bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 11
Leviticus 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 12 →
1
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2
“Auzeni Aisraele kuti nyama zimene angathe kudya pakati pa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi izi:
3
‘Nyama zonse zokhala ndi ziboda zogaŵikana, ndi zobzikula, angathe kudya zimenezo.
4
Koma pakuti pa nyama zobzikula kapena za ziboda zogaŵikanazo, asadye izi: ngamira: imeneyi njonyansa kwa inu pa zachipembedzo, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.
5
Mbira: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.
6
Kalulu: ameneyu ndi wonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale amabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana.
7
Nkhumba: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale ziboda zake nzogaŵikana ndipo mapazi ake ngogaŵikananso, koma siibzikula.
8
Nyama ya zoŵeta zimenezo musamadye, ndipo zikafa musazikhudze. Zimenezi nzonyansa kwa inu.’
9
“Zamoyo zam'madzi zimene mutha kudya ndi izi: zonse zam'madzi zimene zili ndi zilimba ndi mamba, mungathe kudya, ngakhale zikhale zam'nyanja kapena zam'mitsinje.
10
Koma zamoyo zonse zam'nyanja kapena zam'mitsinje zopanda zilimba ndi mamba, tizilombo tonse tam'madzi ndi zamoyo zonse zopezeka m'menemo, nzonyansa kwa inu.
11
Zimenezo zikhale zonyansa kwa inu, ndipo musadye. Zikafa zikhalebe zonyansa kwa inu.
12
Zamoyo zonse zam'madzi zopanda zilimba ndi mamba, nzonyansa kwa inu.
13
“Ndipo mbalame zimene muyenera kuziyesa zonyansa, zoti simuyenera kudya, popeza kuti nzonyansa kwa inu, ndi izi: mphungu, nkhwazi, ndi muimba,
14
nankapakapa, akamtema a mitundu yonse,
15
akhungubwi a mitundu yonse
16
nthiŵatiŵa, chipudo, kakoŵa, akabaŵi a mitundu yonse,
17
kadzidzi, chiswankhono ndi mantchichi,
18
tsekwe, vuwo, dembo,
19
indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.
20
“Zonse za miyendo inai, zouluka, nzonyansa kwa inu.
21
Komabe pakati pa zouluka zonse za miyendo inai, mungathe kudya zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira pa dothi.
22
Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse.
23
Koma zamapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inai nzonyansa kwa inu.
24
“Tsono zimenezi mukazikhudza, zidzakuipitsani, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
25
Aliyense akanyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo.
26
Nyama iliyonse yokhala ndi ziboda zogaŵikana, koma mapazi ake osagaŵikana, kapenanso yosabzikula, njonyansa imeneyo kwa inu, ndipo aliyense woikhudza, adzakhala woipitsidwa.
27
Pakati pa nyama zonse za miyendo inai, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo ku mapazi, nzonyansa kwa inu, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
28
Ndipo munthu amene anyamula nyamazi zitafa, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Zimenezi nzonyansa kwa inu.
29
“Tsono zokwaŵa zonse zimene zili zonyansa kwa inu ndi izi: likongwe, mbeŵa, ng'azi za mitundu yonse,
30
gondwa, mng'anzi, buluzi dududu ndi birimankhwe.
31
Zimenezi nzonyansa kwa inu pakati pa zokwaŵa zonse. Munthu aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
32
Ndipo nyama zimenezi zikagwera pa chinthu chilichonse zitafa, chinthucho chidzakhala chonyansa, chingakhale chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa, kapena chiguduli, kapena chipangizo chilichonse chogwiritsa ntchito iliyonse. Chinthucho achiviike m'madzi, koma chidzakhalabe chonyansa mpaka madzulo. Pambuyo pake chidzakhala chabwino.
33
Tsono china chilichonse mwa zimenezi chikagwera m'mbiya yadothi, zonse za m'menemozo zidzakhala zonyansa, ndipo mbiyayo muiphwanye.
34
Madzi am'mbiyamo akathira pa chakudya chilichonse, chakudyacho chidzakhala chonyansa. Chakumwa chilichonse cha m'mbiya ya mtundu umenewo chidzakhala chonyansa.
35
Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse, chinthucho chidzakhala chonyansa, kaya ndi uvuni kapena chitofu, zonsezo aziphwanye, poti nzonyansa zimenezo, ndipo zidzakhala zonyansa kwa inu.
36
Koma kasupe kapena chitsime chamadzi zidzakhalabe zabwino, ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama chidzakhala chonyansa.
37
Chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbeu zimene anthu akuti abzale, mbeu zimenezo zikhalabe zabwino.
38
Koma mbeuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufa chigwera pa mbeuzo, zidzakhala zonyansa kwa inu.
39
“Munthu akakhudza nyama yofa yokha imene anthu amadya, munthuyo adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
40
Ndipo munthu amene adyako nyamayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Nayenso amene anyamula nyama yakufayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
41
“Chinthu chilichonse chokwaŵa pansi nchonyansa, ndipo musadye.
42
Chinthu chilichonse chokwaŵa ndi kumimba, ndiponso chilichonse cha miyendo inai kapena cha miyendo yambirimbiri, kungoti zonse zokwaŵa pansi, musadye poti nzonyansa kwa inu.
43
Musadzisandutse oipitsidwa ndi chokwaŵa chilichonse, musadziipitse nazo, kuti mungasanduke oipitsidwa.
44
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Tsono mudziyeretse, ndipo mukhale oyera pakuti Ine ndine woyera. Musadziipitse ndi chinthu chokwaŵa pansi chilichonse.
45
Pakuti Ine ndine Chauta, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale oyera, pakuti Ine ndine woyera.”
46
Limeneli ndilo lamulo lonena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda m'madzi, ndi chinthu chilichonse chokwaŵa pansi,
47
kuti muzisiyanitsa pakati pa zonyansa ndi zosanyansa, ndiponso pakati pa zamoyo zimene mungathe kudya ndi zimene simuyenera kudya.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27