu wamba uja, munthuyo adzakhululukidwa.
32
“Ngati munthu abwera kudzapereka nkhosa ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa yake ikhale yaikazi, yopanda chilema.
33
Ndipo asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosa ya nsembe yopepesera machimoyo, ndi kuiphera pa malo amene amaphera nsembe yopsereza.
34
Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a nkhosayo ndi chala chake, ndipo aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalawo patsinde pa guwalo.
35
Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nkhosa yoperekera nsembe yachiyanjano. Ndipo aŵatenthe pa guwa, pamodzi ndi nsembe zina zopsereza pa moto, zopereka kwa Chauta. Umu ndimo m'mene wansembe azichitira mwambo wopepesera tchimo la munthu, ndipo munthuyo adzakhululukidwa.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27