bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 4
1 Chronicles 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 5 →
1
Ana a Yuda naŵa: Perezi, Hezironi, Karimi. Huri ndi Sobala.
2
Reaya mwana wa Sobala adabereka Yahati, Yahati adabereka Ahumai ndi Lahadi. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Azorati.
3
Ana a Huri naŵa: Etamu amene adabereka Yezireele, Isima ndi Idibasi, ndiponso mlongo wao Hazeleleponi;
4
Penuwele amene adabereka Gedori ndi Ezere amene adabereka Husa. Ameneŵa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi tate wa Betelehemu.
5
Asuri amene adabereka Tekowa, anali ndi akazi aŵiri, Hela ndi Nara.
6
Nara adamubalira Ahuzamu, Hefere, Temeni, ndi Haahasitari. Ameneŵa ndiwo anali ana a Nara.
7
Ana a Hela naŵa: Zereti, Izara ndi Etinani.
8
Kozi adabereka Anubu, Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele, mwana wa Harumu.
9
Panali munthu wina dzina lake Yabezi amene anthu ankamlemekeza kupambana abale ake. Mai wake pomutcha dzina la Yabezi ankanena kuti, “Chifukwa ndidamubala movutikira.”
10
Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo.
11
Kelubi, mbale wa Suha, adabereka Meiri, Meiri adabereka Esitoni.
12
Esitoni adabereka Beterafa, Paseya ndi Tehina, tate wa Irinahasi. Ameneŵa ndiwo anthu a ku Reka.
13
Ana a Kenazi naŵa: Otiniyele ndi Seraya. Ana a Otiniyele naŵa: Hatati ndi Meonotai.
14
Meonotai adabereka Ofura. Ndipo Seraya adabereka Yowabu, tate wa Ageharasimu. Adaŵatcha choncho popeza kuti anali anthu azaluso.
15
Ana a Kalebe, mwana wa Yefune, naŵa: Iru, Ela, ndi Naamu. Mwana wa Ela anali Kenazi.
16
Ana a Yehalelele naŵa: Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asarele.
17
Ana a Ezara naŵa: Yetere, Meredi, Efere ndi Yaloni. Meredi adakwatira Bitiya, mwana wa Farao. Mkaziyo adatenga pathupi nabala Miriyamu, Samai ndi Isiba, bambo wa Esitemowa.
18
Tsono mkazi wake Wachiyuda adamubalira Yeredi, bambo wa Gedori, Hebere bambo wa Soko, ndiponso Yekutiyele bambo wa Zanowa.
19
Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, ndiwo adabereka Keila Mgarimi ndiponso Esitemowa Mmaakati.
20
Ana a Simoni naŵa: Aminoni, Rina, Benihanani ndi Tiloni. Ana a Isi naŵa: Zoheti, ndi Benizoheti.
21
Ana a Sela, mwana wa Yuda, naŵa: Eri, tate wa Leka, Laada, tate wa Maresa ndi wa mabanja a anthu oomba nsalu zabafuta ku Betasebea.
22
Kunalinso Yokimu, pamodzi ndi amuna a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi amene ankalamula ku Mowabu, koma adabwerera ku Lehemu (tsono nkhani zimenezitu nzakalekale).
23
Ameneŵa anali anthu oumba mbiya ndiponso nzika za ku Netaimu ndi ku Gedera. Adakhala kumeneko pamodzi ndi mfumu, namaigwirira ntchito.
24
Ana a Simeoni naŵa: Nemuwele, Yamini, Yaribu, Zera ndi Shaulo.
25
Salumu anali mwana wake, kudzanso Mibisamu ndi Misima.
26
Ana a Misima naŵa: Hamuele kudzanso Zakuli ndi Simei.
27
Simei anali nawo ana aamuna 16, ndi ana aakazi asanu ndi mmodzi. Koma abale ake analibe ana ambiri, ndipo mabanja ao sadakule kufanana ndi anthu a ku Yuda.
28
Iwowo ankakhala ku Beereseba, Molada, Hazara-Suwala,
29
Biliha, Ezemu, Toladi,
30
Betuele, Horoma, Zikilagi,
31
Betemara-Kaboti, Hazara-Susimu, Betebiri ndiponso ku Saaraimu. Imeneyi inali mizinda yao mpaka nthaŵi imene Davide adayamba kulamulira.
32
Ndipo midzi yao inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, mizinda isanu,
33
pamodzi ndi midzi yao ina yozungulira mizinda imeneyi, mpaka kukafika ku Baala. Kumeneku ndiko kumene ankakhala ndipo ankasunga mndandanda wa maina.
34
Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya,
35
Yowele, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asiyele,
36
Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaiya, Adiyele, Yesimiele, Benaya,
37
Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri ndiponso mwana wa Semaya.
38
Anthu amene tatchulaŵa ndiwo anali atsogoleri a mabanja ao, ndipo mabanja a makolo ao adaonjezeka kwambiri.
39
Motero adapita cha kunja kwa mudzi wa Gedori, kuvuma kwa chigwa, kuti akafunefune busa la ziweto zao.
40
Kumeneko adakapezako busa lokoma ndi la msipu wambiri. Dziko lakenso linali lalikulu, labata ndi laufulu. Anthu amene ankakhala kumeneko kale anali Ahamu.
41
Anthu a fuko a Simeoniwo, ochita kulembedwa maina, adadza pa nthaŵi ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, ndipo adaononga mahema a Ahamuwo ndi kupha Ameuni amene adaŵapeza kumeneko. Adaonongeratu anthu onsewo kotero kuti dzina lao silidamvekenso mpaka lero lino. Kenaka iwowo adakhala ku malo amenewo, popeza kuti kunali msipu womadyetsako ziweto zao.
42
Asimeoni ena okwanira mazana asanu, adapita ku phiri la Seiri. Atsogoleri ao anali Pelatiya, Neyariya, Refaya ndi Uziyele, ana a Isi.
43
Iwowo adaononga Aamaleke otsala amene anali atapulumuka, ndipo adakhala kumeneko mpaka lero lino.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29