bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Job 28
Job 28
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 29 →
1
Koma kuli mtapo wa siliva, Ndi malo a golidi amene amuyenga.
2
Citsulo acitenga m'nthaka, Ndi mkuwa ausungunula kumwala.
3
Munthu athawitsa mdima, Nafunafuna mpaka malekezero onse, Miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa.
4
Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu; Aiwalika ndi phazi lopitapo; Apacikika kutali ndi anthu, nalendewa-lendewa.
5
Kunena za nthaka, kucokera momwemo mumaturuka cakudya, Ndi m'munsi mwace musandulizika ngati ndi moto.
6
Miyala yace ndiyo malo a safiro, Ndipo iri nalo pfumbi lagolidi.
7
Njira imeneyi palibe ciombankhanga ciidziwa; Lingakhale diso la kabawi losapenyapo.
8
Nyama zodzikuza sizinapondapo, Ngakhale mkango waukali sunapitapo.
9
Munthu atambasulira dzanja lace kumwala; Agubuduza mapiri kuyambira kumizu.
10
Asema njira pakati pa matanthwe, Ndi diso lace liona ciri conse ca mtengo wace.
11
Atseka mitsinje ingadonthe; Naturutsira poyera cobisikaci.
12
Koma nzeru, idzapezeka kuti? Ndi luntha, malo ace ali kuti?
13
Munthu sadziwa mtengo wace; Ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.
14
Pozama pakuti, Mwa ine mulibe; Ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe.
15
Silipezeka ndi golidi, Sayesapo siliva mtengo wace.
16
Sailinganiza ndi golidi wa Ofiri, Ndi sohamu wa mtengo wace wapatali kapena safiro.
17
Golidi ndi krustalo sizilingana nayo; Ndi kusinthana kwace, siisinthanika ndi zisambiro za golidi woyengetsa.
18
Korali kapena ngale sizikumbukikapo. Mtengo wace wa nzeru uposa wa korali wofiira.
19
Topazi wa Kusi sufanana nayo, Sailinganiza ndi golidi wolongosoka.
20
Koma nzeru ifuma kuti? Ndi luntha, pokhala pace pali kuti?
21
Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse, Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,
22
Cionongeko ndi Imfa zikuti, Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.
23
Mulungu ndiye: azindikira njira yace, Ndiye adziwa pokhala pace.
24
Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi, Naona pansi pa thambo ponse;
25
Pamene anaikira mphepo muyeso wace, Nayesera madzi miyeso;
26
Pakucitira mvula lamulo, Ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;
27
Pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera; Anaikonza, naisanthula.
28
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; Ndi kupatukana naco coipa ndiko luntha.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42