bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 18
Leviticus 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 19 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Uza Aisraele kuti, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
3
Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao.
4
Muzichita zimene ndikukulamulani, ndi kutsata malamulo anga ndi kuŵamvera. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
5
Nchifukwa chake muchite zimene ndikukulamulani ndipo muzimvera malamulo anga, motero mudzakhala ndi moyo. Ine ndine Chauta.
6
“Munthu wina aliyense mwa inu asagone ndi wachibale wake. Ine ndine Chauta.
7
Usachititse manyazi bambo wako pakugona ndi mai wako. Ameneyo ndi mai wako, usamchititse manyazi.
8
Usachititse manyazi bambo wako pakugona ndi mkazi wake aliyense.
9
Usagone ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa bambo wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, ngakhale abadwire kwanu kapena kuchilendo.
10
Usagone ndi mdzukulu wako, mwana wa mwana wako wamwamuna, kapena mdzukulu wako, mwana wa mwana wako wamkazi, chifukwa kuteroko nkudzivula.
11
Usagone ndi mwana wamkazi wa mkazi wa bambo wako amene bambo wakoyo adabala, poti ameneyo ndi mlongo wako.
12
Usagone ndi mlongo wa bambo wako, poti ameneyo ndi thupi limodzi ndi bambo wako.
13
Usagone ndi mbale wa mai wako, poti ameneyo ndi thupi limodzi ndi mai wako.
14
Usagone ndi mkazi wa mbale wa bambo wako, poti ameneyo ndi mai wako.
15
Usagone ndi mkazi wa mwana wako, poti ameneyo ndi mpongozi wako.
16
Usagone ndi mkazi wa mbale wako, chifukwa kuteroko nkuvula mbale wako.
17
Usagone ndi mkazi ndiponso ndi mwana wamkazi wa mkaziyo, ndipo usagone ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi lake la mkaziyo, ndipo kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri.
18
Ndipo usakwatire mbale wa mkazi wako ndi kumuvula pamene mbale wako ali moyo.
19
“Usayandikire mkazi kuti umvule pamene ali wosamba.
20
Usagone ndi mkazi wa mnzako ndi kudziipitsa naye.
21
Usatenge mwana wako aliyense kuti umpereke ngati nsembe yamoto kwa Moleki, kuti ungaipitse dzina la Mulungu wako. Ine ndine Chauta.
22
Usagone ndi mwamuna ngati mkazi. Chimenecho ndi chinthu chonyansa.
23
Ndipo usagone ndi nyama ndi kudziipitsa nayo, ngakhalenso mkazi aliyense asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo, pakuti chimenecho ndi chisokonezo choopsa.
24
“Musadziipitse ndi zinthu zimenezi, chifukwa mitundu ina ya anthu amene ndikuipirikitsa inu mukubwera, idadziipitsa ndi zoipa zoterezi.
25
Dziko lidaipa kotero kuti ndidalanga tchimo lake, ndipo dzikolo lidasanza anthu ake okhalamo.
26
Koma inuyo mutsate malamulo anga ndi kuchita zimene ndikukulamulani. Musachite chilichonse mwa zonyansazi, ngakhale inu mbadwanu kapena mlendo wokhala pakati panu.
27
Pajatu anthu am'dzikomo amene adaalipo inu musanafike, ankachita zonyansa zonsezi, kotero kuti dziko lidaipitsidwa.
28
Musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mukaliipitsa, monga momwe lidasanzira mtundu wa anthu umene udaalipo m'dzikomo, inu musanafike.
29
Pakuti aliyense amene adzachita zonyansa zimenezi, adzachotsedwa pakati pa anthu anzake.
30
Tsono mverani malamulo anga oletsa kutsata zonyansa zimene anthu ankazichita, inu musanafike. Musadziipitse nazo konse. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27