bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Job 38
Job 38
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 39 →
1
Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kabvumvulu, nati,
2
Ndani uyu adetsa uphungu, Ndi mau opanda nzeru?
3
Udzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna; Ndikufunsa, undidziwitse.
4
Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira.
5
Analemba malire ace ndani, papeza udziwa? Anayesapo cingwe cace ndani?
6
Maziko ace anakumbidwa pa ciani? Kapena anaika ndani mwala wace wa pangondya,
7
Muja nyenyezi za m'mawa zinayimba limodzi mokondwera, Ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi cimwemwe?
8
Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko, Muja idakamula ngati kuturuka m'mimba,
9
Muja ndinayesa mtambo cobvala cace, Ndi mdima wa bii nsaru yace yakulunga,
10
Ndi kuilembera malire anga, Ndi kuika mipikizo ndi zitseko,
11
Ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo; Apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?
12
Kodi walamulira m'mawa ciyambire masiku ako, Ndi kudziwitsa mbanda kuca malo ace;
13
Kuti agwire malekezero a dziko lapansi, Nakutumule oipa acokeko?
14
Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa cosindikiza, Ndi zonse zibuka ngati cobvala;
15
Ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone, Ndi dzanja losamulidwa lityoledwa.
16
Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama peni peni?
17
Kodi zipata za imfa zinabvumbulukira iwe? Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa?
18
Kodi unazindikira citando ca dziko lapansi? Fotokozera, ngati ucidziwa conse.
19
Iri kuti njira yomukira pokhala kuunika? Ndi mdima, pokhala pace pali kuti,
20
Kuti upite nao ku malire ace, Kuti uzindikire miseu ya ku nyumba yace?
21
Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo, Ndi masiku ako acuruka kuwerenga kwao.
22
Kodi unalowa m'zosungiramo cipale cofewa? Kapena unapenya zosungiramo matalala,
23
Amene ndiwasungira tsiku la nsautso, Tsiku lakulimbana nkhondo?
24
Njira iri kuti yomukira pogawikana kuunika, Kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa pa dziko lapansi?
25
Ndani anacikumbira mcera cimvula, Kapena njira ya bingu la mphezi,
26
Kubvumbitsa mvula pa dziko lapanda anthu, Ku cipululu kosakhala munthu,
27
Kukhutitsa thengo la kunkhwangwala, Ndi kuphukitsa msipu?
28
Kodi mvula iri naye atate? Kapena wabala ndani madontho amame?
29
Cipale cinaturuka m'inimba ya yani? Ndi cisanu cocokera m'mwamba anacibala ndani?
30
Madzi aundana ngati mwala, Ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi.
31
Kodi ungamange gulu la Nsangwe? Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana?
32
Ungaturutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao? Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ace?
33
Kodi udziwa malemba a kuthambo? Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi?
34
Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo, Kuti madzi ocuruka akukute?
35
Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke, Ndi kunena nawe, Tiri pano?
36
Ndani analonga nzeru m'mitambomo? Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha?
37
Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru, Ndi kutsanulira micenje ya kuthambo ndani,
38
Pokandika pfumbi, Ndi kuundana zibuma pamodzi?
39
Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama? Ndi kukwaniritsa cakudya ca misona,
40
Pamene ibwathama m'ngaka mwao, Nikhala mobisala kulaliramo?
41
Amkonzeratu khungubwi cakudya cace ndani, Pamene ana ace apfuulira kwa Mulungu, Nauluka-uluka osowa cakudya?
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42