bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 2
1 Chronicles 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 3 →
1
Ana a Israele naŵa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
2
Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi, ndi Asere.
3
Ana a Yuda naŵa: Eri, Onani, ndi Sela. Ana atatu ameneŵa adamubalira ndi Batisuwa mkazi wa ku Kanani. Tsono Eri mwana wa Yuda anali wa makhalidwe oipa, choncho Chauta adamupha.
4
Mpongozi wake Tamara nayenso adamubalira Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
5
Ana a Perezi naŵa: Hezironi ndi Hamuli.
6
Ana a Zera naŵa: Zimiri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse pamodzi analipo asanu.
7
Ana a Karimi naŵa: Akara amene adaavuta Aisraele. Iyeyo adaaba zinthu zoyenera kuziwononga.
8
Mwana wa Etani anali Azariya.
9
Ana amene adabereka Hezironi naŵa: Yerameele, Ramu ndi Kelebe.
10
Ramu adabereka Aminadabu, Aminadabu adabereka Nasoni, mkulu wa fuko la Yuda.
11
Nasoni adabereka Salimoni, Salimoni adabereka Bowazi,
12
Bowazi adabereka Obede, Obede adabereka Yese.
13
Yese adabereka Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, wachitatu Simea,
14
wachinai Netanele, wachisanu Radai,
15
wachisanu ndi chimodzi Ozemu, wachisanu ndi chiŵiri Davide.
16
Alongo ao anali Zeruya ndi Abigaile. Ana a Zeruya naŵa: Abisai, Yowabu ndi Asahele, onse pamodzi atatu.
17
Abigaile adabala Amasa ndipo bambo wake wa Amasa anali Yetere Mwismaele.
18
Kalebe mwana wa Hezironi anali nawo ana omubalira mkazi wake Azuba ndiponso Yerioti. Ana amene adabala mkaziyo naŵa: Yesere, Sobabu ndi Aridoni.
19
Atafa Azuba, Kalebe adakwatira Efrati amene adamubalira Huri.
20
Huri adabereka Uri, ndipo Uri adabereka Bezalele.
21
Pambuyo pake Hezironi, ali wa zaka 60, adakakwatira mwana wa Makiri bambo wake wa Giliyadi. Ndipo mkaziyo adamubalira Segubu.
22
Segubu adabereka Yairi amene anali ndi mizinda 23 m'dziko la Giliyadi.
23
Koma anthu a ku Gesuri ndi a ku Aramu adaŵalanda Havoti-Yairi, Kenati pamodzi ndi midzi yake yomwe, yonse pamodzi inalipo midzi 60. Onseŵa anali adzukulu a Makiri, bambo wake wa Giliyadi.
24
Atafa Hezironi, Kalebe adakwatira Efurata, mkazi wa bambo wake Hezironi. Ndipo mkaziyo adamubalira Asuri, bambo wake wa Tekowa.
25
Ana a Yerameele, mwana wachisamba wa Hezironi, naŵa: Ramu mwana wachisamba, Buna, Oreni, Ozemu, ndi Ahiya.
26
Yerameele analinso ndi mkazi wina dzina lake Atara. Mkaziyu adabala Onamu.
27
Ana a Ramu, mwana wachisamba wa Yerameele, anali Maazi, Yamini ndi Ekeri.
28
Ana a Onamu anali Samai ndi Yada. Ana a Samai anali Nadabu ndi Abisuri.
29
Mkazi wake wa Abisuri anali Abihaili, ndipo mkaziyo adamubalira Abani ndi Molidi.
30
Ana a Nadabu anali Seledi ndi Apaimu. Seledi adafa opanda ana.
31
Mwana wa Apaimu anali Isi. Mwana wa Isi anali Sesani. Mwana wa Sesani anali Alai.
32
Ana a Yada mbale wa Samai anali Yetere ndi Yonatani. Yetere adafa opanda ana.
33
Ana a Yonatani anali Peleti ndi Zaza. Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Yerameele.
34
Sesani analibe ana aamuna, anali ndi ana aakazi okhaokha. Koma anali ndi kapolo wake wa ku Ejipito, dzina lake Yara.
35
Motero Sesani adakwatitsa mwana wake wamkazi kwa Yara kapolo wake uja. Ndipo mkaziyo adamubalira Attai.
36
Attai adabereka Natani, Natani adabereka Zabadi.
37
Zabadi adabereka Efilala, Efilala adabereka Obede.
38
Obede adabereka Yehu, Yehu adabereka Azariya.
39
Azariya adabereka Helezi, Helezi adabereka Eleasa.
40
Eleasa adabereka Sisimai, Sisimai adabereka Salumu.
41
Salumu adabereka Yekamiya, ndipo Yekamiya adabereka Elisama.
42
Ana a Kalebe mbale wa Yerameele naŵa: Maresa, mwana wake wachisamba, bambo wake wa Zifi. Mwana wa Maresa anali Hebroni.
43
Ana a Hebroni naŵa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
44
Sema adabereka Rahama, bambo wake wa Yorikeamu ndipo Rekemu adabereka Samai.
45
Mwana wa Samai anali Maoni. Tsono Maoni adabereka Betezuri.
46
Nayenso Efa, mzikazi wa Kalebe, adamubalira Harani, Moza ndi Gazezi. Harani adabereka Gazezi.
47
Ana a Yadai naŵa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efa ndi Saafi.
48
Maaka, mzikazi wa Kalebe, adamubalira Sebere ndi Tirihana.
49
Mkaziyo adabalanso Saafi, bambo wake wa Madimana, ndi Seva bambo wake wa Makibena ndiponso bambo wa Gibea. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa.
50
Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata, naŵa: Sobala amene adabereka Kiriyati-Yearimu,
51
Salima amene adabereka Betelehemu, ndiponso Harefi amene adabereka Betegadere.
52
Sobala bambo wake wa Kiriyati-Yearimu adaberekanso ana ena, naŵa: Harowe, ndiye kuti theka la Amenuwoti.
53
Mabanja a Kiriyati-Yearimu naŵa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Ameneŵa ndiwo makolo a Azorati ndi Aesitaoli.
54
Ana a Salima naŵa: Betelehemu, Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu ndi hafu la Amanahati, ndiponso Azori.
55
Mabanjanso a alembi amene ankakhala ku Yabesi naŵa: Atirati, Asimeati ndi Asukati. Ameneŵa ndiwo Akeni amene adachokera kwa Hamati, kholo la banja la Rekabu.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29