bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 17
1 Chronicles 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 18 →
1
Davide atayamba kukhazikika m'nyumba yachifumu, tsiku lina adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.”
2
Natani adauza Davide kuti, “Ai, chitani chilichonse chimene mukuganiza mumtima mwanu, poti Mulungu ali nanu.”
3
Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti,
4
“Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Sudzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo.
5
Ine sindidakhalepo m'nyumba chiyambire tsiku limene ndidatsogolera Aisraele mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali m'hema.
6
Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?”
7
“Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, Ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja, kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele.
8
Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzamveketsa dzina lako, kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.
9
Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko, kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija,
10
kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidagonjetsa adani ako onse. Kuonjezera pamenepo, ndikukuuza kuti Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako.
11
Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako kumanda, Ine ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba.
12
Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kuti ukhale wamuyaya.
13
Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo kuti uloŵe ufumu ndiwe.
14
Koma ndidzamkhalitsa mu Nyumba yanga ndi mu ufumu wanga, ndipo ufumu wake udzakhala mpaka muyaya.’ ”
15
Natani adalankhula ndi Davide potsata mau onseŵa, ndiponso potsata zimene adaaziwona m'masomphenyaŵa.
16
Tsono mfumu Davide adaloŵa m'chihema chopembedzeramo Chauta. Adakhala pansi nayamba kupemphera, adati, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nchiyani, kuti Inu mwandifikitsa mpaka pamene ndiliripa?
17
Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Mulungu. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandiwonetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Chauta Mulungu.
18
Ndipo nchiyaninso chimene Davide anganene kwa Inu, popeza kuti mwamchitira ulemu chotere mtumiki wanu? Zoonadi Inu mumamdziŵa mtumiki wanu.
19
Chifukwa chokonda mtumiki wanu, ndiponso malinga ndi mtima wanu, Inu Chauta, mwachita chinthu chachikulu choterechi, pondidziŵitsa zakutsogolozi.
20
Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu Chauta, ndipo palibe mulungu wina koma Inu nokha.
21
Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamene ankafika anthu anu, amene mudaŵaombola ku Ejipito.
22
Inu mudaŵasandutsa anthu anu Aisraele kuti akhale anthu anu mpaka muyaya, ndipo Inu Chauta mudakhala Mulungu wao.
23
“Tsopano Inu Chauta, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa, muchite monga momwe mudaanenera.
24
Choncho dzina lanu lidzakhala lomveka mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israele, ndiyedi Mulungu wao wa Israele!’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya.
25
Inu Mulungu mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pempheroli kwa Inu.
26
Inu Chauta, ndinu Mulungu, ndipo mwalonjeza zinthu zabwino zimenezi kwa mtumiki wanu.
27
Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pajatu zimene Inu Chauta mwazidalitsa, zimakhala zodalitsidwadi mpaka muyaya.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29