bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Job 15
Job 15
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 16 →
1
Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2
Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika, Ndi kudzaza mimba yace ndi mphepo ya kum'mawa?
3
Kodi atsutsane ndi mnzace ndi mau akusathandiza? Kapena ndi maneno akusaphindulitsa?
4
Zedi uyesa cabe mantha, Nucepsa cilingiriro pamaso pa Mulungu.
5
Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako, Nusankha lilime la ocenjerera.
6
Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikucitira umboni wakukutsutsa.
7
Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?
8
Kodi unamva uphungu wacinsinsi wa Mulungu? Ndipo unadzikokera nzeru kodi?
9
Udziwa ciani, osacidziwa ife? Uzindikira ciani, cosakhala mwa ife?
10
Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa, Akuposa atate wako masiku ao,
11
Masangalatso a Mulungu akucepera kodi? Kapena uli naco cinsinsi kodi?
12
Mtima wako usonthokeranji nawe? Maso ako aphethira-phethira cifukwa ninji?
13
Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, Ndi kulola mau otere aturuke m'kamwa mwako.
14
Munthu nciani kuti akhale woyera, Wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?
15
Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ace; Ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pace,
16
Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, Wakumwa cosalungama ngati madzi.
17
Ndidzakuonetsa, undimvere; Cimene ndinaciona, ndidzakufotokozera;
18
Cimene adacinena anzeru, Adacilandira kwa makolo ao, osacibisa;
19
Ndiwo amene analandira okha dzikoli, Wosapita mlendo pakati pao;
20
Munthu woipa adzipweteka masiku ace onse, Ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21
M'makutu mwace mumveka zoopsetsa; Pali mtendere amfikira wakumuononga.
22
Sakhulupirira kuti adzaturukamo mumdima, Koma kuti lupanga limlindira;
23
Ayendayenda ndi kufuna cakudya, nati, Ciri kuti? Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima,
24
Nsautso ndi cipsinjo zimcititsa mantha, Zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo;
25
Pakuti amtambasula dzanja lace moyambana ndi Mulungu, Napikisana ndi Wamphamvuyonse.
26
Amthamangira Iye mwaliuma, Ndi zikopa zace zocindikira.
27
Popeza anakuta nkhope yace ndi kunenepa kwace, Nacita mafunyenye a mafuta m'zuuno zace;
28
Adzakhala m'midzi yopasuka, M'nyumba zosakhalamo munthu, Zoti zisandulika muunda.
29
Sadzakhala wolemera, ndi cuma cace sicidzakhalitsa, Ndi zipatso zace sizidzacuruka padziko.
30
Sadzacoka mumdima; Lawi la moto lidzaumitsa nthambi zace; Ndipo adzacoka ndi mpumo wa m'kamwa mwace.
31
Asatame zopanda pace, kudzinyenga nazo; Pakuti zopanda pace zidzakhala combwezera cace.
32
Cidzacitika isanadze nthawi yace; Pakuti nthambi yace siidzaphuka.
33
Adzayoyoka zipatso zace zosapsa ngati mpesa, Nadzathothoka maluwa ace ngati mtengo wazitona.
34
Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala cumba, Ndi moto udzapsereza mahema a olandira cokometsera mlandu.
35
Aima ndi cobvuta, nabala mphulupulu, Ndi m'mimba mwao mukonzeratu cinyengo.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42