bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 23
1 Chronicles 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 24 →
1
Davide atakalamba, masiku ake atatha, adaika Solomoni mwana wake kuti akhale mfumu ya Israele.
2
Davide adasonkhanitsa atsogoleri onse a Israele, ansembe ndi Alevi.
3
Adaŵerenga Aleviwo kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo. Chiŵerengero chao chinali anthu 38,000.
4
Ndipo adati, “Mwa ameneŵa anthu 24,000 adzakhale oyang'anira ntchito za m'Nyumba ya Chauta. Anthu 6,000 adzakhale nduna ndi aweruzi,
5
anthu 4,000 adzakhale alonda apakhomo, ndipo anthu 4,000 enawo azidzatamanda Chauta ndi zipangizo zoimbira zimene ndazipereka kuti zikhale zotamandira Chauta.”
6
Pambuyo pake Davide adaŵagaŵa anthuwo m'magulumagulu kutsata ana aŵa a Levi: Geresomo, Kohati ndi Merari.
7
Ana a Geresomo anali Ladani ndi Simei.
8
Ana a Ladani anali atatu: Yehiyele mtsogoleri, Zetamu ndi Yowele.
9
Ana a Simei anali atatu: Selomoti, Haziyele ndi Harani. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mabanja a makolo a Ladani.
10
Ana a Simei anali Yahati, Ziza, Yeusi ndi Beriya. Anai ameneŵa anali ana a Simei.
11
Yahati anali mtsogoleri, ndipo Ziza anali wachiŵiri wake. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri, nchifukwa chake adaŵaŵerengera ngati makolo a banja limodzi.
12
Ana a Kohati anali anai: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele.
13
Ana a Amuramu anali Aroni ndi Mose. Aaroni adampatula kuti aziyang'anira zinthu zopatulika za Mulungu. Iyeyo ndi ana ake ankapereka nsembe zofukiza pamaso pa Chauta mpaka muyaya, ndipo ankatumikira ndi kudalitsa anthu m'dzina la Chautayo mpaka muyaya.
14
Koma ana a Mose, munthu wa Mulungu uja, adaŵawerengera pamodzi ndi fuko la Levi.
15
Ana a Mose anali Geresomo ndi Eliyezere.
16
Ana a Geresomo mtsogoleri wao anali Sebuele.
17
Eliyezere anali ndi mwana mmodzi yekha dzina lake Rehabiya. Rehabiyayu anali ndi ana ambirimbiri.
18
Mtsogoleri wa ana a Izara anali Selomiti.
19
Ana a Hebroni naŵa: Yeriya mtsogoleri, wachiŵiri Amariya, wachitatu Yahaziele ndipo wachinai anali Yekameamu.
20
Ana a Uziyele naŵa: Mika mtsogoleri, ndipo wachiŵiri anali Isiya.
21
Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Ana a Malai naŵa: Eleazara ndi Kisi.
22
Eleazara adafa opanda ana aamuna, koma aakazi okhaokha. Abale ao, ana a Kisi, ndiwo amene adaŵakwatira.
23
Ana atatu a Musi naŵa: Mali, Edere ndi Yeremoti.
24
Ameneŵa ndiwo amene anali ana a Levi potsata atsogoleri a mabanja a makolo ao, monga m'mene adalembedwera. Ankatsata chiŵerengero cha anthu kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo. Ameneŵa ndiwo amene ankayenera kugwira ntchito yotumikira ku Nyumba ya Chauta.
25
Paja Davide adaati, “Chauta Mulungu wa Israele wapatsa anthu ake mtendere. Ndipo adzakhala ku Yerusalemu mpaka muyaya.
26
Motero nkosafunikiranso kuti Alevi azisenza chihema chija kapena zipangizo za chipembedzo.”
27
Potsata mau omalizira a Davidewo, ameneŵa ndiwo anali chiŵerengero cha Alevi, kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo.
28
“Ntchito yao idzakhala yothandiza ana a Aroni pa ntchito yaunsembe ya ku Nyumba ya Chauta. Azidzasamala mabwalo ndi zipinda, kuyeretsa zonse zimene zili zopatulika, ndiponso azidzagwira ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Chauta.
29
Ali nayonso ntchito yosamalira buledi wopatulika, ufa wa nsembe yaufa, mitanda ya buledi wosatupitsa, nsembe zopereka m'chiwaya, nsembe yosanganiza ndi mafuta. Alinso ndi ntchito yoyesa ndi kupima nsembe zonse zoperekedwa m'Nyumba ya Chauta.
30
M'maŵa mulimonse azithokoza ndi kutamanda Chauta. Aziteronso ndi madzulo omwe.
31
Ndipo azitero nthaŵi zonse akamapereka kwa Chauta nsembe zopsereza za masiku a Sabata, za pokhala mwezi uliwonse, ndiponso za pa chikondwerero china chilichonse chachipembedzo. Ntchito zotumikira Chautazi adzazichita kwamuyaya.
32
Motero azidzayang'anira chihema cha msonkhano ndiponso malo opatulika, ndipo azidzathandiza abale ao, zidzukulu za Aroni, potumikira ku chihema chamsonkhano.”
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29