bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Leviticus 25
Leviticus 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 26 →
1
Chauta adauza Mose pa phiri la Sinai kuti,
2
“Uza Aisraele kuti: Mukadzaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo, nthaka yomwe izikapatulira Chauta chaka chasabata.
3
Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo muzikathenera mitengo yanu yamphesa ndi kuthyola zipatso zake.
4
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri chikhale chaka chopumuza nthaka, chaka chopatulikira Chauta, ndipo musalime minda yanu kapena kuthenera mitengo yanu yamphesa.
5
Musakolole zimene zidamera zokha m'munda mwanu, ndipo musathyole mphesa za mitengo yanu yosathenera. Chaka chimenechi chikhale chopumuza nthaka.
6
Chaka chachisanu ndi chiŵiri chopumulacho chidzakupatsani chakudya chokwanira nonsenu, inuyo ndi akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito anu pamodzi ndi alendo amene akukhala nanu.
7
Ng'ombe zanu ndi nyama za m'dziko mwanu zizidzadya zimene nthaka idzabereka.”
8
“Muziŵerenga masabata asanu ndi aŵiri a zaka, zaka zisanu ndi ziŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri, kuti nyengo ya masabata asanu ndi aŵiri a zakayo ikwanire zaka 49 pamodzi.
9
Tsono pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mulize lipenga mokweza. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo, ndilo tsiku limene mulize lipengalo m'dziko lanu lonse.
10
Mupatule chaka cha 50, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu m'dziko lonselo kwa onse amene ali m'menemo. Kwa inu chaka chimenecho chidzakhale chokondwerera zaka 50, pamene aliyense adzayenera kubwerera pa mtunda wake, ndipo aliyense mwa inu abwerere ku banja lake.
11
Chaka chimenecho cha 50 chikhale chaka chachikondwererodi. Pa chaka chimenechi musabzale kanthu, kapena kukolola mphulumukwa, kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosathenera.
12
Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka 50. Chikhale chaka chopatulika kwa inu ndipo mudye zam'likale.
13
“Chaka chimenechi chokondwerera zaka 50, aliyense abwerere pa mtunda wake.
14
Ukagulitsa mnzako munda, kapena ukagula munda kwa mnzako, pasakhale kuchenjeretsana.
15
Ugule kwa mnzako potsata chiŵerengero cha zaka zimene zidapita kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha 50 chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiŵerengero cha zaka zokolola zimene zatsala.
16
Zaka zikachuluka uwonjezere mtengo, zaka zikachepa uchepetse mtengo, poti akukugulitsani potsata chiŵerengero cha zaka zokolola.
17
Musachenjeretsane, koma muwope Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
18
“Muzimvera malamulo anga ndi kutsata zimene ndikukulamulani, ndipo muzizichitadi. Potero mudzakhala m'dzikomo popanda chokuvutani.
19
Nthaka idzakupatsani zipatso zake, mudzazidya mpaka kukhuta, ndipo mudzakhala m'dzikomo popanda chokuvutani.
20
Mukafunsa kuti: Kodi pa chaka chachisanu ndi chiŵiri tidzadya chiyani, tikapanda kubzala kapena kukolola dzinthu?
21
Ine ndidzalamula kuti mukhale ndi madalitso pa chaka chachisanu ndi chimodzi, kuti nthaka ibale zakudya zokwanira zaka zitatu.
22
Pamene mubzala pa chaka chachisanu ndi chitatu muzidzadya sundwe. Mpaka chaka chachisanu ndi chinai pokolola, mudzidzadyabe sundwe.”
23
“Mtunda usagulitsidwe mpaka muyaya, pakuti dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo ndiponso oyendayenda okhala ndi Ine.
24
M'dziko monse m'mene mudzakhalemo, mudzaloleza anzanu kuwombola mtunda umene unali wao kale.
25
“Mbale wanu akakhala wosauka, nagulitsako gawo lina la mtunda wake, wachibale wake abwere kudzaombola mtunda umene mbale wake wagulitsawo.
26
Munthu akakhala wopanda mbale woti aombole mtundawo, ndipo pambuyo pake munthuyo nkusanduka wolemera, napeza zokwanira kuti auwombole,
27
aŵerenge zaka kuyambira pamene adagulitsa mtundawo. Amubwezere amene adaagulayo ndalama zimene akadayenera kuzipereka mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Atatero, atenge mtunda wake.
28
Koma akapanda kukhala nazo zokwanira zoti aombolere, mtundawo udzakhalebe m'manja mwa amene adagulayo, mpaka pa chaka chokondwerera zaka 50. Pa chaka chimenecho mtundawo udzakhala woombola ndipo ubwerere kwa mwiniwake.
