bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 14
1 Chronicles 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 15 →
1
Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri odziŵa kumanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akammangire nyumba Davideyo.
2
Motero Davide adazindikira kuti Chauta wamkhazikitsa kuti akhale mfumu yolamulira Aisraele, ndiponso kuti wakweza ufumu wake chifukwa cha Aisraele, anthu ake.
3
Davide adakwatira akazi ena ku Yerusalemu, ndipo adabereka ana enanso aamuna ndi aakazi.
4
Ana amene Davide adaberekera ku Yerusalemu ndi aŵa: Samuwa, Sobabu, Natani, Solomoni,
5
Ibara, Elisuwa, Elipeleti,
6
Noga, Nefegi, Yafiya,
7
Elisama, Beeliyada, ndi Elifeleti.
8
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko lonse la Aisraele, adapita onse kukamfunafuna. Davide atamva zimenezo, adatuluka kukamenyana nawo nkhondo.
9
Tsono Afilisti adafika nayamba kufunkha m'chigwa cha Refaimu.
10
Pamenepo Davide adafunsa kwa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nawo nkhondo Afilistiwo? Kodi mudzaŵapereka m'manja mwanga?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita. Ndidzaŵaperekadi m'manja mwako.”
11
Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ndi dzanja langa Mulungu waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.
12
Afilistiwo adasiya milungu yao kumeneko ndipo Davide adalamula kuti aiyatse moto, ndipo adaitenthadi.
13
Nthaŵi ina Afilistiwo adabweranso naloŵa m'chigwa mom'muja.
14
Davide atafunsanso Mulungu, Mulungu adamuuza kuti, “Usati uŵalondole. Uchite moŵazungulira, uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija.
15
Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo utuluke kukamenyana nawo. Pakuti Mulungu wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.”
16
Davide adachitadi monga momwe Mulungu adaamlamulira, ndipo adagonjetsa gulu lankhondo la Afilistilo kuyambira ku Gibiyoni mpaka ku Gezere.
17
Ndipo mbiri ya Davide idawanda ku maiko onse, ndipo Ambuye adachititsa mantha anthu a mitundu yonse kuti azimuwopa Davideyo.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29