bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 6
1 Chronicles 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 7 →
1
Ana a Levi naŵa: Geresomo, Kohati, ndi Merari.
2
Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele.
3
Ana a Amuramu naŵa: Aroni, Mose ndi Miriyamu. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abibu, Eleazara ndi Itamara.
4
Eleazara adabereka Finehasi, Finehasi adabereka Abisuwa,
5
Abisuwa adabereka Buki, Buki adabereka Uzi,
6
Uzi adabereka Zeraya, Zeraya adabereka Meraiyoti,
7
Meraiyoti adabereka Amariya, Amariya adabereka Ahitubi,
8
Ahitubi adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Ahimaazi,
9
Ahimaazi adabereka Azariya, Azariya adabereka Yohanani,
10
Yohanani adabereka Azariya (ndi iyeyu uja ankatumikira za unsembe ku nyumba imene Solomoni adamanga ku Yerusalemu).
11
Azariya adabereka Amariya, Amariya adabereka Ahitubi,
12
Ahitubi adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Salumu,
13
Salumu adabereka Hilikiya, Hilikiya adabereka Azariya,
14
Azariya adabereka Seraya, Seraya adabereka Yehozadaki.
15
Ndipo Yehozadaki adagwidwa ukapolo nthaŵi imene Chauta adalola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu.
16
Ana a Levi naŵa: Geresomo, Kohati ndi Merari.
17
Maina a ana a Geresomo naŵa: Libini ndi Simei.
18
Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele.
19
Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Mabanja a Levi potsata makolo ao ndi ameneŵa.
20
Ana a Geresomo naŵa: Libini, Yahati ndi Zima,
21
Yowa, Ido, Zera, ndi Yeterai.
22
Ana a Kohati naŵa: Aminadabu, Kora, Asiri,
23
Elikana, Ebiyasafa, Asiri,
24
Tahati, Uriyele, Uziya ndi Shaulo.
25
Ana a Elikana naŵa: Amasai, Ahimoti,
26
Elikana, Zofai, Nabati,
27
Eliyabu, Yerohamu ndi Elikana.
28
Ana a Samuele naŵa: Yowele mwana wake wachisamba, Abiya mwana wake wachiŵiri.
29
Ana a Merari naŵa: Mali, Libini, Simei, Uza,
30
Simea, Hagiya ndi Asaya.
31
Panali anthu ena amene Davide adaŵasankhula kuti azitsogolera mwambo wa nyimbo m'Nyumba ya Chauta, ataikamo Bokosi lachipangano.
32
Ankatumikira akuimba nyimbo pakhomo pa malo opatulika a m'chihema chamsonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu. Ndipo ankagwira ntchito yao yotumikirayo potsata malamulo amene adaaŵapatsa.
33
Ameneŵa ndiwo anthu amene ankatumikira pamodzi ndi ana ao aamuna. Pa banja la Kohati panali Hemani, katswiri woimba. Mndandanda wa mibadwo yao unali motere: Hemani anali mwana wa Yowele, mwana wa Samuele.
34
Samuele anali mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa.
35
Towa anali mwana wa Zufu, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai.
36
Amasai anali mwana wa Elikana, mwana wa Yowele, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya.
37
Zefaniya anali mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Abiyasafu, mwana wa Kora.
38
Kora anali mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israele.
39
Panalinso mbale wake Asafu amene ankatsogolera gulu lachiŵiri la oyimba. Asafuyo anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea.
40
Simea anali mwana wa Mikaele, mwana wa Baaseiya, mwana wa Malikiya.
41
Malikiya anali mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya.
42
Adaya anali mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana wa Simei.
43
Simei anali mwana wa Yahati, mwana wa Geresomo, mwana wa Levi.
44
Etani wa fuko la Merari ankatsogolera gulu lachitatu la oimba. Banja lao likuchokera kwa Levi motere: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki.
45
Maluki anali mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya.
46
Hilikiya anali mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semere.
47
Semere anali mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
48
Ndipo abale ao Alevi ndiwo amene adasankhidwa kuti azigwira ntchito zonse za m'chihema cha Mulungu.
49
Koma Aroni pamodzi ndi ana ake ankapereka nsembe pa guwa la nsembe zopsereza, ndi pa guwa lofukizirapo lubani. Iwowo ndiwo ankachita ntchito zonse zoyenera malo opatulika kwambiri, ndi kuchita mwambo wolipirira machimo a Aisraele. Ankachita zimenezi potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu adaŵalamula.
