bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 14
Leviticus 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 15 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Lamulo la munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake nali: Abwere naye kwa wansembe.
3
Tsono wansembeyo atuluke kunja kwa mahema, ndipo amuwonetsetse wodwalayo. Ngati wakhateyo apezeke kuti wachira,
4
wansembe alamule anthu kuti wodwala amene akuti ayeretsedweyo, amtengere mbalame zamoyo ziŵiri zimene Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali ndi kanthambi ka hisope.
5
Wansembeyo alamule anthuwo kuti mbalame imodzi aiphere m'mbale yadothi pamwamba pa madzi atsopano.
6
Wansembe atenge mbalame yamoyo ija pamodzi ndi nthambi yamkungudza ija, kansalu kamlangali kaja ndi kachitsamba ka hisope kaja. Zonsezo pamodzi ndi mbalame yamoyoyo, aziviike m'magazi a mbalame yomwe adaiphera m'mbale pamwamba pa madzi atsopano ija.
7
Tsono wansembe awaze magazi kasanu ndi kaŵiri pa munthu amene akuti amuyeretse khateyo. Pamenepo wodwalayo amutche kuti ndi woyeretsedwa, ndipo aiwulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.
8
Wodwala amene wayeretsedwayo, achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe m'madzi; tsono atatero, adzakhala woyeretsedwa. Atatha zonsezo aloŵe chakumahema, koma akhale kunja kwa hema lake masiku asanu ndi aŵiri.
9
Pa tsiku lotsiriza amete tsitsi lake lonse kumutu. Ametenso ndevu zake pamodzi ndi nsidze zomwe, tsitsi lake lonse ndithu. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba, ndipo atatero, adzakhala woyeretsedwa.
10
“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, wodwalayo atenge anaankhosa amphongo aŵiri opanda chilema, atengenso mwanawankhosa mmodzi wamkazi, wa chaka chimodzi, wopanda chilema, ndi chochepereka cha chakudya wosalala wolemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, ndiponso mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
11
Wansembe amene ayeretse wodwalayo, aimiritse munthu woti ayeretsedweyo ali ndi zopereka zake zonse, pamaso pa Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano.
12
Wansembe atengeko mwanawankhosa wamphongo mmodzi ndi kumpereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja. Aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
13
Mwanawankhosayo amuphere pamalo pomwe amaphera nyama yoperekera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, ndiye kuti pa malo oyera aja, pakuti chopereka chopepesera kupalamula ndi chake cha wansembe, monga momwe chimakhalira chopereka chopepesera machimo. Zoperekazo nzoyera kopambana.
14
Wansembe atengeko magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula, ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja.
15
Wansembe atapeko mafuta pang'ono, nkuŵathira m'dzanja lake lakumanzere.
16
Ndipo aviike chala chake cha ku dzanja lamanja m'mafuta amene ali m'dzanja lakumanzerewo, ndi kuwazako mafutawo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri pamaso pa Chauta.
17
Mafuta otsala m'dzanja la wansembeyo, aŵapakeko pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woyeretsedwa uja, ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pamene anali atapaka magazi aja a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.
18
Mafuta otsala m'dzanja la wansembe, aŵathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja. Ndimo m'mene wansembe amchitire munthuyo mwambo wompepesera pamaso pa Chauta.
19
Pambuyo pake wansembe apereke nsembe yopepesera machimo, kuti achite mwambo wompepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Kenaka wansembeyo aphe nyama yoperekera nsembe yopsereza,
20
ndipo aipereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya pa guwa. Atatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wodwalayo, ndipo pamenepo munthuyo adzakhala woyeretsedwa.
21
“Koma munthu wodwalayo akakhala wosauka, kuti alibe zonsezo, apereke mwanawankhosa wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula. Aipereke moweyula manja, kuti achite mwambo wompepesera. Aperekenso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ukhale nsembe yaufa, pamodzi ndi mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
22
Aperekenso njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, monga m'mene angathere. Imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
23
Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pakhomo pa chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta, kuti munthuyo ayeretsedwe.
24
Wansembe atenge mwanawankhosa woperekera nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
25
Tsono nkhosa yoperekera nsembe yopepesera kupalamulayo aiphe. Atengeko magazi ake ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja.
26
Kenaka wansembe athireko mafuta m'dzanja lake lamanzere,
27
awazeko mafutawo kasanu ndi kaŵiri ndi chala cha ku dzanja lamanja pamaso pa Chauta.
