bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 21
Leviticus 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 22 →
1
Chauta adauza Mose kuti, “Ulankhule ndi ansembe, ana a Aroni, ndipo uŵauze kuti: Pasapezeke ndi mmodzi yemwe amene adziipitse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake.
2
Koma angathe kukhudza mai wake, bambo wake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi,
3
kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amakhala pafupi naye, poti chikhalire alibe mwamuna.
4
Wansembe asadziipitse pa imfa ya munthu amene wakwatira naye ku banja limodzi.
5
Ansembe asamete tsitsi kumutu kwao, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zao, kapenanso kudzichekacheka pa thupi.
6
Akhale oyera pamaso pa Ine Mulungu, ndipo asachititse manyazi dzina langa. Amapereka nsembe zotentha pa moto, chakudya cha Mulungu wao, nchifukwa chake azikhala oyera.
7
Asakwatire mkazi wachiwerewere kapena mkazi amene wadziipitsa, ndiponso asakwatire mkazi amene mwamuna wake wamsudzula, pakuti wansembe ndi woyera pamaso pa Mulungu wake.
8
Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa Ine Chauta amene ndimakuyeretsani, ndine woyera.
9
Ndipo mwana wamkazi wa wansembe aliyense akadziipitsa pokhala wachiwerewere, amaipitsa bambo wake. Mwanayo ayenera kumtentha pa moto.
10
“Munthu amene ali mkulu wa ansembe onse, amene adamdzoza pa mutu ndi mafuta, ndiponso amene adapatulidwa pakumuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake, kapena kung'amba zovala zake kusonyeza kuti ali pamaliro.
11
Asakaloŵe kumene kuli munthu wakufa aliyense ndi kudziipitsa, ngakhale mtembo wa bambo wake kapena wa mai wake.
12
Asatuluke m'malo oyera kapena kuipitsa malo oyera a Mulungu wake, pakuti mafuta odzozera a Mulungu wake amene adamdzoza nawo ali pa iye. Ine ndine Chauta.
13
Ndipo akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna,
14
asakwatire mkazi wamasiye kapena mkazi wosudzulidwa, kapenanso mkazi wachiwerewere. Koma akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, amene sanadziŵeko mwamuna,
15
kuti asaloŵetse mtundu wosayera pakati pa ana ake, pakuti Ine ndine Chauta amene ndinamuyeretsa.”
16
Chauta adauza Mose kuti,
17
“Uza Aroni kuti munthu aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, amene ali ndi chilema, asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake.
18
Munthu aliyense wachilema sayenera kusendera pafupi, monga munthu wakhungu kapena wopunduka miyendo, munthu wopunduka nkhope kapena wokhala ndi chiwalo china chachitali dziŵi,
19
munthu wa phazi lopunduka kapena wa dzanja lopunduka,
20
munthu wanundu kapena kafupidolo, munthu wa maso opunduka, munthu wa nthenda yonyerenyesa, kapena wamphere, kapenanso wotswanyika mavalo.
21
Mwa zidzukulu za wansembe Aroni pasadzapezeke munthu ndi mmodzi yemwe wokhala ndi chilema, amene adzapereke nsembe zopsereza kwa Chauta. Popeza kuti ali ndi chilema, sayenera kusendera pafupi ndi guwa kuti akapereke zakudya za Mulungu wake.
22
Koma angathe kudya chakudya choperekedwa kwa Mulungu wake, buledi wopatulika kopambana uja, pamodzi ndi zotsalira zopatulika za nsembe.
23
Koma asadzabwere pafupi ndi nsalu yochinga, kapena kuyandikira guwa, chifukwa ali ndi chilema, kuwopa kuti angadzaipitse malo anga oyera. Pakuti Ine ndine Chauta amene ndidapatula malo amenewo.”
24
Zimenezi ndizo zimene Mose adauza Aroni ndi ana ake aamuna ndiponso Aisraele onse.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27