bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 28
1 Chronicles 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 29 →
1
Davide adasonkhanitsa ku Yerusalemu akuluakulu onse a Aisraele, ndiye kuti akuluakulu a mafuko, akapitao a magulu amene ankatumikira mfumu, atsogoleri a ankhondo zikwi, atsogoleri a ankhondo mazana, akulu osunga katundu yense ndi ng'ombe za mfumu ndi za ana ake, pamodzi ndi akulu oyang'anira nyumba ya mfumu, anthu amphamvu, ndiponso ngwazi zonse zankhondo.
2
Tsono mfumu Davide adaimirira nati, “Tamverani abale anga ndiponso anthu anga. Ine ndinkaganiza zomanga nyumba yokhalamo Bokosi lachipangano la Chauta, limene lili ngati malo opondapo mapazi Mulungu wathu. Ndipo ndidakonza zomangira nyumbayo.
3
Koma Mulungu adandiwuza kuti, ‘Iweyo usati undimangire nyumba, poti iwe ndiwe munthu wankhondo ndipo udakhetsa magazi.’
4
Komabe Chauta, Mulungu wa Israele, adandisankha ine pakati pa onse a m'banja la kholo langa, kuti ndikhale mfumu ya Israele mpaka muyaya. Pajatu Iyeyo adasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri wa mafuko onse, ndipo ku fuko la Yuda adasankhako banja la bambo wanga. Ndipo pakati pa ana a atate angawo kudakomera Mulungu kuti asankhe ine, kuti ndikhale mfumu ya Aisraele.
5
Choncho mwa ana anga onse, potitu Chauta adandipatsa ana ambiri, Iyeyo wasankha Solomoni, kuti akhale pa mpando waufumu wa Chauta ndi kumalamulira Israele.
6
Adandiwuza kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzamange nyumba yanga ndiponso mabwalo anga. Ndamsankha iyeyo kuti akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala bambo wake.
7
Ufumu wake ndidzaukhazikitsa mpaka muyaya, akalimbikiradi kumvera malamulo ndi malangizo anga, monga momwe akuchitira tsopano.’
8
“Tsono pamaso pa Aisraele onse ndiponso pamaso pa msonkhano umenewu, Mulungu wathu alikumva, ndikukuuzitsani kuti muzisunga ndi kusamala malamulo onse a Chauta Mulungu wanu, kuti mukhalitse m'dziko labwinoli, ndipo lidzakhale nthaŵi zonse choloŵa cha ana anu, inu mutapita.
9
“Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, uzimvera Mulungu wa atate ako, ndipo uzimtumikira ndi mtima wonse, modzipereka kwathunthu. Paja Chauta amasanthula mtima wa munthu aliyense, ndipo amadziŵa maganizo a munthu aliyense. Ukamfunafuna, udzampeza. Koma ukalekana naye, Iyeyo adzakutaya mpaka muyaya.
10
Tsono uganizire bwino zimenezi, pakuti Chauta wakusankha iweyo kuti ummangire nyumba, m'mene Iye azikhalamo ngati mwake. Limba mtima tsono, ndipo uigwire ntchitoyi.”
11
Pambuyo pake Davide adapereka kwa Solomoni mwana wake mapulani a Nyumba ya Chauta, oonetsa khonde lake, zipinda zosungiramo chuma, zipinda zake zam'mwamba, zipinda zake zam'kati, ndiponso malo opepesera machimo.
12
Adaperekanso pulani ya zonse zimene ankaziganizira za mabwalo a Nyumba ya Chauta, ya zipinda zonse zozungulira, ya nyumba zosungiramo chuma cha m'Nyumba ya Chauta, ndiponso ya nyumba yosungiramo mphatso zopatulika.
13
Adafotokoza za magaŵidwe a magulu a ansembe ndi a Alevi, ndiponso magaŵidwe a ntchito zonse za m'Nyumba ya Chauta. Adafotokozanso za ziŵiya zonse zogwira nazo ntchito m'Nyumba ya Chauta.
14
Adalangizanso za kulemera kwa golide wopangira ziŵiya zonse zagolide zofunika, kulemera kwa siliva wopangira ziŵiya zasiliva zonse zofunika,
15
kulemera kwa golide wa zoikapo nyale pamodzi ndi nyale zake, kulemera kwa golide wa choikaponyale chilichonse chagolide pamodzi ndi nyale zake, kulemera kwa siliva wa choikaponyale chasiliva pamodzi ndi nyale zake, potsata ntchito ya choikaponyale chilichonse,
16
kulemera kwa golide wa tebulo lililonse la buledi woperekedwa kwa Chauta, kulemera kwa siliva wa matebulo asiliva,
17
kwa golide weniweni wa mafoloko, mabeseni ndi zikho. Adalangizanso za mbale zagolide ndi zasiliva, pamodzi ndi kulemera kwa mbale iliyonse.
18
Adalangiza za kulemera kwa golide wopangira guwa la zofukiza, ndiponso pulani ya guwalo. Adapereka pulani ya galeta lagolide, ndiye kuti akerubi amene ankatambasula mapiko ao kuphimbira Bokosi lachipangano la Chauta.
19
Davide adati, “Zonse ndalembazi zikugwirizana ndi mau amene adalembedwa potsata malangizo a Chauta mwiniwake, ndipo ndidamvetsa bwino kuti ntchito yonseyo iyenera kuchitika potsata mapulaniwo.”
20
Tsono Davide adauza mwana wake Solomoni kuti, “Khala wamphamvu ndipo uchite zimenezo molimba mtima. Usaope, usataye mtima, pakuti Chauta Mulungu wanga ali nawe. Sadzaleka kukusamala ndipo sadzakusiya pa ntchito zonse za Nyumba ya Chautazi.
21
Magulu a ansembe ndi a Alevi oyenera kugwira ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta ngokonzeka ndithu. Ndipo iwe, pa ntchito yonseyo, udzakhala nawo anthu aluso odzipereka pa ntchito yao. Anthu wamba onse ndi atsogoleri ao omwe uzidzaŵalamulira ndiwe zoti achite.”
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29