bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 25
1 Chronicles 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 26 →
1
Davide pamodzi ndi akuluakulu osamalira za utumiki adapatulanso anthu ena otumikira mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni amene ankalosa poimba ndi apangwe ndi azeze ndiponso ziwaya zamalipenga. Mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchitoyo ndiponso mndandanda wa ntchito zao nawu:
2
Mwa ana a Asafu panali Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asarela. Amene ankaŵatsogolera ndi Asafu. Ameneŵa ankalalika, mfumu ikaŵalamula kutero
3
Panali ana asanu ndi mmodzi a Yedutuni, maina ao naŵa: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Amene ankaŵatsogolera ndi bambo wao Yedutuni. Iwoŵa ankalalika ndiponso kuimba ndi pangwe pothokoza ndi kutamanda Chauta.
4
Ana a Hemani naŵa: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, Romamiti-Yezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, kudzanso Mahaziyoti.
5
Onseŵa anali ana a Hemani, mneneri wa mfumu, potsata malonjezo a Mulungu akuti adzamkweza iyeyo. Pakuti Mulungu adaampatsa Hemaniyo ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.
6
Iwowo ankaimba potsata malangizo a bambo wao m'Nyumba ya Mulungu. Ankaimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira ku Nyumba ya Mulungu. Asafu, Yedutuni ndi Hemani inkaŵalamulira ndi mfumu imene.
7
Anthu onseŵa anali aluso pa zoimba, achibale ao nawonso adaaphunzira kwambiri kuimbira Chauta. Onse pamodzi analipo 288.
8
Poŵagaŵira ntchito zao ankachitira maere, osasiyanitsa pakati pa ang'onoang'ono ndi akuluakulu, aphunzitsi ndi ophunzira.
9
Maere oyamba adagwera Yosefe, wa banja la Asafu. Achiŵiri adagwera Gedaliya, iyeyo ndi abale ake ndi ana ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
10
Maere achitatu adagwera Zakuri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
11
Maere achinai adagwera Iziri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
12
Maere achisanu adagwera Netaniya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
13
Maere achisanu ndi chimodzi adagwera Bukiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
14
Maere achisanu ndi chiŵiri adagwera Yesarela, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
15
Maere achisanu ndi chitatu adagwera Yesaya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
16
Maere achisanu ndi chinai adagwera Mataniya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
17
Maere akhumi adagwera Simei, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
18
Maere a 11 adagwera Azarele, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
19
Maere a 12 adagwera Hasabiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
20
Maere a 13 adagwera Subaele, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
21
Maere a 14 adagwera Matitiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
22
Maere a 15 adagwera Yeremoti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
23
Maere a 16 adagwera Hananiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
24
Maere a 17 adagwera Yosibekasa, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
25
Maere a 18 adagwera Hanani, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
26
Maere a 19 adagwera Maloti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
27
Maere a 20 adagwera Eliyata, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
28
Maere a 21 adagwera Hotiri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
29
Maere a 22 adagwera Gidaliti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
30
Maere a 23 adagwera Mahaziyoti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
31
Maere a 24 adagwera Romamiti-Yezere, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29