50
Ana a Aroni ndi zidzukulu zake naŵa: Eleazara, Finehasi, Abisuwa,
51
Buki, Uzi, Zerahiya,
52
Meraiyoti, Amariya, Ahitubi,
53
Zadoki ndi Ahimaazi.
54
Naŵa malo ao kumene ankakhala potsata malire a malowo: Zidzukulu za Aroni za m'mabanja a Kohati zidalandira chigawo choyamba,
55
ndiye kuti Hebroni, m'dziko la Yuda pamodzi ndi mabusa omwe.
56
Koma minda ndi miraga ya mzindawo adaipatsa Kalebe mwana wa Yefune.
57
Ana a Aroni adaŵapatsa mizinda iyi: Hebroni, mzinda wopulumukiramo uja, ndiponso Libina pamodzi ndi mabusa ake omwe, Yatiri, Esitemowa pamodzi ndi mabusa ake omwe,
58
Hileni pamodzi ndi mabusa ake omwe, Debiri pamodzi ndi mabusa ake omwe,
59
Asani pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Betesemesi pamodzi ndi mabusa ake omwe.
60
Ndipo kuchotsa ku fuko la Benjamini, adaŵapatsa Geba pamodzi ndi mabusa ake omwe, Alemeti pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Anatoti ndi mabusa ake omwe. Mizinda yao yonse, malinga ndi mabanja ao onse, inalipo khumi ndi itatu.
61
Tsono adachita maele ndipo Akohati otsala adaŵagawira midzi khumi kuchokera pa fuko lahafu la Manase.
62
Ageresomo, potsata mabanja ao, adaŵagawira mizinda khumi ndi itatu kuchokera pa mafuko a Isakara, Asere, Nafutali ndiponso Manase ku Basani.
63
Amerari, potsata mabanja ao, adaŵagawira mizinda khumi ndi iŵiri kuchokera pa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.
64
Umu ndi m'mene Aisraele adapatsira Alevi mizinda ndi mabusa ake omwe.
65
Atachita maele, adaŵapatsanso mizinda ija imene inali ya mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.
66
Mabanja ena a ana a Kohati adalandira mizinda kuchokera pa fuko la Efuremu.
67
Mizindayo inali iyi: Sekemu, mzinda wopulumukiramo uja, pamodzi ndi mabusa ake ku dziko lamapiri la Efuremu, Gezere pamodzi ndi mabusa ake,
68
Yokomeamu pamodzi ndi mabusa ake, Betehoroni pamodzi ndi mabusa ake,
69
Aiyaloni pamodzi ndi mabusa ake, Gatirimoni pamodzi ndi mabusa ake.
70
Koma mizinda yochokera pa fuko la Manase wakuzambwe, Anere pamodzi ndi mabusa ake, ndiponso Bileamu pamodzi ndi mabusa ake, adaipereka kwa otsala a mabanja a Kohati.
71
Mizinda yochokera pa fuko la Manase wakuvuma, imene Ageresomo adalandira, ndi iyi: Golani ku Basani pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Asitaroti pamodzi ndi mabusa ake omwe.
72
Yochokera pa fuko la Isakara ndi iyi: Kedesi pamodzi ndi mabusa ake omwe, Daberati pamodzi ndi mabusa ake omwe,
73
Ramoti pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Anemu ndi mabusa ake omwe.
74
Yochokera pa fuko la Asere ndi iyi: Masala pamodzi ndi mabusa ake omwe, Abidoni pamodzi ndi mabusa ake omwe,
75
Hukoki pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Rehobu pamodzi ndi mabusa ake omwe.
76
Yochokera pa fuko la Nafutali ndi iyi: Kedesi wa ku Galilea pamodzi ndi mabusa ake omwe, Hamoni pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Kiriyataimu: pamodzi ndi mabusa ake omwe.
77
Amerari otsala adalandirako mizinda kuchokera pa fuko la Zebuloni: Rimono pamodzi ndi mabusa ake omwe, Tabori pamodzi ndi mabusa ake omwe,
78
Patsidya pa mtsinje wa Yordani ku Yeriko, kuvuma kwa Yordani, mizinda yochokera pa fuko la Rubeni ndi iyi: Bezere kuchigwa pamodzi ndi mabusa ake omwe, Yaza pamodzi ndi mabusa ake omwe,
79
Kedemoti pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Mefati pamodzi ndi mabusa ake omwe.
80
Yochokera pa fuko la Gadi ndi iyi: Ramoti ku Giliyadi pamodzi ndi mabusa ake omwe, Mahanaimu pamodzi ndi mabusa ake omwe,
81
Hesiboni pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Yazere pamodzi ndi mabusa ake omwe.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29