bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 16
Leviticus 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 17 →
1
Chauta adalankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana aŵiri a Aroni omwe adaphedwa, atasendera mosayenera pafupi ndi Chauta.
2
Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni mbale wako kuti asamaloŵa nthaŵi iliyonse ku malo opatulika kwambiri, kuseri kwa nsalu yochinga, pamaso pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi lachipangano, kuti angafe, chifukwa Ine ndidzaonekera mu mtambo pamwamba pa chivundikirocho.
3
Koma Aroniyo aziloŵa m'malo opatulikawo motere: azitenga mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.
4
Azivala mwinjiro woyera wabafuta, azivalanso kabudula wabafuta ndi kumangira lamba wabafuta, ndipo avalenso nduŵira yabafuta kumutu. Zimenezi ndi zovala zopatulika. Avale zimenezi atasamba thupi lonse.
5
Aroniyo atenge atonde aŵiri ochokera ku mpingo wa Aisraele, kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa imodzi yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.
6
“Aroni apereke ng'ombe yamphongo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwiniwake, kuti achite mwambo wopepesera machimo ake ndi a banja lake.
7
Tsono atenge mbuzi ziŵiri zija, ndipo aziike pamaso pa Chauta pakhomo pa chihema chamsonkhano.
8
Pompo Aroni achite maere pa mbuzi ziŵirizo, kuti imodzi ikhale ya Chauta, ndipo ina ikhale ya Azazele.
9
Aroniyo abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Chauta, ndipo aipereke kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.
10
Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Azazele, abwere nayo yamoyo pamaso pa Chauta, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo, ndi kuitumiza ku chipululu kwa Azazele.
11
“Aroni apereke ng'ombe yamphongoyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini, ndipo motero achite mwambo wopepesera machimo ake ndi a banja lake. Tsono aphe ng'ombeyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini.
12
Kenaka atenge kambiya kodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Chauta, atape lubani wonunkhira ndi woperapera, manja aŵiri, ndipo aloŵe naye kuseri kwa nsalu yochinga.
13
Atatero, athire lubani pa moto pamaso pa Chauta, kuti utsi wa lubaniwo uphimbe chivundikiro chimene chikhala chili pamwamba pa bokosi lachipangano, kuti angafe.
14
Kenaka atengeko magazi ena a ng'ombeyo, aŵawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha bokosi lachipangano mbali yakuvuma. Ndiponso awazeko magaziwo kasanu ndi kaŵiri ndi chala chake patsogolo pa chivundikirocho.
15
“Tsono Aroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu. Magazi ake aloŵe nawo kuseri kwa nsalu yochinga, ndi kuchita nawo monga momwe adachitira ndi magazi a ng'ombe, pakuwaza magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho.
16
Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera malo oyera chifukwa cha kuipitsidwa kwa Aisraele, ndiponso chifukwa cha kusamvera kwao, ndiye kuti machimo ao onse. Achite chimodzimodzi ndi chihema chamsonkhano chokhala ndi iwo pakati pa machimo ao.
17
Musakhale munthu ndi mmodzi yemwe m'chihema chamsonkhano, pamene Aroni akuloŵa kukachita mwambo wopepesera malo oyera. Musakhale munthu mpaka atamaliza kuchita mwambo wopepesera machimo ake a iye mwini, a banja lake, ndi a mpingo wa Aisraele.
18
Tsono atatuluka Aroniyo apite ku guwa limene lili pamaso pa Chauta ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ng'ombe yamphongo ndiponso a mbuzi, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwalo molizungulira.
19
Awazeko magazi ena pamwamba pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri, kuti alipatule ndi kuliyeretsa pochotsa machimo a Aisraele.
20
“Atamaliza kuchita mwambo wopepesera malo oyera, chihema chamsonkhano pamodzi ndi guwa, wansembeyo apereke mbuzi yamoyo kwa Chauta.
21
Tsono Aroni asanjike manja ake pamutu pa mbuziyo, ndipo aululire pa mbuzi imeneyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwao konse, ndiye kuti machimo ao onse. Machimowo aŵaike pamutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire ku chipululu mbuziyo.
22
Mbuziyo isenze machimo ao onse ndi kumanka nawo ku chipululu. Munthuyo aileke mbuzi imeneyo kuti ipite ku chipululu.
23
“Kenaka Aroni aloŵe m'chihema chamsonkhano, avule zovala zabafuta zimene adavala pokaloŵa m'malo oyera zija, ndipo azisiye komweko.
24
Asambe thupi lonse ku malo oyera, ndipo avale zovala zake. Atuluke kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero, ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini ndi a anthu.
25
Mafuta a nyama ya nsembe yopepesera machimo, aŵatenthere pa guwa.
26
Tsono munthu amene adathamangitsira mbuzi kwa Azazele uja, achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe ku zithando.
27
Ng'ombe ndi mbuzi zoperekera nsembe zopepesera machimo zija, zimene magazi ake adabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera malo oyera, azitulutsire kunja kwa zithando. Zikopa zake, nyama yake ndi ndoŵe yake azitenthe.
28
Munthu amene atenthe zimenezo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, tsono pambuyo pake angathe kuloŵa ku zithando.
29
“Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya kuti mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa tsiku lakhumi la mwezi, muzisala zakudya ndipo musagwire ntchito iliyonse, inu mbadwa, ndiponso mlendo wokhala nao pakati panu.
30
Pajatu pa tsiku limenelo padzakhala mwambo wopepesera machimo anu, kuti machimo anu achotsedwe. Choncho mudzakhala oyera pamaso pa Chauta.
31
Limeneli lidzakhala tsiku lanu lalikulu la sabata lopumula, ndipo mudzasale zakudya. Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya.
32
Wansembe amene wadzozedwa nayeretsedwa kuti akhale mkulu wa ansembe onse m'malo mwa bambo wake, adzachite mwambo wopepesera machimo, atavala zovala zopatulika zabafuta.
33
Adzachite mwambo wopepesera malo oyera. Adzachitenso mwambo wopepesera chihema chamsonkhano ndi guwa, ndiponso mwambo wopepesera machimo a ansembe anzake ndi a mpingo wonse.
34
Limeneli lidzakhala lamulo lanu lamuyaya, kuti muzidzachita mwambo wopepesera machimo onse a Aisraele kamodzi pa chaka.” Tsono Mose adachita monga momwe Chauta adamlamulira.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27