bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Job 34
Job 34
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 35 →
1
Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,
2
Tamverani mau anga, inu anzeru; Mundicherere khutu inu akudziwa.
3
Pakuti khutu liyesa mau, Monga m'kamwa mulawa cakudya.
4
Tidzisankhire coyeneraco, Tidziwe mwa tokha cokomaco.
5
Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama, Ndipo Mulungu wandicotsera coyenera ine.
6
Kodi ndidzinamizire? Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwa.
7
Wakunga Yobu ndani, Wakumwa mwano ngati madzi?
8
Wakutsagana nao ocita mphulupulu, Nayendayenda nao anthu oipa.
9
Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako Kubvomerezana naye Mulu ngu.
10
Cifukwa cace mundimvere ine, eni nzeru inu, Nkutali ndi Mulungu kucita coipa, Ndi Wamphamvuyonse kucita cosalungama.
11
Pakuti ambwezera munthu monga mwa nchito yace, Napezetsa munthu ali yense monga mwa mayendedwe ace.
12
Ndithu zoonadi, Mulungu sangacite coipa, Ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.
13
Anamuikiza dziko lapansi ndani? Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani?
14
Akadzikumbukila yekha mumtima mwace, Akadzisonkhanitsira yekha mzimu wace ndi mpweya wace,
15
Zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi, Ndi munthu adzabwerera kupfumbi.
16
Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ici, Cherera khutu kunena kwanga.
17
Kodi munthu woipidwa naco ciweruzo adzalamulira? Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa?
18
Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pace iwe, Kapena kwa akalonga, Oipa inu?
19
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, Wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo nchito ya manja ace.
20
M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku, Anthu agwedezeka, napita, Amphamvu acotsedwa opanda dzanja lakuwacotsa.
21
Pakuti maso ace ali pa njira ya munthu ali yense, Napenya moponda mwace monse.
22
Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa, Kuti ocita zopanda pace abisaleko.
23
Pakuti Mulungu alibe cifukwa ca kulingiriranso za munthu, Kuti afike kwa. Iye kudzaweruzidwa.
24
Aphwanya eni mphamvu osaturutsa kubwalo mlandu wao, Naika ena m'malo mwao.
25
Pakuti asamalira nchito zao, Nawagubuduza usiku kuti aphwanyike.
26
Awakantha ngati oipa, Poyera pamaso pa anthu.
27
Popeza anapambuka, naleka kumtsata, Osasamalira njira zace ziri zonse.
28
M'mwemo anafikitsa kwa Iye kupfuula kwa osauka; Ndipo anamva Iye kupfuula kwa ozunzika.
29
Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yace adzampenyerera ndani? Cikacitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, ncimodzimodzi;
30
Kuti munthu wonyoza Mulungu asacite ufumu, Ndi anthu asakodwe mumsampha,
31
Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu, Ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwa?
32
Cimene sindiciona mundilangize ndi Inu, Ngati ndacita cosalungama sindidzabwerezanso.
33
Kodi cilango ca Mulungu cikhale monga mucifuna inu, pakuti mucikana? Musankhe ndi inu, ine ai; M'mwemo monga mudziwa, nenani.
34
Anthu ozindikira adzanena nane, Inde anthu anzeru onse akundimva adzati,
35
Yobu alankhula wopanda kudziwa, Ndi mau ace alibe nzeru.
36
Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha, Cifukwa ca kuyankha kwace monga anthu amphulupulu,
37
Pakuti pa kucimwa kwace aonjeza kupikisana ndi Mulungu, Asansa manja pakati pa ife, Nacurukitsa maneno ace pa Mulungu.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42