28
Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.
29
Mafuta otsala amene ali m'dzanja la wansembe aŵapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo, kuti amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta.
30
Tsono malinga ndi m'mene adapezeramo, apereke njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri.
31
Azipereke ziŵirizo kuti imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo ina ikhale nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka cha chakudya. Atatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu amene ayeretsedweyo pamaso pa Chauta.
32
Limeneli ndilo lamulo la munthu wakhate amene alibe zinthu zoperekera kuyeretsedwa kwake.”
33
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti
34
“Mukakaloŵa m'dziko la Kanani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo ndikakagwetsa ndere m'nyumba iliyonse m'dziko lanulo,
35
mwiniwake nyumbayo adzapite kwa wansembe, akamuuze kuti, ‘Ndikuwona ngati kuti m'nyumba mwanga muli ndere.’
36
Tsono wansembe asanawonetsetse nderezo, alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse m'nyumbamo, kuti zam'nyumbazo angazitchule kuti nzoipitsidwa. Pambuyo pake wansembeyo aloŵe m'nyumbamo kuti aonemo.
37
Ndipo aonetsetse nderezo. Akapezeka kuti zili m'khoma la nyumba, niziwoneka ndi maanga achisipu kapena ofiira, ndipo ikaoneka kuti yaloŵera mpaka m'kati,
38
wansembeyo atuluke m'nyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo aitseke nyumbayo masiku asanu ndi aŵiri.
39
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri wansembeyo abwerenso kudzayang'ana. Nderezo zikakhala kuti zafalikira m'makoma a nyumbayo,
40
wansembeyo alamule kuti anthu agamule miyala m'mene muli nderezo, ndipo akaitaye ku dzala kunja kwa mzinda.
41
Pambuyo pake wansembe auze anthu kuti apale makoma onse m'kati mwa nyumbayo, ndipo dothi akupalalo akalitaye ku dzala kunja kwa mzinda.
42
Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuiloŵetsa m'malo mwa miyala adagumula ija, mwiniwakeyo atengenso dothi lina ndipo amate nyumbayo.
43
“Nderez zikabukanso m'nyumba atagumula kale miyala ija, ndipo ataipala ndi kuimatanso,
44
wansembe apite kukayang'ana. Zikakhala kuti zafalikiranso m'nyumbamo, ndiye kuti ndere zomwe zidafalikira m'nyumbamo ndi zoopsa. Nyumbayo njoipitsidwa.
45
Aigwetse nyumbayo, tsono miyala yake, mitengo yake pamodzi ndi dothi limene adamatira nyumbayo, zonse akazitaye ku dzala kunja kwa mzinda.
46
Ndipo munthu amene waloŵa m'nyumbamo itatsekedwa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
47
Munthu amene wagona m'nyumbamo achape zovala zake, ndipo amene wadyeramo nayenso achape zovala zake.
48
“Koma wansembe akabwera naonetsetsa m'nyumbamo ndi kupeza kuti nthendayo sidafalikiremo, nyumbayo ataimata kale, wansembe aitchule nyumbayo kuti njosaipitsidwa, poti nderezo mulibe.
49
Mwiniwake wa nyumbayo atenge timbalame tiŵiri, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali, ndi kachitsamba ka hisope, kuti zikhale zoyeretsera nyumbayo.
50
Kamodzi mwa timbalame tiŵirito, wansembe akaphere m'mbale yadothi pamwamba pa kasupe.
51
Kenaka atenge nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndi kansalu kamlangali, pamodzi ndi kambalame kamoyo kaja, zonsezo aziviike m'magazi a kambalame kophedwa kaja, ndiponso m'madzi atsopano aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kaŵiri.
52
Atatero, ndiye kuti wansembeyo waiyeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi atsopano, mbalame yamoyo, nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndiponso kansalu kamlangali.
53
Mbalame yamoyo ija aiwulutsire kunja kwa mzinda ku thengo. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”
54
Izi ndizo zimene muyenera kuchita ngati muona kuti
55
mwadetsedwa chifukwa cha khate la mfundu yonyerenyesa, nguwi la pa chovala, ndere za m'nyumba,
56
khate lachithupsa, khate lam'buko ndi khate labanga.
57
Malamulo ameneŵa ngonena za chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa. Atsatidwe pa nthenda zonse za khate.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27