bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 18
1 Chronicles 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 19 →
1
Pambuyo pake, Davide adathira nkhondo Afilisti naŵagonjetsa. Ndipo adalanda Gati pamodzi ndi midzi yake yomwe kwa Afilistiwo.
2
Adagonjetsanso Amowabu, ndipo Amowabuwo adasanduka otumikira Davide, ndipo ankakhoma msonkho kwa iye.
3
Ku Hamati Davideyo adagonjetsanso Hadadezere mfumu ya ku Zoba, pamene inkapita kukakhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.
4
Ndipo Davide adalanda Hadadezere magaleta 1,000, anthu a pa akavalo 7,000, ndi asilikali apansi 20,000. Atatero, Davide adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okoka magaleta, koma adasungako akavalo okwanira magaleta 100.
5
Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000.
6
Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita.
7
Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu.
8
Kuchokera ku Tibati ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri. Ndi mkuŵa umenewo Solomoni adapanga chimbiya ndi nsanamira ndiponso ziŵiya zina za ku Nyumba ya Chauta.
9
Pamene Tou mfumu ya ku Hamati adamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse la ankhondo la Hadadezere, mfumu ya ku Zoba,
10
adatuma mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Tou kaŵirikaŵiri. Tsono adamtumizira Davide mphatso zamitundumitundu zopangidwa ndi golide, siliva ndi mkuŵa.
11
Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta, pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina, ndiye kuti anthu a ku Edomu, a ku Mowabu, kwa Aamoni, kwa Afilisti, ndi kwa Aamaleke.
12
Pa nthaŵi imeneyi Abisai, mwana wa Zeruya, adapha Aedomu okwanira 18,000 ku chigwa cha Mchere.
13
Tsono Davide adaika ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu, ndipo Aedomu onse adasanduka anthu otumikira Davideyo. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
14
Motero Davide adalamulira dziko lonse la Israele, ndipo ankayendetsa zonse mwachilungamo ndi mosakondera.
15
Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri.
16
Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Savisa anali mlembi.
17
Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali nduna zazikulu pa ntchito zotumikira mfumu.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29