bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 13
1 Chronicles 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 14 →
1
Davide adapempha nzeru kwa atsogoleri a anthu zikwi, kwa atsogoleri a anthu mazana, ndi kwa mtsogoleri wina aliyense.
2
Pambuyo pake adauza msonkhano wonse wa Aisraele kuti, “Ngati zikukukomerani inu, ndipo ngati chimenecho ndiye chifuniro cha Chauta, Mulungu wathu, tiyeni titumize mau kwa abale athu onse amene akukhala m'dziko lonse la Israele ndiponso kwa ansembe ndi kwa Alevi okhala ku mizinda ndi ku miraga yake, kuti anthuwo adzasonkhane pamodzi kwa ife kuno.
3
Tsono tibwere nalonso bokosi lachipangano la Chauta wathu. Paja pa nthaŵi ya Saulo sitidalisamale Bokosilo.”
4
Msonkhano wonse udavomereza zimenezo, poti anthu onse adaaona kuti nzabwino.
5
Choncho Davide adasonkhanitsa Aisraele onse kuyambira ku mtsinje wa Sihori ku Ejipito mpaka ku chipata cha Hamati, kuti abwere nalo Bokosi lachipangano la Mulungu kuchokera ku Kiriyati-Yearimu.
6
Ndipo Davide pamodzi ndi Aisraele onse adakwera kupita ku Baala, ndiye kuti ku Kiriyati-Yearimu m'dera la ku Yuda, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Mulungu. Bokosilo limadziŵika ndi dzina la Chauta amene amakhala pa akerubi ngati pa mpando waufumu.
7
Bokosi lachipanganolo adalinyamula pa ngolo yatsopano, kuchoka nalo ku nyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo ndiwo amene ankayendetsa ngoloyo.
8
Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse anali ankakondwera kwambiri kulemekeza Mulungu poimba nyimbo ndi azeze, apangwe ndi ting'oma, ziwaya zamalipenga ndi malipenga amene.
9
Tsono atafika ku malo ophunthirapo tirigu ku Kidoni, ng'ombe zidaafuna kugwetsa Bokosi lija, ndiye Uza nkutambalitsa dzanja kuti aligwirire Bokosilo.
10
Pomwepo Chauta adampsera mtima Uzayo namkantha chifukwa chakuti adatambalitsa dzanja lake nakhudza Bokosi lija. Adafera pomwepo pamaso pa Chauta.
11
Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza.
12
Davide adachita mantha ndi Mulungu tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndingathe bwanji kufika nalo kwathu Bokosi la Mulunguli?”
13
Motero sadabwere nalo Bokosilo kwao ku mzinda wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti.
14
Choncho Bokosi lachipanganolo lidakhala miyezi itatu kwa Obededomu, m'nyumba mwake. Ndipo Chauta adadalitsa banja la Obededomu pamodzi ndi zonse zimene adaali nazo.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29