bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 27
Leviticus 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Uza Aisraele kuti: Ngati munthu adalumbira kuti adzapereka munthu mnzake kwa Mulungu, koma pambuyo pake akufuna kumuwombola,
3
zoyenera kupereka ndi izi: pa munthu wamwamuna wa zaka makumi aŵiri mpaka zaka 60, pakhale masekeli asiliva 50, potsata kaŵerengedwe ka kunyumba ya Mulungu.
4
Munthu wake akakhala wamkazi, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva makumi atatu.
5
Akakhala munthu wa zaka zisanu mpaka zaka makumi aŵiri, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva makumi aŵiri pa munthu wamwamuna, ndipo khumi pa munthu wamkazi.
6
Akakhala munthu wa mwezi umodzi mpaka zaka zisanu, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva zisanu pa munthu wamwamuna, ndipo zitatu pa munthu wamkazi.
7
Munthu wake akakhala wa zaka 60 kapena kupitirirapo, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva 15 pa munthu wamwamuna, ndipo khumi pa munthu wamkazi.
8
Munthu akakhala wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira mtengo umenewo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo aike mtengo pa iye. Mtengo umene wansembeyo aike ukhale wolingana ndi momwe munthu wolumbirayo angalipire.
9
“Ikakhala nyama yonga imene anthu amaperekera nsembe kwa Chauta, zonse zimene anthu amapereka kwa Chauta nzopatulika.
10
Munthu asapereke ina m'malo mwake kapena kuisinthitsa ndi ina, asapereke yabwino m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yabwino. Ndipo akasinthitsa nyama ina ndi inzake, nyamayo pamodzi ndi inzake waisinthitsayo zikhala zopatulika.
11
Ikakhala nyama yonyansa, yonga imene siloledwa kuipereka ngati nsembe kwa Chauta, munthuyo abwere ndi nyamayo kwa wansembe.
12
Ndipo wansembe atchule mtengo wake poona ngati njabwino kapena ai. Monga momwe iwe wansembe utchulire, mtengo udzakhala momwemo.
13
Koma akafuna kuti aiwombole, aonjezepo pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wakewo.
14
“Pamene munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulikira Chauta, wansembe aiwone ngati ili yabwino kapena ai. Monga momwe wansembe aiwonere, idzakhala momwemo.
15
Munthu woiperekayo akafuna kuti aombole nyumba yakeyo, pa mtengo wake wa nyumbayo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo idzakhala yake.
16
“Munthu akapereka kwa Chauta chigawo cha dera la choloŵa chake, mtengo umene uike ukhale wolingana ndi mbeu zodzabzalamo. Pa mbeu za barele zokwanira makilogaramu 20, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva 50.
17
Akapereka munda wake kuyambira pa chaka chokondwerera zaka 50, mtengo wake ukhale wathunthu monga momwe iwe udaikira.
18
Koma akapereka munda wake chitatha chaka chokondwerera zaka 50, wansembe aŵerenge mtengo wa ndalama molingana ndi zaka zotsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka 50, ndipo achotse pa mtengo umene wansembe waika.
19
Munthu amene adapereka munda, akafuna kuti auwombole, pa mtengo wa mundawo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo udzakhala wake.
20
Koma ngati safuna kuti aombole kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzaombolekanso.
21
Mwini mundawo atausiya pa chaka chokondwerera zaka 50, udzakhala wopatulikira Chauta ngati munda woperekedwa. Wansembe adzautenga kuti ukhale wake.
22
Munthu akapereka kwa Chauta munda umene waugula, umene suli chigawo cha choloŵa chake,
23
wansembe aŵerenge mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka 50. Tsono munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo, kuti zikhale zopatulikira Chauta.
24
Pa chaka chokondwerera zaka 50, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene adaugulitsayo, amene mtundawo unali wake ngati choloŵa chake.
25
Potchula mtengo uliwonse, wansembe aziŵerenga monga momwe amaŵerengera m'Nyumba ya Chauta, ndiye kuti sekeli imodzi ikwanire magera makumi aŵiri.
26
“Koma pasakhale munthu amene apereke mwana woyamba wa nyama. Mwanayo ali kale wa Chauta, popeza kuti ndi woyamba. Ngakhale ikhale ng'ombe kapena nkhosa, nja Chauta imeneyo.
27
Ikakhala nyama yonyansa pa chipembedzo, aiwombole pa mtengo umene wansembe aike, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake. Koma akapanda kuiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe aike.
28
“Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwathunthu kwa Chauta, kaya ndi munthu kapena nyama kapena munda umene uli choloŵa chake, chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Chinthu chilichonse choperekedwa choncho kwa Chauta, nchopatulika kopambana.
29
Munthu aliyense amene waperekedwa kotheratu, sangathe kuwomboledwa, aziphedwa basi.
30
“Chigawo chilichonse chachikhumi cham'dziko, kaya ndi cha mbeu zam'nthaka, kaya ndi cha zipatso zam'mitengo, nchake cha Chauta. Chimenecho nchopatulikira Chauta.
31
Munthu akafuna kuti aombole chigawo chimodzi chachikhumi chilichonse, aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake.
32
Ndipo chigawo chachikhumi chilichonse cha nsambi wa ng'ombe ndi wa nkhosa, ndiye kuti nyama yachikhumi iliyonse imene mbusa aiŵerenge, ikhale yopatulikira Chauta.
33
Mwiniwake asafunse ngati nyamayo njabwino kapena njoipa, ndipo asaisinthitse. Akaisinthitsa ndi ina, imeneyo pamodzi ndi imene waisinthitsayo zidzakhala zopatulikira Chauta, ndipo sangaziwombole.”
34
Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose pa phiri la Sinai kuti auze Aisraele.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27