bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 9
1 Chronicles 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 10 →
1
Tsono Aisraele onse adalembedwa potsata mibadwo yao m'buku la mafumu a Aisraele. Anthu a ku Yuda adaatengedwa ukapolo kunka ku Babiloni chifukwa chakuti anali osakhulupirika.
2
Tsono Aisraele oyamba kukakhala m'maiko mwao ndi m'mizinda yao anali anthu wamba, ansembe, Alevi ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu.
3
Anthu ena a ku Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase amene ankakhala ku Yerusalemu anali motere:
4
A kwa Ayuda anali aŵa: Utai, mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi, mwana wa Yuda.
5
A kwa Asiloni anali aŵa: Asaya mwana wachisamba pamodzi ndi ana ake.
6
A kwa Azera anali aŵa: Yeuwele ndi achibale ao, onse pamodzi 690.
7
A kwa Abenjamini anali aŵa: Salu, mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuwa,
8
Ibineya mwana wa Yerohamu, Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri ndiponso Mesulamu, mwana wa Sefatiya, mwana wa Reuwele, mwana wa Ibineya.
9
Ndipo mabanja ao potsata mibadwo yao analipo 956. Onse amene alembedwa pamwambapaŵa anali atsogoleri a mabanja.
10
Mwa ansembe panali Yedaya, Yehoyaribu, Yakini,
11
ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi, mkulu woyang'anira Nyumba ya Mulungu.
12
Panalinso Adaya, mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasihuri, mwana wa Malikiya, ndiponso Maasai mwana wa Adiyele, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri.
13
Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja analipo 1,760, anthu odziŵa kwambiri ntchito za ku Nyumba ya Chauta.
14
A kwa Alevi naŵa: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa kubanja kwa Merari.
15
Panalinso Bakibakara, Heresi, Galali kudzanso Mataniya, mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu.
16
Panalinso Obadiya, mwana wa Semaya, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni, ndiponso Berekiya, mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi yoyandikana ndi tauni ya Anetofati.
17
Alonda apamakomo naŵa: Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani pamodzi ndi abale ao (Salumu ndiye anali mtsogoleri,)
18
ndipo mpaka nthaŵi imeneyo, anthu a fukoli adaikidwa kuti azilonda pa khomo lakuvuma la Mfumu. Ameneŵa ndiwo amene kale anali alonda apamakomo ku zithando za Alevi.
19
Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja, ankayang'anira ntchito ya utumiki pakhomo pa chihema, monga ankachitira azibambo ao, amene ankayang'anira mudzi wazithando wa Chauta ndi kulonda pa chipata.
20
Finehasi, mwana wa Eleazara ndiye ankaŵalamulira kale. Chauta anali naye!
21
Zekariya mwana wa Meselemiya ankadikira pa khomo la chipata cha chihema chamsonkhano.
22
Onseŵa, amene adasankhidwa kuti akhale alonda apamakomo, analipo 212. Adalembedwa potsata mibadwo yao ku midzi yao. Davide ndi Samuele mneneri ndiwo adaŵaika m'malo ao a ntchito chifukwa cha kukhulupirika kwao.
23
Motero iwowo ndi zidzukulu zao ankayang'anira ndi kumalonda pa makomo a Nyumba ya Chauta, monga ankachitira ku chihema chija.
24
Alondawo anali ku mbali zonse zinai, kuvuma, kuzambwe, kumpoto ndi kumwera.
25
Abale ao amene ankakhala nao m'midzi mwao, ankabwera kamodzikamodzi kudzakhala nao masiku asanu ndi aŵiri,
26
pakuti atsogoleri anai a alonda apamakomo amene anali Alevi, ankayang'anira zipinda ndiponso mosungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta.
27
Usiku ankakhala mozungulira Nyumba ya Chauta, pakuti iwowo ndiwo amene adaasenza udindo waulonda, ndipo anali ndi ntchito yotsekula Nyumbayo m'maŵa mulimonse.
28
Ena mwa Aleviwo ankayang'anira ziŵiya za pa chipembedzo, pakuti kunali kofunika kuziŵerenga pozibweza kapena pozitulutsa.
29
Ena mwa iwowo adasankhidwa kuti aziyang'anira zipangizo ndi ziŵiya zina zopatulika. Ena ankayang'anira ufa wosalala, vinyo, mafuta, lubani ndiponso zonunkhira.
30
Koma ndi ansembe amene ankasanganiza zonunkhirazo,
31
ndipo Matitiya, mmodzi mwa Alevi, mwana wachisamba wa Salumu Mkora, ankayang'anira kaphikidwe ka makeke.
32
Abale ao enanso a kwa Akohati ankayang'anira buledi woperekedwa, kuti azimkonza pasabata paliponse.
33
Alevi ena akuluakulu ankayang'anira oimba nyimbo. Iwowo ankakhala m'zipinda m'Nyumba ya Chauta, osamangika ndi ntchito zina, pakuti ankatumikira usana ndi usiku.
34
Onsewo anali atsogoleri a mabanja a makolo a Alevi potsata mibadwo yao, ndipo ankakhala ku Yerusalemu.
35
Yeiyele amene adaamanga mzinda wa Gibiyoni, ankakhala ku Gibiyoni komweko. Mkazi wake anali Maaka.
36
Mwana wake wachisamba anali Abidoni ndipo pambuyo pa iyeyo panali Zuri, Kisi, Baala, Nere, Nadabu,
37
Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti,
38
bambo wa Simea. Tsono, monga achibale ao aja, iwoŵanso ankakhala ku Yerusalemu pamodzi ndi achibale aowo.
39
Nere adabereka Kisi, Kisi adabereka Saulo, Saulo adabereka Yonatani, Malikisuwa, Abinadabu, ndi Esibaala.
40
Yonatani anabereka Meribaala. Meribaala adabereka Mika.
41
Ana a Mika naŵa: Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi.
42
Ahazi adabereka Yara, Yara adabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimiri. Zimiri adabereka Moza.
43
Moza adabereka Bineya, Bineya adabereka Rafaya, Rafaya adabereka Eleasa, Eleasa adabereka Azele.
44
Azele anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo maina ao naŵa: Azirikamu, Bokeru, Ismaele, Seyariya, Obadiya ndi Hanani. Onseŵa anali ana a Azele.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29