bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Chronicles 29
1 Chronicles 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
1
Pambuyo pake Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Solomoni mwana wangayu, amene Mulungu yekha wamsankha, akali wamng'ono ndi wosadziŵa zambiri, ndipo ntchitoyi njaikulu. Nyumbayi sidzakhala ya munthu koma ya Chauta.
2
Choncho ndidapereka za ku Nyumba ya Chauta wanga monga m'mene ndidathera, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuŵa wopangira zinthu zamkuŵa, chitsulo chopangira zinthu zazitsulo ndi mitengo yopangira zinthu zamtengo. Ndidaperekanso miyala yochuluka yomangira, ya mtundu wa onikisi, miyala ya maŵangamaŵanga, miyala yambiri yamitundumitundu yamtengowapatali ndiponso miyala ya marabulo.
3
Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga.
4
Ndikupereka matani a golide 100, golide wake wabwino kwambiri wa ku Ofiri, ndi matani a siliva wosalala 240. Zonsezo zidzakhala zokutira makoma a Nyumba,
5
ndiponso zogwiritsira ntchito zonse zochitika ndi anthu aluso, golide wopangira zinthu zagolide ndiponso siliva wopangira zinthu zasiliva. Tsono pakati pa inuyonso ndani amene atapeko mwaufulu zinthu zake ndi kuzipereka kwa Chauta?”
6
Pomwepo atsogoleri a mabanja a makolo adapereka zopereka zao mwaufulu, monga momwe adachitiranso atsogoleri a mafuko, atsogoleri a magulu a anthu zikwi, atsogoleri a magulu a anthu mazana ndiponso akapitao a ntchito za mfumu.
7
Zimene adapereka ku ntchito ya Nyumba ya Chauta ndi izi: matani 170 a golide, makilogramu 84 a ndalama zagolide za mtundu wina, matani 340 a siliva, matani pafupifupi 620 a mkuŵa, ndipo matani oposa 3,400 a chitsulo.
8
Aliyense amene anali nayo miyala ya mtengo wapatali, ankaipereka ku nyumba zosungiramo chuma cha Chauta. Amene ankasamala zimenezo anali Yehiyele Mgeresoni.
9
Tsono anthu adakondwa chifukwa chakuti akulu aowo ankapereka mwaufulu ndiponso ndi mtima wao wonse. Nayenso mfumu Davide adakondwa kwambiri.
10
Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu.
11
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
12
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
13
Tsopano tikukuthokozani, Inu Mulungu wathu, ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.
14
“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndi ayani kuti tingathe kupereka mwaufulu motere? Paja zinthu zonse zimachokera kwa Inu ndipo zimene tikupereka kwa Inu nzanu zomwe.
15
Inu Chauta, mukudziŵa kuti ife ndife alendo chabe pansi pano. Tili ngati anthu ongokhala nao chabe, monga momwe analiri makolo athu. Masiku athu okhala pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi chabe ndipo palibe poti tingakhulupirire.
16
Inu Chauta, Mulungu wathu, inde tapereka mphatso zimenezi kuti akumangireni nyumba, koma zonsezi zikuchokera m'manja mwanu ndipo nzanu zomwe.
17
Mulungu wanga, ndikudziŵa kuti Inu mumapenyetsetsa mtima, ndipo mumakondwera ndi anthu achilungamo. Ndapereka mwaufulu zinthu zonse ndi mtima wolungama, ndipo tsopano ndaŵaona anthu anu amene ali panoŵa nawonso akupereka mwaufulu ndi mokondwa kwa Inu.
18
Inu Chauta, Mulungu wa makolo athu aja, Abrahamu, Isaki ndi Israele, limbitsani nthaŵi zonse maganizo ndi makhalidwe ameneŵa mwa anthu anu, ndipo akhale ndi mtima wokhulupirika mpaka kwa Inu muyaya.
19
Mwana wanga Solomoni mumpatse mtima wangwiro, kuti azisunga malamulo ndi malangizo anu ndi kuŵatsata bwino ndithu, ndiponso kuti amange nyumba imene ine ndaipezera zofunika zonsezi.”
20
Tsono Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Tamandani Chauta, Mulungu wanu.” Apo anthu onsewo adatamanda Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaŵeramitsa mitu yao napembedza Chauta, ndipo adalambira mfumu.
21
M'maŵa mwake anthuwo adapereka kwa Chauta, nsembe zopsereza izi: ng'ombe 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ndiponso anaankhosa 1,000, pamodzi ndi chopereka cha chakumwa, kudzanso nsembe zina zochuluka zoperekera Aisraele onse.
22
Tsiku limenelo adadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Solomoni, mwana wa Davide, anthu adamlonga ufumu kachiŵiri. Adamdzoza pamaso pa Chauta kuti akhale mfumu, ndipo Zadokinso kuti akhale wansembe.
23
Tsono Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Chauta nakhala mfumu m'malo mwa Davide atate ake. Zinthu zinkamuyendera bwino, ndipo Aisraele onse ankamumvera.
24
Atsogoleri onse, ankhondo ndi ana a mfumu Davide omwe, onsewo adadzipereka kwa mfumu Solomoni.
25
Aisraele onse adaona m'mene Chauta adakwezera Solomoni. Adampatsadi ukulu wa ufumu wakuti mfumu ina iliyonse sidaulandirepo m'dziko la Israele, iyeyo asanaloŵe.
26
Umu ndimo m'mene Davide, mwana wa Yese, adalamulira Aisraele onse.
27
Nthaŵi imene Davide adalamulira Aisraele idakwanira zaka 40. Adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri ku Hebroni, ndipo ku Yerusalemu adalamulirako zaka 33.
28
Tsono adamwalira atafika pokalamba zedi. Masiku ake adachuluka, pamodzi ndi chuma ndi ulemerero wake. Ndipo Solomoni, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
29
Tsono ntchito za mfumu Davide kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza pake, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Samuele, m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la mbiri ya mneneri Gadi.
30
M'menemo adasimba za kulamulira kwake, za mphamvu zake ndiponso za zonse zimene zidamuwonekera iyeyo, mpakanso zimene zidaonekera fuko la Israele ndiponso zimene zidaonekera maiko ena ozungulira.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29