bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 10
1 Chronicles 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 11 →
1
Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraele adathaŵa Afilisti; ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa.
2
Afilistiwo adapanikiza Saulo ndi ana ake, ndipo adapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa ana a Saulo.
3
Nkhondo idampanikiza kwambiri Sauloyo, ndipo anthu amauta adampeza namlasa koopsa.
4
Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo.
5
Wonyamula zida uja ataona kuti Sauloyo wafa, nayenso adadzigwetsa pa lupanga lake, nkufa.
6
Umu ndimo m'mene adafera Saulo, iyeyo ndi ana ake atatu, pamodzi ndi banja lake lonse.
7
Aisraele onse amene anali ku chigwa, ataona kuti gulu lankhondo lathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake aphedwa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo.
8
M'maŵa mwake, Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake pa phiri la Gilibowa.
9
Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe.
10
Tsono adaika zida za Sauloyo m'nyumba ya milungu yao, ndipo adakhomerera mutu wakewo ku nyumba ya Dagoni, mulungu wao.
11
Koma anthu a ku Yabesi-Giliyadi atamva zonse zimene Afilisti adaamchita Saulo,
12
amuna onse olimba mtima adanyamuka kukatenga mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake kubwera nayo ku Yabesi. Adakwirira mafupa aowo patsinde pa mtengo wa thundu ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri.
13
Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu,
14
ndipo sankafuna kuti Chauta amutsogolere. Nchifukwa chake Chautayo adamupha napereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29