bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 11
1 Chronicles 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 12 →
1
Aisraele onse adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi.
2
Kale, ngakhale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo, nkumabwera nawonso. Ndipo Chauta, Mulungu wanu, adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya anthu anga Aisraele.’ ”
3
Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse, potsata mau a Chauta ochokera m'kamwa mwa Samuele.
4
Pambuyo pake Davide pamodzi ndi Aisraele onse adapita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, ndiye kuti Yebusi, kumene kunkakhala Ayebusi nzika za dzikolo.
5
Ayebusiwo adauza Davide kuti, “Kuno sudzaloŵako ai.” Komabe Davideyo adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide.
6
Davide anali atanena kuti, “Aliyense amene ayambe kukantha Ayebusi, adzakhala mkulu wolamulira gulu lankhondo.” Tsono Yowabu mwana wa Zeruya ndiye adayamba kupitako, motero adakhala mtsogoleri wankhondo woyamba.
7
Popeza kuti Davide ankakhala m'lingamo, lingalo linkatchedwa Mzinda wa Davide.
8
Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku linga la Milo mpaka m'kati mwake. Yowabu ndiye adakonza mbali ina ya mzindawo.
9
Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta wamphamvuzonse anali naye.
10
Tsono aŵa ndiwo atsogoleri a nkhondo a Davide, amene ankamthandiza pamodzi ndi Aisraele onse, kuti akhale mfumu potsata mau a Chauta onena za Israele.
11
Mndandanda wa anthu amphamvu a Davide ndi uwu: Yasobeamu Muhakimoni ndiye amene anali wamkulu mwa atsogoleri a anthu aja. Tsiku lina adapha ndi mkondo wake anthu 300 nthaŵi imodzi.
12
Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, Mwahohi.
13
Iyeyo anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu pamene Afilisti adaasonkhana kumeneko kuti amenyane naye nkhondo. Kumeneko kudaali munda wodzaza ndi barele ndipo anthu a Davide adathaŵa kuwopa Afilistiwo.
14
Koma Eleazara ndi anzake adakaima m'kati mwa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo. Motero Chauta adaŵapulumutsa ndi kuŵapambanitsa kwambiri.
15
Tsiku lina atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja adatsikira ku thanthwe mpaka kwa Davide ku phanga la Adulamu. Kufupi nkumeneko ankhondo a Afilisti anali atamanga zithando zankhondo ku chigwa cha Refaimu.
16
Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kanali ku Betelehemu.
17
Ndiye Davide atamva ludzu kwambiri adati, “Ha, wina akadandipatsa madzi a m'chitsime chimene chili pafupi ndi chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!”
18
Pomwepo anthu atatu amphamvu aja adapita akubzola zithando za Afilisti, nakatunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo, adangoŵathira pansi kuŵapereka kwa Chauta.
19
Ndipo adati, “Ndithu, pali Mulungu, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao pa minga, pang'ono akadataya moyo wao pokabwera nawo madzi ameneŵa.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja.
20
Abisai, mbale wake wa Yowabu, anali mkulu wa atsogoleri makumi atatu aja. Ndiye adapha ndi mkondo wake anthu 300, nakhala wotchuka ngati anthu atatu aja.
21
Iye anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja.
22
Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima, amene ankachita ntchito zazikulu. Iyeyo adapha ngwazi ziŵiri za ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.
23
Adaphanso Mwejipito wina wamkulu thupi, kutalika kwake ngati mamita aŵiri ndi theka. Mwejipitoyo anali ndi mkondo m'manja wofanafana ndi mtanda wa munthu woomba nsalu. Koma Benaya adapita kwa iyeyo atatenga ndodo, nalanda mkondowo kumanja kwa Mwejipito uja, nkumupha ndi mkondo wake womwewo.
24
Zimenezi ndizo adachita Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo adatchuka ngati atsogoleri makumi atatu amphamvu aja.
25
Iyeyu anali womveka mwa atsogoleri makumi atatuwo, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza.
26
Anthu amphamvu a m'magulu ankhondowo anali aŵa: Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
27
Samoti wa ku Harodi, Helezi Mpeloni,
28
Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti,
29
Sibekai Muhusati, Ilai Mwahohi,
30
Maharai wa ku Netofa, Heledi mwana wa Baana wa ku Netofa,
31
Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea, Mbenjamini. Panalinso Benaya wa ku Piratoni,
32
Hurai wa ku mitsinje ya ku Gaasi, Abiyele Mwarabati,
33
Azimaveti wa ku Baharumi, Eliyaba wa ku Saaliboni,
34
Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Muharari,
35
Ahiyamu mwana wa Sakara Muharari, Elifala mwana wa Uri,
36
Hefere Mmekerati, Ahiya Mpeloni,
37
Heziro wa ku Karimele, Naarai mwana wa Ezibai,
38
Yowele mbale wake wa Natani, Mibara mwana wa Hagiri,
39
Zeloki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,
40
Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,
41
Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai,
42
Adina mwana wa Siza Mrubeni, mtsogoleri wa Arubeni, ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,
43
Hanani mwana wa Maaka, ndiponso Yosafati Mmitini,
44
Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyele ana a Hotamu Mweroeri,
45
Yediyaele mwana wa Simiri, ndi Yoha mbale wake Mtizi,
46
Eliyele Mmahavi, ndiponso Yeribai ndi Yosaviya, ana a Elinamu, kudzanso Itima Mmowabu,
47
Eliyele, Obede ndi Yaasiyele Mmezobai.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29