bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Job 6
Job 6
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 7 →
1
Koma Yobu anayankha, nati,
2
Mwenzi atayesa bwino cisoni canga, Ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!
3
Pakuti zikadalemera tsopano koposa mcenga wa kunyanja; Cifukwa cace mau anga ndasonthokera kunena.
4
Pakuti mibvi ya Wamphamvuyonse yandilowa, Mzimu wanga uumwa ulembe wace; Zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
5
Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu? Ilira kodi ng'ombe pa cakudya cace?
6
Kodi cinthu cosakolera cidyeka copanda mcere? Coyera ca dzira cikolera kodi?
7
Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza Zikunga cakudya cosakolera kwa ine.
8
Ha! ndikadakhala naco cimene ndicipempha, Mulungu akadandipatsa cimene ndicilira!
9
Cimkomere Mulungu kundiphwanya, Alole dzanja lace lindilikhel
10
Pamenepo ndidzasangalala, Ndidzakondwera naco cowawa cosandileka; Pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo.
11
Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze? Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?
12
Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala? Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?
13
Mulibe thandizo mwa ine ndekha; cipulumutso candithawa.
14
Iye amene akadakomoka, bwenzi lace ayenera kumcitira cifundo; Angaleke kuopa Wamphamvuyonse.
15
Abale anga anacita monyenga ngati kamtsinje, Ngati madzi a timitsinje akupitirira.
16
Amada cifukwa ca madzi oundana. M'menemo cipale cofewa cibisika;
17
Atafikira mafundi, mitsinje iuma; Kukatentha, imwerera m'malo mwao.
18
Aulendo akutsata njira yao apambukapo, Akwerera poti se, natayika.
19
Aulendo a ku Tema anapenyerera, Makamu a ku Seba anaiyembekezera.
20
Anazimidwa popeza adaikhulupirira; Anafikako, nathedwa nzeru.
21
Pakuti tsopano mukhala mamwemo; Muona coopsa, mucitapo mantha.
22
Ngati ndinati, Mundipatse? Kapena, Muperekeko kwa ine cuma canu?
23
Kapena, Mundilanditse m'dzanja la mdani? Kapena, Mundiombole m'dzanja la oopsa?
24
Mundilangize, ndipo ndidzakhala cete ine; Mundizindikiritse umo ndinalakwira.
25
Mau oongoka si ndiwo amphamvu? Koma kudzudzula kwanu mudzudzula ciani?
26
Kodi muyesa kudzudzula mau? Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.
27
Indetu, mugwetsera wamasiye msampha, Mumkumbira bwenzi lanu mbuna.
28
Koma tsopano balindani, mundipenyerere; Ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.
29
Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu; Inde, bwereraninso, mlandu wanga ngwolungama.
30
Kodi pali cosalungama palilime panga? Ngati sindizindikira zopanda pace m'kamwa mwanga?
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42