bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 16
1 Chronicles 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 17 →
1
Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu.
2
Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu onse m'dzina la Chauta.
3
Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli ya nyama ndiponso keke ya mphesa zouma.
4
Ndipo adaika Alevi ena kuti azitumikira ku Bokosi lachipangano la Chauta, ndiye kuti azipemphera, azithokoza ndi kumatamanda Chauta, Mulungu wa Israele.
5
Asafu ndiye amene anali mtsogoleri, ndipo omthandiza wake anali Zekariya, Yeiyele, Semiramoti, Yehiyele, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obededomu ndi Yeiyele. Ameneŵa ndiwo adasankhindwa kuti akhale oliza azeze ndi apangwe. Asafu ndiye amene anali woliza ziwaya zamalipenga,
6
ndipo Benaya ndi Yehaziele, ansembe, ndiwo amene anali oliza malipenga nthaŵi zonse patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta.
7
Tsiku limenelo ndi limene Davide adayamba kulamula Asafu ndi abale ake kuti akhale oyang'anira nyimbo zothokoza Chauta.
8
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
9
Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
10
Munyadire dzina lake loyera. Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta.
11
Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
12
Muzikumbukira ntchito zodabwitsa za Chauta, zozizwitsa zimene adachita, ndi m'mene ankaweruzira anthu,
13
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake, inu ana a Yakobe, osankhidwa a Chauta.
14
Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu. Amalamulira dziko lonse lapansi.
15
Muzikumbukira chipangano chake nthaŵi zonse, musaiŵale mpaka muyaya mau amene Iye adalamula,
16
Amakumbikira chipangano adachita ndi Abrahamu chija, lonjezo lake limene adachita molumbira kwa Isaki.
17
Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe, kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya.
18
Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani, kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.”
19
Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nao m'dzikomo,
20
ongomayendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina,
21
sadalole ndi mmodzi yemwe aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo.
22
Adati, “Musaŵakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.”
23
Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake.
24
Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
25
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
26
Paja milungu ya anthu a mitundu ina ndi mafano chabe, koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.
27
Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi chimwemwe zili m'Nyumba mwake.
28
Tamandani Chauta, inu anthu a mitundu yonse, vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nza Chauta.
29
Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera.
30
Njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Ndithu dziko lapansi lakhazikika kolimba, osatha kuligwedeza.
31
Zakumwamba zisangalale, za pansi pano zikondwere, zonsezo zilengeze kwa anthu onse kuti, “Chauta ndiye mfumu.”
32
Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo, minda ikondwe pamodzi ndi zonse zomera m'menemo.
33
Mitengo yam'nkhalango idzaimbira Chauta mokondwa, pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.
34
Thokozani Chauta, pakuti ngwabwino, chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.
35
Munenenso kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, mutisonkhanitse ndi kutilanditsa kwa mitundu ina ya anthu, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, ndi kuti tizinyadira pokutamandani.
36
Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, kuyambira muyaya mpaka muyaya!” Tsono anthu onse adati, “Inde momwemo.” Ndipo adatamanda Chauta.
37
Tsono Davide adasiya Asafu pamodzi ndi abale ake kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta, kuti azitumikira nthaŵi zonse ku Bokosilo monga m'mene kunkafunikira tsiku lililonse.
38
Obededomu pamodzi ndi abale ake 68 ankathandizana nawo pa ntchitoyo. Nthaŵi imeneyo Obededomu, mwana wa Yedutuni, ndiponso Hosa, anali ndi udindo wolonda pa makomo.
39
Davide adasiyanso wansembe Zadoki pamodzi ndi abale ake ansembe ku chihema cha Chauta, ku kachisi wa ku Gibiyoni.
40
Adaŵasiya kumeneko kuti azipereka nthaŵi zonse nsembe zopsereza kwa Chauta pa guwa la nsembe zopsereza, m'maŵa ndi madzulo, potsata zonse zimene zidalembedwa m'buku la Malamulo a Mose amene Chauta adalamula Aisraele.
41
Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni, kudzanso onse otsala amene adasankhidwa moŵatchula maina, kuti azithokoza Chauta, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika ndi chamuyaya.
42
Hemani ndi Yedutuni ankayang'anira malipenga ndi ziwaya zamalipenga, ndiponso zipangizo zina zoimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni adaŵaika kuti azilonda pa chipata.
43
Pambuyo pake anthu onse adachoka, aliyense kupita kunyumba kwake. Davide nayenso adapita kwao kuti akadalitse banja lake.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29