bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 27
1 Chronicles 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 28 →
1
Nawu mndandanda wa atsogoleri a mabanja a Aisraele olamulira ankhondo zikwi ndiponso ankhondo mazana, pamodzi ndi akulu ao amene ankatumikira mfumu. Ankasinthanasinthana mwezi ndi mwezi pa chaka chilichonse, gulu lililonse linali ndi anthu okwanira 24,000.
2
Yosobeamu mwana wa Zabidiele ankayang'anira gulu loyamba pa mwezi woyamba. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
3
Iyeyu anali mdzukulu wa Perezi, ndipo ndiye anali mkulu wa atsogoleri onse ankhondo mwezi woyamba.
4
Dodai Mwahohi anali woyang'anira gulu la mwezi wachiŵiri. Mtsogoleri wa gulu limeneli anali Mikiloti. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
5
Mtsogoleri wa ankhondo pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa Yehoyada mkulu wa ansembe. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
6
Benaya ameneyu ndiye amene ankatsogolera anthu makumi atatu aja. Amizabadi mwana wake ndiye amene ankatsatana naye polamulira gulu lakelo.
7
Asahele, mbale wake wa Yowabu, anali mtsogoleri pa mwezi wachinai, ndipo mwana wake Zebadiya adaloŵa m'malo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
8
Mtsogoleri pa mwezi wachisanu anali Samuti mdzukulu wa Izara. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
9
Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chimodzi anali Ira, mwana wa Ikesi Mtekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
10
Mtsogoleri pa mwezi wa chisanu ndi chiŵiri anali Helezi Mpeloni, mmodzi mwa zidzukulu za Efuremu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
11
Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chitatu anali Sibekai Muhusa, wa m'banja la Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
12
Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chinai anali Abiyezere, mmodzi mwa Aanetoti, Mbenjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
13
Mtsogoleri pa mwezi wachikhumi anali Maharai, wa ku Netofa, wa m'banja la Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
14
Mtsogoleri pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, mmodzi wa fuko la Efuremu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
15
Mtsogoleri pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, mdzukulu wa Otiniyele. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
16
Atsogoleri amene ankayang'anira mafuko a Aisraele anali aŵa: Mtsogoleri wa Arubeni anali Eliyezere, mwana wa Zikiri. Mtsogoleri wa Asimeoni anali Sefatiya, mwana wa Maaka.
17
Mtsogoleri wa Alevi anali Hasabiya, mwana wa Kemuwele. Mtsogoleri wa Aaroni anali Zadoki.
18
Mtsogoleri wa Ayuda anali Elihu, mmodzi mwa abale a Davide. Mtsogoleri wa Aisakara anali Omuri, mwana wa Mikaele.
19
Mtsogoleri wa Azebuloni anali Isimaya, mwana wa Obadiya. Mtsogoleri wa Anafutali anali Yeremoti, mwana wa Aziriele.
20
Mtsogoleri wa Aefuremu anali Hoseya, mwana wa Azaziya. Mtsogoleri wa fuko lahafu la Manase lakuzambwe anali Yowele, mwana wa Pedaya.
21
Mtsogoleri wa fuko lahafu la Manase lakuvuma, dera la Giliyadi anali Ido, mwana wa Zekariya. Mtsogoleri wa Abenjamini anali Yasiyele, mwana wa Abinere.
22
Mtsogoleri wa Adani anali Azarele, mwana wa Yerohamu. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mafuko a Aisraele.
23
Davide sadaŵerengere kumodzi anthu osafika zaka 20 zakubadwa, pakuti Chauta adaalonjeza kuti Aisraele adzachuluka ngati nyenyezi zakumwamba.
24
Yowabu mwana wa Zeruya adayambapo kuŵerenga, koma sadatsirize ai. Mkwiyo wa Chauta udaŵagwera Aisraele chifukwa cha zimenezi, ndipo chiŵerengerocho sadachiloŵetse m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
25
Azimaveti mwana wa Adiyele ankayang'anira chuma cha mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayang'anira chuma cham'miraga, cham'mizinda, cham'midzi ndi cha m'nyumba zankhondo.
26
Eziri mwana wa Kelubi ankayang'anira anthu ogwira ntchito zolima ku minda.
27
Simei wa ku Rama ankayang'anira minda yamphesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayang'anira vinyo kuti asungike bwino mosungira mwake.
28
Baala-Hanani wa ku Gederi anali woyang'anira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ku Sefera. Yowasi ankayang'anira mosungira mafuta.
29
Sitirai wa ku Saroni ankayang'anira ziŵeto za ku busa la ku Saroni. Safati, mwana wa Adilai, ankayang'anira ziŵeto zakuzigwa.
30
Obili Mwismaele ankayang'anira ngamira. Yedeiya Mmeronoti ankayang'anira abulu. Yazizi Muhagiri ankayang'anira nkhosa ndi mbuzi.
31
Onseŵa ndiwo amene anali akulu oyang'anira chuma cha mfumu Davide.
32
Yonatani, mtsibweni wake wa Davide, anali phungu wake, popeza kuti anali munthu womvetsa zinthu, ndiponso wophunzira bwino. Iyeyo pamodzi ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni, ankaphunzitsa ana a mfumu.
33
Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndipo Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu.
34
Ahitofele atamwalira, m'malo mwake mudaloŵa Yehoyada, mwana wa Benaya, ndiponso Abiyatara. Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29