bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 19
1 Chronicles 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 20 →
1
Pambuyo pake Nahasi, mfumu ya Aamoni, adamwalira, ndipo Hanuni, mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
2
Tsono Davide adati, “Ine ndidzamchitira zabwino Hanuni mwana wa Nahasi, pakuti inenso bambo wake ankandichitira zabwino.” Choncho Davide adatuma amithenga kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika kwa Hanuni, m'dziko la Aamoni, kuti akampepese.
3
Koma akalonga a Aamoni adauza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide watuma anthu odzakuthuzitsani mtima, ndiye kuti akulemekeza bambo wanu? Osati atumiki akewo abwera kwa inu kuti adzazinde dziko, ndipo kuti akalipenya, alilande?”
4
Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adadula zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao.
5
Tsono Davide adamva za atumiki akewo, adatuma anthu kuti akakumane nawo, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye mudzabwere kuno.”
6
Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, Hanuni ndi Aamoniwo adatumiza siliva wa makilogramu 34,000, kuti akalipirire magaleta ndiponso anthu a pa akavalo a ku Mesopotamiya, a ku Aramaaka ndi a ku Zoba.
7
Adalipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi gulu lake lankhondo. Amenewo adabwera nadzamanga zithando zankhondo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni adabwera kuchokera ku mizinda yao kudzamenya nkhondo.
8
Davide atamva zimenezo, adatuma Yowabu pamodzi ndi gulu lake lonse la ankhondo.
9
Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa chipata cha mzinda. Koma mafumu amene adaadzawo anali paokha ku malo opanda mitengo.
10
Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo.
11
Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni.
12
Tsono Yowabu adauza Abisai kuti, “Ngati Asiriya andipose mphamvu, iwe udzandithandize. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ineyo ndidzabwera kudzakuthandiza.
13
Khala wolimba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”
14
Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriyawo kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika.
15
Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, mbale wa Yowabu, nakaloŵa mu mzinda. Pamenepo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu.
16
Koma Asiriya ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adatuma amithenga kuti abwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate, pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.
17
Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani nkukaŵapeza Asiriyawo. Adandanditsa ankhondo ake kuti amenyane nawo. Tsono pamene Davide ankandanditsa ankhondo ake mopenyana ndi Asiriya, iwoŵa adayamba kumenyana naye.
18
Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo ankhondo a Davide adapha Asiriya okwera magaleta ankhondo okwanira 7,000, ndi ankhondo apansi okwanira 40,000. Adaphanso Sofaki mtsogoleri wa gulu lao lankhondo.
19
Tsono akalonga a Hadadezere ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adapangana za mtendere ndi Davide, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya sadafunenso kumathandiza Aamoniwo.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29