bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Job 21
Job 21
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 22 →
1
Pamenepo Yobu anayankha, nati,
2
Mvetsetsani mau anga; Ndi ici cikhale citonthozo canu.
3
Mundilole, ndinene nanenso; Ndipo nditanena ine, sekani.
4
Kodi ine, kudandaula kwanga, ndidandaulira munthu? Ndipo ndilekerenji kupsa mtima?
5
Ndiyang'anireni, nimusumwe, Gwirani pakamwa panu.
6
Ndikangokumbukila ndibvutika mtima, Ndi thupi langa licita nyau nyau.
7
Oipa akhaliranji ndi moyo, Nakalamba, nalemera kwakukuru?
8
Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao, Ndi ana ao pamaso pao,
9
Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha, Ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.
10
Ng'ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika; Ng'ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza.
11
Aturutsa makanda ao ngati gulu, Ndi ana ao amabvinabvina.
12
Ayimbira lingaka ndi zeze, Nakondwera pomveka citoliro.
13
Atsekereza masiku ao ndi zokoma, Natsikira m'kamphindi kumanda.
14
Koma adati kwa Mulungu, Ticokereni; Pakuti sitifuna kudziwa njira zanu.
15
Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire? Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?
16
Taonani, zokoma zao siziri m'dzanja lao; (Koma uphungu wa oipa unditalikira.)
17
Ngati nyali za oipa zizimidwa kawiri kawiri? Ngati tsoka lao liwagwera? Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wace?
18
Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo, Ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?
19
Mukuti, Mulungu asungira ana ace a munthu coipa cace, Ambwezere munthuyo kuti acidziwe.
20
Aone yekha cionongeko cace m'maso mwace, Namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.
21
Pakuti comsamalitsa nyumba yace nciani, atapita iye, Ciwerengo ca miyezi yace citadulidwa pakati?
22
Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru? Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka.
23
Wina akufa, wabiriwiri, Ali cikhalire ndi cipumulire.
24
Mbale zace zidzala ndi mkaka; Ndi wongo wa m'mafupa ace uli momwe.
25
Koma mnzace akufa ali nao mtima wakuwawa, Osalawa cokoma konse.
26
Iwo agona cimodzimodzi kupfumbi, Ndi mphutsi ziwakuta.
27
Taonani, ndidziwa maganizo anu, Ndi ciwembu mundilingirira moipa,
28
Pakuti munena, Iri kuti nyumba ya kalonga? Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti?
29
Simunawafunsa kodi opita m'njira? Ndipo simusamalira zotsimikiza zao?
30
Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka? Naturutsidwa tsiku la mkwiyo?
31
Adzamfotokozera ndani njira yace pamaso pace? Nadzamlipitsa ndani pa ici anacicita?
32
Potsiriza pace adzapita naye kumanda, Nadzadikira pamanda pace,
33
Zibuma za kucigwa zidzamkomera. Adzakoka anthu onse amtsate, Monga anamtsogolera osawerengeka.
34
Potero munditonthozeranji nazo zopanda pace, Popeza m'mayankho mwanu mutsala mabodza okha?
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42