bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 15
Leviticus 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 16 →
1
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2
“Muuze Aisraele kuti: Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zimenezo nzonyansa ndithu.
3
Lamulo lake lokhudza za kudziipitsa ndi zonyansa zotuluka ku maliseche a munthu nali: malisechewo akamatulutsabe mafinya, kaya aleka, munthuyo ndi woipitsidwa ndithu.
4
Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonepo, lidzakhala loipitsidwa. Chinthu chilichonse chimene akhalepo, chidzakhala choipitsidwa.
5
Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake, ndipo asambe, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
6
Munthu amene akhale pa chinthu chilichonse chimene wotulutsa mafinyayo adakhalapo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
7
Aliyense wokhudza thupi la munthu wotulutsa mafinyayo, achape zovala zake ndipo asambe, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
8
Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu mnzake amene ali wosaipitsidwa, mnzakeyo achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
9
Ndipo chokhalira chilichonse chapakavalo, chimene munthu wotulutsa mafinya uja adakhalapo, chidzakhala choipitsidwa.
10
Aliyense amene akhudze chinthu chilichonse chimene munthuyo adakhalapo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense amene achinyamule, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
11
Aliyense amene munthu wotulutsa mafinyayo amkhudze asanasambe m'manja, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
12
Chiŵiya chadothi chimene munthu wotulutsa mafinyayo akhudze, achiphwanye, ndipo chiŵiya chilichonse chamtengo achitsuke m'madzi.
13
“Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri a kuyeretsedwa kwake, kenaka achape zovala zake, asambe pa kasupe, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
14
Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, ndi kubwera nazo pamaso pa Chauta pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo azipereke kwa wansembe.
15
Wansembeyo apereke zimenezo, kuti imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ina ikhale nsembe yopsereza. Pamenepo wansembeyo ndiye kuti wachita mwambo wopepesera pamaso pa Chauta machimo a munthu wotulutsa mafinya uja.
16
“Mwamuna akataya pansi mbeu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
17
Chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse pomwe pagwera mbeu yaumunapo achitsuke, koma zikhalabe zoipitsidwa mpaka madzulo.
18
Mwamuna akataya mbeu yake pogona ndi mkazi, onse aŵiriwo asambe, koma akhalabe oipitsidwa mpaka madzulo.
19
“Mkazi akakhala wosamba, ndipo ikakhala nthaŵi yeniyeni yakusamba, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, aliyense amene amkhudze akhala woipitsidwa mpaka madzulo.
20
Ndipo chilichonse chimene mkaziyo agonere ali woipitsidwabe, chikhala choipitsidwa. Chinthu china chilichonse chimene akhalire chikhala choipitsidwa.
21
Aliyense wokhudza bedi la mkaziyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhala woipitsidwa mpaka madzulo.
22
Aliyense wokhudza chimene mkaziyo amakhalapo, achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.
23
Kaya chinthucho chikhale bedi kapena chinthu china chilichonse chimene mkaziyo amakhalapo, munthu akachikhudza, akhala woipitsidwa mpaka madzulo.
24
Mwamuna aliyense akagona ndi mkazi amene akusambabe, mwamunayo akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo bedi lililonse limene mwamunayo agonepo likhala loipitsidwa.
25
“Mkazi akataya magazi masiku ambiri osakhala nthaŵi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira pa nthaŵi yake ya kusamba, masiku onsewo mkaziyo ali wotaya magazi ndi woipitsidwa, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba.
26
Bedi lililonse limene mkaziyo agonepo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, lidzakhala loipitsidwa. Ndipo zonse zimene amakhalirapo zikhala zoipitsidwa, monga momwe zimakhalira zoipitsidwa pamene ali wosamba pa nthaŵi yake.
27
Aliyense wokhudza zimenezi akhala woipitsidwa. Tsono achape zovala zake ndi kusamba thupi lonse, koma akhala woipitsidwabe mpaka madzulo.
28
Atatha matenda a kusamba kwakeko, mkazi aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake akhala woyeretsedwa.
29
Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano.
30
Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo ina ikhale nsembe yopsereza. Akatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Chauta, chifuwa cha matenda ake osamba aja.
31
“Choncho mudzaŵayeretsa Aisraele m'kuipitsidwa kwao, kuti angafe chifukwa chochita tchimo la kudetsa chihema changa, chimene chili pakati pao.”
32
Lamulo limeneli ndi la mwamuna amene ali ndi nthenda yotulutsa mafinya m'thupi mwake, ndiponso la amene ataya pansi mbeu yake yaumuna, imene imamsandutsa woipitsidwa.
33
Lamulo limenelinso ndi la mkazi amene ali ndi matenda osamba. Lamuloli ndi la aliyense, mwamuna kapena mkazi, amene ali ndi nthenda yotulutsa mafinya kumaliseche kwake, ndiponso la mwamuna amene agona ndi mkazi woipitsidwa.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27