bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 17
Leviticus 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 18 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Uza Aroni ndi ana ake, pamodzi ndi Aisraele onse, kuti Chauta akulamula kuti,
3
‘Mwisraele aliyense akapha ng'ombe, kapena mwanawankhosa, kapena mbuzi, ku zithando kapena kunja kwa zithando,
4
koma osabwera nayo pa khomo pa chihema chamsonkhano, kuti ikhale mphatso yopereka kwa Chauta, munthuyo wapalamula mlandu wa magazi, chifukwa wakhetsa magazi. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.
5
Ndiye kunena kuti Aisraele azitenga nyama zimene akadaphera kwina kwake, afike nazo pamaso pa Chauta kwa wansembe wokhala pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo aziphere pomweko, kuti zikhale nsembe zachiyanjano.
6
Ndipo wansembe awaze magazi ake pa guwa la Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Atatero atenthe mafuta ake, kuti atulutse fungo lokomera Chauta.
7
Motero nsembe zao asadzapherenso milungu yachabe imene amadziipitsa nayo. Limeneli likhale lamulo lao lamuyaya pa mibadwo yonse.’
8
“Uŵauze kuti, ‘Mwisraele aliyense, kapena mlendo amene amakhala pakati pao, wopereka nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse,
9
akapanda kubwera nayo pakhomo pa chihema chamsonkhano kudzaipereka pamaso pa Chauta, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’
10
“Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala pakati pao, akadya magazi, ndidzamfulatira ndi kumchotsa pakati pa anthu anzake.
11
Pakuti moyo wake wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi, ndipo ndaŵapereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amene amachotsa machimo, chifukwa cha moyo umene umakhala m'magazimo.
12
Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti munthu aliyense mwa inu, kapena mlendo wokhala pakati panu, asadye magazi.
13
Ndipo Aisraele onse kapena alendo okhala pakati pao, amene amapha ku uzimba nyama kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuŵakwirira ndi dothi.
14
“Pajatu moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwake. Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti, ‘Musadye magazi a cholengedwa chilichonse, pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwakemo. Aliyense wodya magazi adzachotsedwa.
15
Munthu aliyense wodya chinthu chofa chokha, kapena chojiwa ndi chilombo, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo pambuyo pake adzakhala woyeretsedwa.
16
Koma akapanda kuchapa zovalazo, kapena akapanda kusamba thupi lonse, adzasenza machimo ake.’ ”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27