29
“Munthu akagulitsa nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi linga, angathe kuiwombola chisanathe chaka chathunthu ataigulitsa. Adzatha kuiwombola pa nthaŵi yomweyo.
30
Nyumbayo ikapanda kuwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi malingawo idzakhala ya munthu amene adagulayo pa mibadwo yake yonse. Sidzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50.
31
Koma nyumba zam'midzi, zosazingidwa ndi malinga, achite nazo monga momwe amachitira ndi minda yam'dzikomo. Angathe kuziwombola, ndipo zibwezedwe pa chaka chokondwerera zaka 50.
32
Koma kunena za mizinda ya Alevi nyumba zimene zili m'mizinda mwao, Aleviwo angathe kuziwombola nthaŵi iliyonse.
33
Mlevi wina akapanda kuwombola nyumba imene idagulitsidwa mumzinda mwaomoyo aibweze pa chaka chokondwerera zaka 50. Pakuti nyumba zimene zili m'mizinda ya Alevi ndi zao za Aleviwo pakati pa Aisraele.
34
Koma minda ya m'milaga ya mizindayo singagulitsidwe, pakuti mindayo ndi yao mpaka muyaya.”
35
“Mbale wako akakhala wosauka, ndipo sangathe kudzisamala, iweyo umthandize. Uzikhala naye monga ngati mlendo, ndiponso monga ngati munthu wokhala nao kanthaŵi.
36
Usalandire chiwongoladzanja pa ndalama zimene adakongola, kapena kuwonjezerapo zina, koma uziwopa Mulungu wako, ndipo ulole mbale wakoyo kuti akhale nawe.
37
Musakongoze mnzanu ndalama zanu kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumpatsa chakudya kuti mupeze phindu.
38
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito kuti ndikupatseni dziko la Kanani, ndipo kuti ndikhale Mulungu wanu.”
39
“Mbale wako amene ukukhala naye akakhala wosauka nadzigulitsa kwa iwe, usamuyese kapolo wako.
40
Akhale ngati wantchito wako, ndiponso ngati mlendo wako. Azikugwirira ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka 50.
41
Pambuyo pake achoke kwa iwe, pamodzi ndi ana ake omwe, apite ku banja lake, ndi kubwerera ku choloŵa cha makolo ake.
42
Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, asagulitsidwe ngati akapolo.
43
Usaŵalamule mwankhalwe, koma uziwopa Mulungu wako.
44
Kunena za akapolo aamuna kapena aakazi oti muzikhala nawo, mungathe kuŵagula kwa mitundu ina ya anthu okuzungulirani.
45
Mungathenso kuŵagula pakati pa alendo amene akukhala pakati panu ndiponso pakati pa mabanja okhala nanu amene adabadwira m'dziko mwanu. Amenewo angathe kukhala anu.
46
Akapolowo mungathe kuŵasiya m'manja mwa ana anu, inu mutafa, kuti akhale choloŵa chao nthaŵi zonse. Amenewo mungathe kuŵayesa akapolo, koma abale anu Aisraele musaŵalamule mwankhalwe.
47
“Mlendo kapena munthu wodzangokhala nanu akalemera, ndipo mbale wanu wokhala naye pafupi akakhala wosauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendoyo kapena kwa munthu wodzangokhala nanu uja, kapena kwa aliyense wa banja la mlendolo,
48
mbale wanu wodzigulitsayo angathe kuwomboledwa. Wina mwa abale ake angathe kumuwombola,
49
kapena mbale wa bambo wake, kapena mwana wa mbale wa bambo wake, kapena wachibale wa pabanja pake, onseŵa angathe kumuwombola. Koma wodzigulitsayo akalemera, angathe kudziwombola yekha.
50
Aŵerengerane ndi munthu adamgulayo kuyambira chaka chimene adadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Mtengo wa kuwomboledwa kwake ukhale wolingana ndi chiŵerengero cha zakazo. Nthaŵi imene anali ndi mbuyakeyo iŵerengedwe monga ngati nthaŵi ya munthu wantchito.
51
Zaka zikakhala kuti zikadalipo zambiri, pa mtengo umene adalipira pomgula, iye abweze mtengo womuwombolerawo.
52
Zikangotsala zaka zoŵerengeka kuti chifike chaka chokondwerera zaka 50, aŵerengerane ndi mbuye wake, ndipo potsata zaka zotsala mpaka cha 50, abweze ndalama za kuwomboledwa kwake.
53
Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa, chaka ndi chaka. Asamlamule mwankhalwe, iwe ukupenya.
54
Akapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, adzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50, iyeyo pamodzi ndi ana ake.
55
Ndithudi kwa Ine Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27