bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 7
1 Chronicles 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 8 →
1
Ana a Isakara naŵa: Tola, Puwa, Yasubu, ndi Simironi, anai.
2
Ana a Tola naŵa: Uzi, Refaya, Yeriyele, Yamai, Ibisamu, ndi Semuele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ndiye kuti a banja la Tola. Onsewo anali ankhondo amphamvu pa mibadwo yao. Chiŵerengero chao pa nthaŵi ya Davide chinali 22,600.
3
Mwana wa Uzi anali Iziraya. Ana a Iziraya naŵa: Mikaele, Obadiya, Yowele ndiponso Isiya. Asanu onsewo anali atsogoleri.
4
Pamodzi ndi iwowo, malinga ndi mibadwo yao ndi mabanja a makolo ao, panali anthu ankhondo 36,000, pakuti anali ndi akazi ambiri ndiponso ana ambiri.
5
Abale ao a mabanja onse a Isakara analipo onse pamodzi 87,000, ankhondo amphamvu, olembedwa potsata mibadwo yao.
6
Ana a Benjamini naŵa: Bela, Bekere ndiponso Yediyaele, atatu pamodzi.
7
Ana a Bela naŵa: Eziboni, Uzi, Uziyele, Yerimoti ndi Iri, asanu, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ankhondo amphamvu. Ndipo chiŵerengero chao potsata mibadwo yao chinali 22,034.
8
Ana a Bekere naŵa: Zimira, Yowasi, Eliyezere, Eliyoenai, Omuri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onseŵa anali ana a Bekere.
9
Ndipo kulembedwa kwao potsata kubadwa kwao ndiponso malinga ndi mibadwo yao, pokhala atsogoleri a mabanja a makolo ao, analipo 20,200, ankhondo amphamvu okhaokha.
10
Mwana wa Yediyaele anali Bilihani. Ana a Bilihani naŵa: Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara.
11
Onseŵa anali ana a Yediyaele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ankhondo amphamvu 17,200, anthu okonzekera kumenya nkhondo.
12
Supimu ndi Hupimu anali ana a Iri, ndipo analinso a fuko ili. Husimu anali mwana wa Dan.
13
Ana a Nafutali naŵa: Yaziyele, Guni, Yezere ndi Salumu. Anali adzukulu a Biliha.
14
Ana a Manase naŵa: Asiriele amene adamuberekera mzikazi wake wa ku Aramu. Mkazi yemweyo adabalanso Makiri, bambo wake wa Giliyadi.
15
Makiri adapezera Hupimu ndi Supimu akazi, wina wake wina wake. Mlongo wake anali Maaka. Dzina la wachiŵiriyo linali Zelofehadi. Ndipo Zelofehadiyo anali ndi ana aakazi okhaokha.
16
Tsono Maaka, mkazi wa Makiri, adabala mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Peresi. Mbale wake anali Seresi, ndipo ana ake aamuna anali Ulamu ndi Rakemu.
17
Mwana wa Ulamu anali Bedani. Ameneŵa anali ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase.
18
Mlongo wake Hamoleketi adabala Isihodi, Abiyezere ndi Mala.
19
Ana a Semida naŵa: Ahiyani, Sekemu, Liki ndi Aniyamu.
20
Zidzukulu za Efuremu nazi: Sutela, Beredi, Tahati, Eleada, Tahati,
21
Zabadi, Sutela. Efuremu anali nawonso ana aŵiri: Ezere ndi Eleadi amene adaphedwa ndi anthu a ku Gati eni ake a dzikolo, chifukwa chakuti adabwera kudzalanda ng'ombe zao.
22
Ndiye Efuremu bambo wao adalira maliro masiku ambiri, choncho abale ake adadza kudzamtonthoza.
23
Pambuyo pake Efuremu adakaloŵa kwa mkazi wake, ndipo mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana. Mwanayo adamutcha dzina loti Beriya, chifukwa chakuti tsoka lidaagwera banja lake.
24
Mwana wake wamkazi anali Seera, amene adamanga mzinda wa Betehoroni wakunsi ndi Betehoroni wakumtunda, kudzanso Uzeniseera.
25
Mwana wina wa Efuremu anali Refa, amene zidzukulu zake zinali izi: Resefi, Tela, Tahani,
26
Ladani, Amihudi, Elisama,
27
Nuni ndi Yoswa.
28
Maiko ao kumene ankakhala anali Betele pamodzi ndi midzi yake. Chakuvuma kunali Naarani, chakuzambwe kunali Gezere pamodzi ndi midzi yake, Sekemu pamodzi ndi midzi yake, ndiponso Aya pamodzi ndi midzi yake.
29
Zidzukulu za Manase zinkalamulira mizinda iyi: Beteseani pamodzi ndi midzi yake, Tanaki pamodzi ndi midzi yake, Megido pamodzi ndi midzi yake, Dori pamodzi ndi midzi yake. Kumeneko ndiko kumene kunkakhala ana a Yosefe mwana wa Israele.
30
Ana a Asere naŵa: Imina, Isiva, Isivi, Beriya ndiponso mlongo wao Sera.
31
Ana a Beriya naŵa: Hebere ndi Malakiyele, amene adamanga Birizaiti.
32
Hebere adabereka Yafileti, Somere, Hotamu ndiponso mlongo wao Suwa.
33
Ana a Yafileti naŵa: Pasaki, Bimala ndi Asivati. Ameneŵa ndiwo ana a Yafileti.
34
Ana a Somere mbale wake naŵa: Roga, Yehuba ndiponso Aramu.
35
Ana a Helemu mbale wake naŵa: Zofa, Imina, Selesi ndi Amala.
36
Ana a Zofa naŵa: Suwa, Harenefere, Suwala, Beri, Imira,
37
Bezere, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Beera.
38
Ana a Yetere naŵa: Yefune, Pisipa ndi Ara.
39
Ana a Ula naŵa: Ara, Haniyele ndi Riziya.
40
Anthu onseŵa anali zidzukulu za Asere. Anali atsogoleri a mabanja a makolo ao, anthu omveka, ankhondo amphamvu, akuluakulu pakati pa akalonga. Chiŵerengero chao cholembedwa m'buku, potsata mibadwo yao yoyenera ntchito yankhondo, chinali 26,000.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29